Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp18 No. 1 tsamba 8-9
  • 1 Lingakuthandizeni Kupewa Mavuto

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1 Lingakuthandizeni Kupewa Mavuto
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)——2018
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KUMWA KWAMBIRI MOWA
  • CHIWEREWERE
  • Kodi Kukopana Kuli Ndi Vuto?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Nkulakwa Kuseŵera Kokopana Pakati pa Mwamuna ndi Mkazi?
    Galamukani!—1998
  • Kodi Kutyasira Kuli Nchivulazo Chotani?
    Galamukani!—1991
  • Kodi Ndingapeŵe Motani Kupweteka kwa Kutyasira?
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)——2018
wp18 No. 1 tsamba 8-9
Mzimayi akumwa mowa kwambiri, ndipo kenako akuphunzira mfundo za m’Baibulo

1 Lingakuthandizeni Kupewa Mavuto

Baibulo limati amene analemba malangizo amene ali m’bukuli anauziridwa ndi Mulungu ndipo malangizowa ndi “opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu.” (2 Timoteyo 3:16) Kodi zimenezi ndi zoona? Tiyeni tione mmene Baibulo lathandizira anthu kuti apewe mavuto aakulu kwambiri.

KUMWA KWAMBIRI MOWA

Delphine, amene tamutchula munkhani yapita ija, anayamba kumwa mowa kwambiri chifukwa choti ankakhala ndi nkhawa. Baibulo sililetsa kumwa mowa pang’ono koma limati: “Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri.” (Miyambo 23:20) Kumwa mowa kwambiri kumabweretsa mavuto monga kudwala, kutha kwa banja komanso kusagwirizana ndi ena. Kumachititsanso kuti anthu ambiri azifa chaka chilichonse. Komatu munthu angapewe mavutowa ngati atamatsatira mfundo za m’Baibulo.

Zimenezi ndi zimene Delphine anachita. Iye anati: “Ndinazindikira kuti mowa sungandithandize kuthetsa mavuto anga. Choncho ndinatsatira malangizo a pa Afilipi 4:6, 7 amene amati: ‘Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma . . . zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.’ Usiku uliwonse ndikayamba kukhala ndi nkhawa ndinkapempha Yehova kuti andithandize. Ndinkamufotokozera zimene zikundidetsa nkhawa komanso zomwe zandikhumudwitsa kapena kundipsetsa mtima. Ndipo ndinkamuchonderera kuti andithandize kuti ndisamangoganizira za mavuto anga. M’mawa ndinkaonetsetsa kuti ndisadzuke ndidakali okhumudwa kapena wokwiya. Kupemphera kunkandithandiza kuti ndiziganizira kwambiri za zinthu zomwe ndili nazo osati zomwe ndilibe. Kenako ndinaganiza zosiya kumwa mowa. Ndinkaona kuti mtendere wamumtima womwe ndinali nawo ndi wamtengo wapatali ndipo sindinkafuna kuutaya.”

CHIWEREWERE

Chiwerewere ndi limodzi mwa makhalidwe amene amabweretsa mavuto ambiri. Koma mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kudziwa zinthu zina zimene zimachititsa kuti munthu achite chiwerewere. Zinthu zake ndi monga kukopana kosayenera komanso kuonera zolaula. Mnyamata wina dzina lake Samuel anati: “Zinali zosavuta kukopa ena. Nthawi zina ndikazindikira kuti mtsikana winawake akundifuna, zinkangondisangalatsa ndikamachita zinthu zomukopa, ngakhale zitakhala kuti ineyo sindikumufuna.” Samuel anazindikira kuti, ngakhale pamene iyeyo analibe maganizo okopa munthu wina, nthawi zambiri anthu ankamudandaula kuti akukopa atsikana. Izi zinachititsa kuti ayambe kuchitira dala khalidweli. Koma kenako anaona kuti sankachita bwino. Iye anati: “Khalidweli si labwino chifukwa limachititsa kuti uzichita zinthu zongokusangalatsa iweyo popanda kuganizira mmene zingakhudzire winayo.”

Samuel anawerenga nkhani ya achinyamata pa webusaiti ya jw.org. Kenako anaganizira mfundo ya palemba la Miyambo 20:11, lomwe limati: “Ngakhale mnyamata amadziwika ndi ntchito zake, ngati zochita zake zili zoyera ndiponso zowongoka.” Kodi lembali linamuthandiza bwanji? Samuel anazindikira kuti kukopa ena sikoyera komanso si kwabwino. Iye anati: “Ndinazindikiranso kuti wachinyamata amene amakopa ena amazolowera makhalidwe amene angadzapangitse kuti banja lake lisamayende bwino. Ndinayamba kuganizira kuti, kodi ndikadzakwatira mkazi wanga adzamva bwanji ngati ataona kuti ndimakopana ndi mkazi wina? Zimenezi zinandipangitsa kuzindikira kuti zimene ndinkachitazo ndi zolakwika. Ngakhale kuti n’zophweka kuyamba kukopana ndi wina, komabe si zinthu zoyenera.” Panopa Samuel anasiya khalidweli. Kupewa kukopana ndi anthu ena kunamuthandiza kuti apewe kuchita chiwerewere.

Nayenso Antonio ankachita khalidwe loipa lomwe likanamupangitsa kuti achite chiwerewere. Iye ankakonda kuonera zolaula. Ngakhale kuti Antonio ankamukonda kwambiri mkazi wake, ankakanika kusiyiratu khalidweli. Koma kuganizira mfundo ya palemba la 1 Petulo 5:8 kunamuthandiza kwambiri. Lembali limati: “Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” Antonio ananena kuti: “Masiku ano zithunzi zolaula zili ponseponse, ndipo munthu akaona zithunzizi zimavuta kuti zichoke m’maganizo mwake. Vesi limeneli linandithandiza kuzindikira kuti mayesero amenewa amachokera kwa Satana. Ndinkafunika kumadzikumbutsa kuti Satana ndi amene amafuna kuti tizionera zolaula. Ndikudziwa kuti ndi Yehova amene angandithandize kukhala ‘woganiza bwino ndiponso kukhala maso’ n’cholinga choti ndizitha kulimbana ndi mayesero amene angawononge maganizo anga, mtima wanga ndiponso banja langa.” Antonio analandira thandizo loyenerera ndipo panopa anasiyiratu khalidwe loonera zolaula. Zimenezi zinamuthandiza kuti apewe mavuto ena aakulu.

Zimene takambiranazi zikusonyeza kuti m’Baibulo muli malangizo amene angatithandize kupewa mavuto aakulu. Nanga bwanji mavuto amene anayamba kale ndipo akuoneka ngati sangathe? Munkhani yotsatira tiona mmene Mawu a Mulungu angatithandizire pothana ndi mavuto ngati amenewa.

Malangizo a m’Baibulo angatithandize kupewa mavuto

Mzimayi akumwa zakumwa zina osati mowa
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena