Akugawira kabuku ka Banja Losangalala ku Georgia
Zitsanzo za Ulaliki
NSANJA YA OLONDA
Funso: Kodi ndi ndani amene amapereka mphatso zabwino kwambiri kuposa aliyense?
Lemba: Yak. 1:17
Perekani Magaziniyo: Nsanja ya Olonda iyi ili ndi mfundo zimene zingatithandize kuti tiziyamikira mphatso yabwino kwambiri imene Mulungu anatipatsa.
KUPHUNZITSA CHOONADI
BANJA LANU LIKHOZA KUKHALA LOSANGALALA
Mawu Oyamba: Tikuonetsa anthu kavidiyo aka konena za banja. [Onetsani vidiyo yothandiza pogawira kabuku kakuti Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala.]
Perekani Kabuku: Ndingathe kukupatsani kabuku kamene katchulidwa muvidiyoyi ngati mungakonde kapena ndingakusonyezeni mmene mungapangire dawunilodi pawebusaiti yathu.
LEMBANI ULALIKI WANUWANU
Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.