MBIRI YA MOYO WANGA
Zinthu Zonse N’zotheka ndi Yehova
Tsiku lina mkazi wanga ali m’basi anamva mayi wina akuuza munthu kuti: “Imfa sidzakhalaponso ndipo akufa adzaukitsidwa.” Mkazi wangayo ankafunitsitsa kumva zambiri moti atangotsika m’basiyo anathamangira mayiyo. Mayiyo anali Apun Mambetsadykova ndipo anali wa Mboni za Yehova. Pa nthawiyo, kulankhula ndi a Mboni kunali koopsa koma zimene Apun anatiphunzitsa zinatithandiza kuti tisinthe kwambiri moyo wathu.
TINKAYAMBA NTCHITO DZUWA LISANATULUKE N’KUWERUKA LITALOWA
Ndinabadwa mu 1937 kufamu inayake pafupi ndi ku Tokmok m’dziko la Kyrgyzstan. Banja lathu linali lamtundu wa Kiegizi ndipo tinkalankhula Chikiegizi. Makolo anga ankagwira ntchito kufamu ndipo ankayamba dzuwa lisanatuluke n’kuweruka litalowa. Anthu ogwira ntchito kumafamu ankangopatsidwa chakudya ndipo ankapatsidwa ndalama kamodzi kokha pachaka. Zinali zovuta kuti mayi anga atisamalire bwinobwino ine ndi mchemwali wanga. Choncho ndinangolekeza sitandade 5, n’kuyamba ntchito pafamuyo.
Mapiri a Teskey Ala-Too
Tinkakhala m’dera losauka ndipo tinkayenera kugwira ntchito yakalavulagaga kuti tipeze zofunika pa moyo. Ndili mnyamata sindinkaganizira n’komwe za tsogolo langa kapena cholinga cha moyo. Ndipo sindinkalota n’komwe kuti kuphunzira mfundo zosangalatsa zokhudza Yehova Mulungu kungasinthe moyo wanga. Koma choonadi chinafika ku Kyrgyzstan m’njira yochititsa chidwi kwambiri. Chinayambira m’dera la kwathu komwe ndi kumpoto kwa dzikoli.
ANTHU AMENE ANATHAMANGITSIDWA ANABWERETSA CHOONADI
Anthu a ku Kyrgyzstan anayamba kuphunzira za Yehova m’ma 1950. Koma zinali zovuta chifukwa choti dzikoli linali la chikomyunizimu. Zinali choncho chifukwa chakuti dzikoli linali pansi pa ulamuliro wa USSR. M’madera onse a ulamuliro umenewu, a Mboni za Yehova sankachita nawo zandale. (Yoh. 18:36) Choncho anthu ankawaona ngati oukira boma ndipo ankawazunza. Koma palibe chilichonse chimene chingalepheretse Mawu a Mulungu kufika m’mitima ya anthu abwino. Mfundo yofunika kwambiri imene ndaiphunzira pa moyo wanga ndi yakuti “zinthu zonse n’zotheka” ndi Yehova.—Maliko 10:27.
Emil Yantzen
Kuzunzidwa kwa Mboni za Yehova kunathandiza kuti anthu ambiri aphunzire choonadi ku Kyrgyzstan. Zili choncho chifukwa chakuti anthu amene ankaonedwa kuti ndi oukira boma ankawathamangitsira kudera lotchedwa Siberia. Milandu ya anthu amenewa itatha, ambiri anabwera kudzakhala ku Kyrgyzstan ndipo ena anabweretsa choonadi. Wina mwa anthu amenewa anali Emil Yantzen, yemwe anabadwira ku Kyrgyzstan mu 1919. Iye atamangidwa anakumana ndi a Mboni za Yehova kundende. Emil anakhala wa Mboni ndipo anabwerera kwawo mu 1956. Anafikira ku Sokuluk pafupi ndi kwathu. Kumeneku n’kumene kunakhazikitsidwa mpingo woyamba m’dzikoli mu 1958.
Victor Vinter
Patangopita chaka chimodzi, m’bale wina dzina lake Victor Vinter anasamukira ku Sokuluk. M’baleyu anali wokhulupirika kwambiri koma anazunzidwa koopsa. Anamangidwa kwa zaka zitatu maulendo awiri chifukwa chosachita nawo zandale, kenako anakhala kundende zaka zinanso 10 komanso anathamangitsidwa m’dzikoli n’kukakhala kwina kwa zaka 5. Koma mavuto ngati amenewa sanalepheretse anthu kuphunzira choonadi m’dzikoli.
CHOONADI CHINAFIKA M’DERA LATHU
Eduard Varter
Pofika mu 1963, ku Kyrgyzstan kunali a Mboni pafupifupi 160 ndipo ambiri anali ochokera ku Germany, ku Ukraine ndi ku Russia. Wina mwa a Mboniwa anali M’bale Eduard Varter amene anabatizidwa ku Germany mu 1924. Cha m’ma 1940, a chipani cha Nazi anamumanga ndipo patapita zaka zina, boma la USSR linamuthamangitsa kwawo. Mu 1961, m’baleyu anasamukira ku Kant, yomwe ndi tauni yapafupi ndi kwathu.
Elizabeth Fot; Aksamai Sultanalieva
Mlongo wina wokhulupirika dzina lake Elizabeth Fot ankakhalanso ku Kant. Mlongoyu ankagwira ntchito yosoka ndipo anali waluso kwambiri. Anthu monga madokotala ndi aphunzitsi ankakonda kugula zovala zimene ankasoka. Mayi wina amene ankakonda kukagula zovala kwa mlongoyu anali Aksamai Sultanalieva. Mayiyu anali mkazi wa munthu wina amene anali ndi udindo kukhoti. Mayiyu atakumana ndi Elizabeth anamufunsa mafunso ambiri okhudza cholinga cha moyo komanso zimene zimachitika munthu akamwalira. Elizabeth anayankha mafunso onse pogwiritsa ntchito Baibulo. Aksamai anakhala wa Mboni ndipo ankalalikira uthenga wabwino mwakhama kwambiri.
Nikolai Chimpoesh
Pa nthawi imeneyi, M’bale Nikolai Chimpoesh, yemwe anachokera ku Moldova, anaikidwa kukhala woyang’anira dera ndipo anagwira ntchito imeneyi kwa zaka pafupifupi 30. Nikolai ankayendera mipingo komanso kuyang’anira ntchito yokopera mabuku n’kumawatumiza m’mipingo. Akuluakulu a boma anatulukira zimene m’baleyu ankachita. Tsiku lina, Eduard Varter anapereka malangizo othandiza kwa m’baleyu. Anamuuza kuti: “Apolisi akakufunsani muzingoyankha mosapita m’mbali kuti mabuku athu amachokera kulikulu lathu ku Brooklyn. Muziwayang’ana m’maso ndipo musamaope chilichonse.”—Mat. 10:19.
Pasanapite nthawi yaitali, Nikolai anaitanidwa kulikulu la apolisi ku Kant. Pofotokoza zimene zinachitika kumeneko, iye anati: “Wapolisi wina anandifunsa kumene timatenga mabuku athu. Ndiye ndinamuyankha kuti amachokera ku Brooklyn. Nditayankha choncho anasowa chonena. Kenako anandiuza kuti ndizipita ndipo sanandiitanenso.” Abale opanda mantha ngati amenewa anapitiriza kulalikira mosamala m’dera lathu lonse la kumpoto kwa Kyrgyzstan. Ndiyeno mu 1980 m’pamene uthenga wabwino wonena za Yehova unafika m’banja lathu ndipo mkazi wanga ndi amene anayamba kuumva.
MKAZI WANGA SANACHEDWE KUZINDIKIRA CHOONADI
Mkazi wanga dzina lake ndi Mairambubu ndipo kwawo ndi kudera la Naryn. Tsiku lina mu August 1974, iye anapita kukacheza kwa mchemwali wanga ndipo limeneli linali tsiku loyamba kukumana ndi ineyo. Ndinamukonda pompopompo moti tinakwatirana tsiku lomwelo.
Apun Mambetsadykova
Mu January 1981, mkazi wanga akupita kumsika pa basi anamva mlongo wina akukambirana ndi munthu ndipo zimene zinachitika n’zimene ndafotokoza kumayambiriro kuja. Mkazi wanga ankafuna kuphunzira zambiri choncho anafunsa dzina la mlongoyo komanso kumene ankakhala. Mlongoyo anamuuza kuti dzina lake ndi Apun koma ankachita zinthu mosamala kwambiri chifukwa choti m’zaka za m’ma 1980 ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa. Choncho m’malo monena kumene amakhala, anafunsa kumene ifeyo timakhala. Mkazi wanga anabwerera kunyumba ali wosangalala kwambiri.
Atangofika anati: “Lero ndamva zinthu zosangalatsa kwambiri. Mayi wina wandiuza kuti posachedwapa imfa idzatha. Akuti nyama zakutchire sizidzakhalanso zoopsa.” Kwa ine zinali ngati nthano chabe moti ndinamuuza kuti: “Tiye tingomudikira. Akabwera adzafotokoze bwinobwino.”
Patapita miyezi itatu, Apun anafika kunyumba kwathu. Kenako alongo ena anapitiriza kubwera ndipo ena mwa iwo anali amtundu wa Kiegizi oyamba kuphunzira choonadi. Alongo amenewa anatithandiza kudziwa mfundo zoona zokhudza Yehova komanso cholinga chake. Ankatiwerengera buku lakuti Kucokera ku Paradaiso Wotayika Kunka ku Paradaiso Wopezekanso.a Popeza bukuli linalipo limodzi lokha ku Tokmok, tinalikopera pamanja.
Mfundo ina imene tinaiphunzira koyambirira ndi ya pa Genesis 3:15. Tinaphunzira kuti Mulungu adzakwaniritsa ulosiwu pogwiritsa ntchito Yesu yemwe ndi Mesiya komanso Mfumu. Umenewu ndi uthenga wofunika kwambiri umene anthu onse ayenera kuumva. Tinazindikira kuti nafenso tiyenera kuthandiza anthu kuti amve uthengawu. (Mat. 24:14) Pasanapite nthawi yaitali, mfundo za m’Baibulo zinayamba kusintha moyo wathu.
KUSONKHANA KOMANSO KUBATIZIDWA PA NTHAWI YA BANI
Tsiku lina, m’bale wina wa ku Tokmok anatiitana ku ukwati. Ine ndi mkazi wanga tinaona kuti a Mboni amachita zinthu mosiyana ndi anthu ena. Pa phwandolo panalibe mowa ndipo zonse zinkachitika mwadongosolo kwambiri. Zinali zosiyana kwambiri ndi maukwati ena amene tinkapita m’mbuyomo. M’maukwati enawo anthu ankaledzera, kutukwana komanso kuchita zinthu zina zoipa.
Nthawi zina tinkasonkhana ndi mpingo wa ku Tokmok. Nyengo ikakhala bwino misonkhanoyi tinkachitira kunkhalango. Abale ndi alongo ankadziwa kuti apolisi akutilondalonda choncho ankapempha m’bale wina kuti azilondera. M’nyengo yozizira tinkasonkhana m’nyumba. Maulendo angapo apolisi anatipeza n’kufunsa zimene tikuchita. Ine ndi mkazi wanga tinabatizidwa mu July 1982 mumtsinje wa Chüy. Pa tsikuli tinafunika kuchita zinthu mosamala kwambiri. (Mat. 10:16) Abale ankafika mwapang’onopang’ono ndipo tinasonkhana kunkhalango. Tinaimba nyimbo yaufumu kenako n’kumvetsera nkhani yaubatizo.
TINAPATSIDWA MWAYI WOCHITA ZAMBIRI MU UTUMIKI
Mu 1987, m’bale wina anandipempha kuti ndikaone munthu wina wachidwi kutauni ya Balykchy. Kuti tikafike kutauniyi tinayenda pa sitima maola 4. Titapita kumeneku maulendo angapo tinaona kuti kuli anthu ambiri ofuna kuphunzira. Apa tinazindikira kuti tili ndi mwayi wochita zambiri mu utumiki.
Ine ndi mkazi wanga tinkakonda kupita ku Balykchy kumapeto kwa mlungu ndipo tinkalowa mu utumiki komanso kuchita misonkhano. Anthu ambiri anayamba kufuna mabuku athu. Ndiye tinkanyamula mabuku ku Tokmok pogwiritsa ntchito matumba onyamulira mbatata. Mwezi uliwonse, pankafunika matumba osachepera pa awiri kuti akwanire anthu onse. Tinkalalikiranso musitima popita ku Balykchy komanso pobwera.
Mu 1995, kutauniyi kunakhazikitsidwa mpingo ndipo apa n’kuti patadutsa zaka 8 kuchokera pamene tinafikako koyamba. Maulendo opita kutauniyi ankafuna ndalama zambiri koma ife tinalibe. Mwamwayi, m’bale wina ankatipatsa ndalama kuti tiziwonjezera pa thiransipoti yathu. Apa tingati Yehova anaona kuti tikufuna kuchita zambiri mu utumiki ndipo ‘anatitsegulira zipata za kumwamba.’ (Mal. 3:10) Zonsezi ndi umboni wakuti chilichonse n’chotheka ndi Yehova.
