Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp19 No. 2 tsamba 12-13
  • Ngati Mukuona Kuti Bola Kungofa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ngati Mukuona Kuti Bola Kungofa
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI N’CHIYANI CHINGAKUTHANDIZENI?
  • KODI PALI NJIRA YOTHETSERATU VUTOLI?
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ife Tonse Tiyenera Kutamanda Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kodi Matenda Ovutika Maganizo Ndi Otani?
    Galamukani!—2009
  • Kupambana Nkhondo Yolimbana ndi Kuchita Tondovi
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Mulungu wa Chitonthozo Chonse” Amathandiza
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
wp19 No. 2 tsamba 12-13
Mzimayi akuwerenga Baibulo n’kumaganizira zimene akuwerengazo

Ngati Mukuona Kuti Bola Kungofa

Adriana, yemwe amakhala ku Brazil, anati: “Nthawi zonse ndinkangoganiza kuti sindingathenso kupirira moti ndinayamba kuona kuti bola kungofa.”

KODI inunso nthawi zina mumaona kuti zingakhale bwino mutangofa? Ngati ndi choncho, ndiye kuti mungamvetse mmene Adriana ankamvera. Iye ankada nkhawa kwambiri moti ankangokhala wokhumudwa ndipo ankaona kuti zinthu sizidzakhalanso bwino. Adriana anamupeza ndi matenda ovutika maganizo.

Taganiziraninso za bambo wina wa ku Japan dzina lake Kaoru. Bamboyu ankasamalira makolo ake okalamba omwe ankadwala. Iye anati: “Pa nthawi imeneyi ndinkakumananso ndi mavuto aakulu kuntchito. Zimenezi zinachititsa kuti ndisamafunenso kudya komanso ndizivutika kugona. Ndinkaona kuti zingakhale bwino nditangofa.”

Bambo wina wa ku Nigeria dzina lake Ojebode anati: “Nthawi zambiri ndinkakhala wokhumudwa ndipo pena ndinkalira, moti ndinayamba kuganiza zongodzipha.” Ubwino wake ndi wakuti a Ojebode, a Kaoru komanso Adriana sanadziphe. Koma chaka chilichonse anthu ambirimbiri amadzipha.

KODI N’CHIYANI CHINGAKUTHANDIZENI?

Ambiri mwa anthu amene amadzipha ndi amuna, ndipo ambiri mwa amenewa amakhala kuti ankachita manyazi kupempha thandizo. Komatu Yesu anena kuti anthu odwala amafunika dokotala. (Luka 5:31) Choncho ngati mukuvutika maganizo, musamachite manyazi kupempha thandizo. Anthu ambiri amene ali ndi vutoli aona kuti zinthu zimasintha akalandira thandizo lakuchipatala. A Ojebode, a Kaoru komanso Adriana analandira thandizo ndipo panopa zinthu ziliko bwino.

Madokotala angakupatseni mankhwala kapena malangizo, kapenanso angagwiritse ntchito njira ziwiri zonsezi pokuthandizani. Anthu amene akuvutika maganizo amafunika kuwalezera mtima. Zimakhalanso bwino ngati achibale komanso anzawo akuwathandiza pa vuto lawoli. Bwenzi labwino kwambiri ndi Yehova ndipo kudzera m’Mawu ake, Baibulo, amathandiza anthu amene akuvutika maganizo.

KODI PALI NJIRA YOTHETSERATU VUTOLI?

Nthawi zambiri anthu amene akuvutika maganizo amafunika kulandira thandizo kwa nthawi yaitali komanso kusintha zina ndi zina pa moyo wawo. Ngati mukuvutika maganizo mungakhale ndi chiyembekezo ngati chimene a Ojebode ali nacho, choti m’tsogolomu zinthu zidzakhala bwino. Iwo anati: “Ndimayembekezera nthawi imene lemba la Yesaya 33:24 lidzakwaniritsidwe. Lembali limanena za nthawi yomwe palibe munthu amene adzanene kuti, ‘Ndikudwala.’” Mofanana ndi a Ojebode, inunso muziyembekezera lonjezo la Mulungu la “dziko lapansi latsopano” limene simudzakhala ‘zopweteka.’ (Chivumbulutso 21:1, 4) Pokwaniritsa lonjezoli Mulungu adzathetsanso kuvutika maganizo. Pa nthawiyo simuzidzadanso nkhawa. Zinthu zonse zimene zikukudetsani nkhawa panopa, “sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.”​—Yesaya 65:17.

Mavesi Amene Angakuthandizeni

Mulungu amadziwa mmene mukumvera.

“Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja . . . ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’”—Yesaya 41:13.

Yehova amadziwa mmene tikumvera kuposa aliyense ndipo amafunitsitsa kutithandiza.

Muziganizira zitsanzo za m’Baibulo.

“[Eliya] anayamba kupempha kuti afe, ponena kuti: ‘ . . . chotsani moyo wanga Yehova.’”​—1 Mafumu 19:4.

A Ojebode ananena kuti: “Kuganizira zitsanzo za m’Mawu a Mulungu kunandithandiza. Ndinazindikira kuti pa nthawi ina mneneri Eliya ankamva ngati mmene inenso ndinkamvera.”

Muziphunzira kuchokera pa zitsanzo za m’Baibulo.

“Ine [Yesu] ndakupempherera iwe [Petulo] kuti chikhulupiriro chako chisathe.”​—Luka 22:32.

Petulo atakana Yesu katatu, anapwetekedwa mtima kwambiri moti anayamba kulira. A Kaoru ananena kuti: “Zimene zinachitikira Petulo zinandithandiza kuona kuti Yehova ndi Yesu ankamvetsa mmene Petulo ankamvera. Zimenezi zinandilimbikitsa kwambiri.”

Zinthu zonse zimene zikukudetsani nkhawa panopa “sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.”—Yesaya 65:17

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena