Akukonza Nyumba ya Ufumu ku Switzerland
Zitsanzo za Ulaliki
NSANJA YA OLONDA
Mawu Oyamba: M’buku la Chivumbulutso muli ulosi wonena za anthu 4 okwera pamahatchi. Ena amachita mantha akamva ulosiwu pomwe ena amachita nawo chidwi kwambiri.
Lemba: Chiv. 1:3
Perekani Magaziniyo: Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza mmene ulosi wonena za anthu okwera pa mahatchiwa ulili wosangalatsa kwa tonsefe.
KUPHUNZITSA CHOONADI
Funso: Kodi mukuganiza kuti n’zotheka anthufe kudziwa zinthu zam’tsogolo?
Lemba: Yes. 46:10
Zoona Zake: Mulungu amatiululira zinthu zam’tsogolo pogwiritsa ntchito Mawu ake, Baibulo.
BANJA LANU LIKHOZA KUKHALA LOSANGALALA
Mawu Oyamba: Ndikufuna kukuonetsani kavidiyo kachidule ka nkhani yokhudza banja. [Onetsani vidiyo yothandiza pogawira kabuku kakuti Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala.]
Perekani Kabuku: Ndingathe kukupatsani kabuku kamene katchulidwa muvidiyoyi ngati mungakonde kapena ndingakusonyezeni mmene mungakapangire dawunilodi pawebusaiti.
LEMBANI ULALIKI WANUWANU
Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.