TINKATANGANIDWA NDI KUSAMALIRA BANJA LATHU KOMANSO UTUMIKI
Mu 1992, ndinaikidwa kukhala mkulu ndipo ndinali mkulu woyamba wamtundu wa Kiegizi m’dzikoli. Mwayi wina wa utumiki unatsegukanso ku Tokmok. Tinkaphunzira Baibulo ndi achinyamata ambiri amtundu wa Kiegizi a m’makoleji. Mmodzi mwa achiyamatawa ali mu Komiti ya Nthambi ndipo awiri akuchita upainiya wapadera. Tinkayesetsanso kuthandiza anthu mumpingo. Cha m’ma 1990, mabuku athu anali m’chilankhulo cha Chirasha ndipo misonkhano inkachitikanso m’Chirasha. Koma anthu olankhula Chikiegizi ankawonjezereka kwambiri. Choncho ineyo ndinkamasulira nkhani m’chilankhulochi kuti nawonso azipindula.
Ndili ndi mkazi wanga komanso ana athu 8 mu 1989
Ine ndi mkazi wanga tinkachitanso khama posamalira ana athu. Tinkawatenga kumisonkhano komanso pokalalikira. Mwana wathu wina wamkazi dzina lake Gulsayra, yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 12, ankakonda kulankhula ndi anthu odutsa pamsewu n’kumawauza mfundo za m’Baibulo. Ana athu ankakonda kuloweza malemba. Ankakondanso kuchita zambiri mumpingo ndipo atakhala ndi ana awo anawathandizanso kuti azichita zomwezo. Panopa tatsala ndi ana 9 ndi zidzukulu 11 ndipo 16 mwa iwo akutumikira Yehova kapena kupita kumisonkhano limodzi ndi makolo awo.
ZINTHU ZINASINTHA KWAMBIRI
Abale amene anafika ndi choonadi m’dera lathu m’ma 1950 akhoza kudabwa kwambiri ndi mmene zinthu zinasinthira. Mwachitsanzo, kuyambira m’ma 1990, takhala ndi ufulu wolalikira komanso kuchita misonkhano ikuluikulu.
Ndili ndi mkazi wanga mu utumiki
Mu 1991, ine ndi mkazi wanga tinapita kumsonkhano wachigawo m’dziko la Kazakhstan womwe unachitikira ku Alma-Ata komwe panopa kumatchedwa ku Almaty. Aka kanali koyamba kupezeka pa msonkhano waukulu. Mu 1993, msonkhano wachigawo woyamba ku Kyrgyzstan unachitikira musitediyamu ya Spartak mumzinda wa Bishkek. Abale ndi alongo anagwira ntchito yoyeretsa sitediyamuyi kwa mlungu wathunthu. Izi zinasangalatsa kwambiri mkulu woyang’anira malowo moti anatiuza kuti tichite msonkhano pasitediyamuyo popanda kulipira chilichonse.
Mu 1994 panachitikanso chinthu china chosangalatsa kwambiri chifukwa buku loyamba kupezeka m’Chikiegizi linatulutsidwa. Panopa, mabuku akumasuliridwa m’chilankhulochi ku ofesi ya nthambi mumzinda wa Bishkek. Mu 1998, boma linavomereza ntchito ya gulu lathu m’dziko la Kyrgyzstan. Panopa gulu lakula kwambiri ndipo m’dzikoli muli ofalitsa oposa 5,000. Tili ndi mipingo 83 ndi magulu 25 a Chitchainizi, Chingelezi, Chikiegizi, Chirasha, Chinenero Chamanja cha ku Russia, Chitekishi, Chiuyiguri ndi Chiuzibeki. Abale ndi alongo a mitundu yosiyanasiyana amenewa amatumikira Yehova mogwirizana. Yehova ndi amene akuthandiza kuti zonsezi zitheke.
Yehova wandithandizanso kusintha kwambiri moyo wanga. Ndinabadwira m’banja losauka ndipo ndinangolekeza sitandade 5. Koma Yehova wandilola kukhala mkulu komanso kuphunzitsa mfundo zamtengo wapatali za m’Baibulo kwa anthu ophunzira kuposa ineyo. Kunena zoona Yehova amachita zodabwitsa. Zimene zandichitikira pa moyo wanga zimandilimbikitsa kuuza ena za Yehova komanso kuti ndi iye “zinthu zonse n’zotheka.”—Mat. 19:26.
a Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma pano linasiya kusindikizidwa.