Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp17 No. 3 tsamba 16
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi zidzatheka kuti padzikoli pakhaledi chilungamo?
  • Kodi Yehova amakonda kwambiri mtundu wina wa anthu kuposa wina?
  • Yehova—Gwero la Chilungamo Chenicheni
    Nsanja ya Olonda—1998
  • “Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”
    Yandikirani Yehova
  • Kodi Zinthu Zopanda Chilungamo Zidzatha Padzikoli?
    Nkhani Zina
  • Chilungamo Posachedwapa Kaamba ka Mitundu Yonse
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
wp17 No. 3 tsamba 16
Anthu a mitundu yosiyanasiyana

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi zidzatheka kuti padzikoli pakhaledi chilungamo?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

Zimene Baibulo limanena

“Ndikudziwa bwino kwambiri kuti Yehova adzazengera mlandu anthu osautsika. Iye adzachitira chilungamo anthu osauka.” (Salimo 140:12) Ufumu wa Mulungu udzabweretsa chilungamo padzikoli.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Mulungu amaona zinthu zopanda chilungamo zimene zikuchitika padzikoli, ndipo adzazithetsa.​—Mlaliki 5:8.

  • Chilungamo chochokera kwa Mulungu chidzachititsa kuti anthu padzikoli azikhala mwamtendere komanso motetezeka.​—Yesaya 32:16-18.

Kodi Yehova amakonda kwambiri mtundu wina wa anthu kuposa wina?

Anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu anadalitsa kapena kutemberera mtundu winawake wa anthu, pomwe ena amakhulupirira kuti Mulungu sakondera mtundu uliwonse wa anthu. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Zimene Baibulo limanena

“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Mulungu amaona kuti anthu onse ndi ofanana.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • M’Baibulo muli “uthenga wabwino” wopita “kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse.”​—Chivumbulutso 14:6.

Kuti mudziwe nthawi imene padziko lonse padzakhale chilungamo, werengani mutu 3 m’buku ili, Zimene Baibulo Limaphunzitsa lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pawebusaiti ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena