Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w17 June tsamba 21
  • “Udalitsike Chifukwa cha Kulingalira Bwino Kwako”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Udalitsike Chifukwa cha Kulingalira Bwino Kwako”
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Abigayeli ndi Davide
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Anachita Zinthu Mwanzeru
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Anachita Zinthu Mwanzeru
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Mkazi Wanzeru Apeŵa Tsoka
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
w17 June tsamba 21
Abigayeli

“Udalitsike Chifukwa cha Kulingalira Bwino Kwako”

MAWU ali pamwambawa anawalankhula ndi Davide pamene ankayamikira mzimayi wina dzina lake Abigayeli. Kodi n’chifukwa chiyani Davide anamuyamikira, nanga tingaphunzire chiyani pa zimene Abigayeli anachita?

Davide anakumana ndi mzimayiyu pa nthawi imene ankathawa Mfumu Sauli. Abigayeli anakwatiwa ndi munthu wachuma kwambiri dzina lake Nabala yemwe anali ndi nkhosa zambiri ndipo ankakhala kudera lamapiri kum’mwera kwa Yuda. Davide ndi amuna amene anali nawo “anali ngati khoma” loteteza abusa ndi nkhosa za Nabala. Kenako Davide anatuma amuna ena kwa Nabala kuti akapemphe kachakudya ‘kalikonse kamene dzanja lake lingapeze.’ (1 Sam. 25:8, 15, 16) Tikaganizira zimene Davide ndi anzake anachita, sitinganene kuti analakwitsa popempha zimenezi.

Koma Nabala anachita zinthu mogwirizana ndi dzina lake lomwe limatanthauza “Wopanda nzeru” kapena “Wopusa.” Iye anawayankha mwamwano ndipo anakana kupereka chakudyacho. Zitatero, Davide anakonzeka kuti akaphe Nabala ndi banja lake lonse chifukwa cha kupusa kwakeko.​—1 Sam. 25:2-13, 21, 22.

Abigayeli atazindikira kuti zimene mwamuna wakeyo anachita ziwabweretsera mavuto, anachita zinthu molimba mtima. Iye anapita kwa Davide mwaulemu n’kumudandaulira kuti aganizire mmene nkhaniyi ingakhudzire ubwenzi wake ndi Yehova. Abigayeli anapereka chakudya chambiri kwa Davide ndi anthu ake. Davide anazindikira kuti Yehova ndi amene anatuma Abigayeli kuti amuletse kupalamula mlandu wopha anthu. Iye anauza Abigayeli kuti: “Udalitsike chifukwa cha kulingalira bwino kwako. Udalitsike chifukwa cha kundigwira lero kuti ndisapalamule mlandu wamagazi.”​—1 Sam. 25:18, 19, 23-35.

Malinga ndi nkhaniyi, tiyenera kupewa kukhala ndi mtima wosayamika ngati wa Nabala. Taphunziranso kuti tikaona kuti vuto linalake likhoza kuchitika tiyenera kuchita zinthu mwanzeru kuti vutolo lisachitike. Mofanana ndi munthu wina amene analemba masalimo, tiyenera kupempha Mulungu kuti ‘atiphunzitse kulingalira bwino ndi kudziwa zinthu.’​—Sal. 119:66.

Tikatero, ena akhoza kuona kuti ndife anzeru. Kaya alankhula kapena ayi, mumtima mwawo akhoza kumva ngati Davide amene ananena kuti: “Udalitsike chifukwa cha kulingalira bwino kwako.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena