Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb17 tsamba 26-29
  • Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
  • Nkhani Yofanana
  • Mwambo Wopereka Nthambi
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova 2014
  • Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
  • Zinthu Zonse N’zotheka ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Kodi Kuofesi ya Mboni za Yehova Kumachitika Zotani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
yb17 tsamba 26-29
M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yotsegulira ofesi ya nthambi ya ku Kyrgyzstan

Kyrgyzstan

ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi

ABALE ndi alongo a m’dziko la Kyrgyzstan komanso ochokera m’mayiko ena anagwira ntchito mwakhama kwa chaka ndi hafu pokonza komanso kuwonjezera ofesi ya nthambi yomwe ili mumzinda wa Bishkek. Mwambo wotsegulira nthambiyi unachitika pa 24 October, 2015, patangotha mwezi umodzi ntchitoyi itatha. Pulogalamuyi inalumikizidwanso m’Nyumba za Ufumu 18 komanso m’malo ena ndipo anthu 3,000 amene anasonkhana m’malowa anamvera mwambowo. M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Muzitumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu.” Tsiku lotsatira, kunachitika msonkhano wolimbikitsa ndipo abale ndi alongo ambiri a m’dzikoli anamvetsera msonkhanowu.

Ofesi ya nthambi ya ku Kyrgyzstan

Nthambi ya ku Kyrgyzstan

Loweruka pa 14 May, 2016, anthu okwana 6,435 anafika pamwambo wotsegulira nthambi ya ku Armenia. Ofesi ya nthambiyi ndi nsanjika 6 zomwe zili m’chinyumba cha nsanjika 18. Mwambowu unalinso wotsegulira Nyumba ya Msonkhano komanso nyumba zomwe ndi Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Nkhani zomwe zinakambidwa pamwambowu zinafotokoza chiyambi cha a Mboni za Yehova ku Armenia. A Mboni oyambirira anali anthu a ku Armenia amene ankakhala ku United States chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900. Kenako choonadi chinafika m’dziko la Armenia cha m’ma 1970 dzikoli lidakali pansi pa ulamuliro wa Soviet Union. Chaposachedwapa a Mboni za Yehova analembetsa kuboma n’kukhala chipembedzo chovomerezeka ndipo kenako m’dzikoli munakhazikitsidwa ofesi ya nthambi. Anthu ambiri omwe anafika pamwambowu analipo pa nthawi imene choonadi chinafika m’dzikoli. Pa nthawi imeneyo iwo sankaganiza kuti m’dzikoli mungadzachitike zinthu zapadera ngati zimenezi. Mwambowu unafika pachimake pamene anthu onse omwe analipo anagwirizana ndi zimene M’bale David Splane, wa m’Bungwe Lolamulira, ananena kuti nthambiyo akuipereka kwa Yehova.

M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yotsegulira ofesi ya nthambi ya ku Armenia; anthu ali pamsonkhano womwe unachitika kumapeto kwa mlunguwo; Anthu akuvina gule wachikhalidwe wa ku Armenian

Armenia

Pamwamba: Mwambo wotsegulira ofesi ya nthambi

Pakati: Abale ndi alongo ali pamsonkhano womwe unachitika kumapeto kwa mlunguwo

Pansi: Abale ndi alongo akuvina gule wachikhalidwe chawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena