Mawu Oyamba
KODI MULUNGU ZIMAM’KHUDZA MUKAMAVUTIKA?
Pakachitika ngozi komanso anthu akamavutika ndiponso kufa, ambiri amafunsa kuti, ‘Kodi Mulungu amaona zimene zikuchitikazi?’ Baibulo limanena kuti:
“Pakuti maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo, koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”—1 Petulo 3:12.
Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza mmene Mulungu amatithandizira komanso zimene akuchita kuti athetse mavuto onse.