Zida zonse zankhondo zidzawonongedwa
Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Kodi padzikoli padzakhaladi mtendere?
Kodi mungayankhe bwanji?
Inde
Ayi
Mwina
Zimene Baibulo limanena
Yesu Khristu akadzayamba kulamulira padzikoli, “padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo.” Izi zikutanthauza kuti mtenderewo udzakhalapo mpaka kalekale.—Salimo 72:7.
Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo
Anthu onse oipa adzawonongedwa. Zimenezi zidzachititsa kuti anthu abwino ‘adzasangalale ndi mtendere wochuluka.’—Salimo 37:10, 11.
Mulungu adzathetsa nkhondo padziko lonse.—Salimo 46:8, 9.
Kodi n’zotheka panopa kukhala ndi mtendere wamumtima?
Anthu ena amakhulupirira kuti . . . n’zosatheka kukhala ndi mtendere wamumtima panopa chifukwa padzikoli pali mavuto ambiri komanso pakuchitika zinthu zopanda chilungamo. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
Zimene Baibulo limanena
Ngakhale panopa, anthu amene ali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu akhoza kukhala ndi “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”—Afilipi 4:6, 7.
Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo
Mulungu akulonjeza kuti adzathetsa mavuto onse komanso zinthu zopanda chilungamo, ndipo ‘adzapanga zinthu zonse kukhala zatsopano.’—Chivumbulutso 21:4, 5.
Tikhoza kukhala ndi mtendere wamumtima ngati timayesetsa kupeza ‘zosowa zathu zauzimu.’—Mateyu 5:3.