Akulalikira kunyumba ndi nyumba ku Italy
Zitsanzo za Ulaliki
NSANJA YA OLONDA
Funso: Kodi Mulungu potilenga anafuna kuti tizifa?
Lemba: Chiv. 21:4
Perekani Magaziniyo: Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya moyo ndi imfa.
KUPHUNZITSA CHOONADI
Funso: Kodi n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri chonchi?
Lemba: 1 Yoh. 5:19
Zoona Zake: Satana Mdyerekezi ndi amene akulamulira dzikoli.
KODI PHUNZIRO LA BAIBULO LIMACHITIKA BWANJI?
Munganene Kuti: A Mboni za Yehova amaphunzitsa anthu Baibulo kwaulere ndipo amawathandiza kupeza mayankho a mafunso ngati awa: N’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri chonchi? Kodi ndingatani kuti banja langa lizisangalala? Kavidiyo aka kakusonyeza mmene phunziro la Baibulo limachitikira. [Onetsani vidiyo yakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji?] Tikhoza kumaphunzira nanu Baibulo pogwiritsa ntchito kabuku aka. [Muonetseni limodzi mwa mabuku ophunzirira Baibulo, ndipo ngati n’kotheka, musonyezeni mmene timaphunzirira.]
LEMBANI ULALIKI WANUWANU
Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.