Kodi Nchifukwa Ninji Ife Tonse Tiyenera Kutamanda Mulungu?
HALELUYA! Liwu limenelo opita kutchalitchi ambiri amalidziŵa bwino kwambiri m’Dziko Lachikristu. Ena a iwo amalitchula mofuula m’mapemphero awo pa Sande. Koma kodi ndi angati amene amalidziŵadi tanthauzo lake? Limenelo kwenikweni ndi liwu lachihebri lotanthauza “Tamandani Ya!” Ndi mfuu yamphamvu yachisangalalo yotamanda Mlengi, amene dzina lake ndi Yehova.a
Liwulo lakuti “Haleluya” limapezeka kambiri m’Baibulo. Chifukwa ninji? Chifukwa pali zifukwa zambiri zotamandira Mulungu. Ya (Yehova) ndiye Mlengi ndi Mchirikizi wa chilengedwe chonsecho. (Salmo 147:4, 5; 148:3-6) Anapanga zinthu za padziko lapansi zimene zimatheketsa moyo. (Salmo 147:8, 9; 148:7-10) Ndipo amakonda anthu kwambiri. Tikachita chifuniro chake, amatidalitsa ndi kutichirikiza pa moyo uno ndi kutipatsa chiyembekezo chotsimikizika cha moyo ukudzawo wabwino koposa. (Salmo 148:11-14) Ya (Yehova) ndiye anauzira mawu awa akuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
Chifukwa chake, chilangizo chikuperekedwa kwa onse chakuti: “Haleluya”! [“Tamandani Ya, anthu inu!” NW]. (Salmo 104:35) Komabe, nzachisoni kuti si onse amene akufuna kulabadira. Lerolino, anthu akuvutika. Ambiri nganjala, ngodwala, kapena otsenderezeka. Ambiri ali ndi chisoni chochuluka chifukwa chogwiritsira ntchito molakwa anamgoneka kapena kumwetsa moŵa kapena chifukwa cha chisembwere chawo kapena kupanduka. Kodi pali zifukwa zimene anthu oterewo angatamandire Mulungu?
‘Yehova Yekha Ndiye Anandipatsa Chiyembekezo’
Inde, zilipo. Yehova akupempha aliyense kuti amdziŵe, kuphunzira kuchita chifuniro chake, ndi kupeza madalitso amene amasonkhezera anthu kumtamanda. Ndipo ambiri amalabadira. Mwachitsanzo, Adriana wa ku Guatemala. Pamene Adriana anali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri, amake anamwalira. Posapita nthaŵi, atate wake anachoka panyumba. Atafitsa zaka khumi, iye anayamba kugwira ntchito kuti azipeza zofunika. Popeza kuti amake anamuuza kuti azitumikira Mulungu ndi tchalitchi, Adriana anagwirizana ndi magulu osiyanasiyana achikatolika, koma pamene anafitsa zaka 12, anakhumudwa nadziphatika pa gulu la m’khwalala. Anayamba kusuta, kumwa anamgoneka, ndi kuba. Kodi mtsikana wamng’ono ngati ameneyo angafunirenji kutamanda Mulungu?
Mbale wake wa Adriana anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, koma Adriana amamseka. Ndiyeno amayi ake aang’ono anamwalira. Pamaliro a amakewo, Adriana anavutika kwambiri ndi mafunso osautsa. Kodi amakewo anapita kuti? Kodi anali kumwamba? Kodi anapita kuhelo wamoto? Zinamsokoneza kwambiri, ndipo Adriana anapita kukachisi wakumanda kukapempherera thandizo, ndipo anagwiritsira ntchito dzina la Mulungu, Yehova, limene mbale wake anamphunzitsa.
Posapita nthaŵi, anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndi kumapezeka pamisonkhano yawo yachikristu. Zimenezi zinamchititsa kuona moyo mwanjira yatsopano, ndipo molimba mtima anasiya kuyanjana ndi magulu a m’khwalala. Adriana, wazaka za m’ma 20 tsopano, akuti: “Chikondi cha Yehova chokha ndicho chinandisiyitsa moyo woipa umenewo. Yehova yekha mwa chifundo chake chachikulu anandipatsa chiyembekezo cha moyo wosatha.” Ngakhale kuti makulidwe ake a Adriana anali ovuta, iye ali nazo zifukwa zabwino koposa zotamandira Mulungu.
Ku Ukraine kukuchokera lipoti losimba za mkhalidwe wina wokayikitsa kwambiri. Mwamuna wina ali khale m’ndende kuyembekeza kunyongedwa. Kodi akudzimvera chifundo? Ngwatondovi kodi? Kutalitali. Pokhala Mboni za Yehova zinamfikira posachedwa ndipo anapezako chidziŵitso cha Yehova, anawapempha kukaonana ndi amake. Tsopano akuwalembera kalata chifukwa wamva kuti iwo anachita zimene anawapempha. Iye akuti: “Zikomo poonana ndi amayi. Nkhani imeneyi inandisangalatsa kuposa zonse zomwe ndinalandira chaka chatha.”
Ponena za iye mwini ndi akaidi anzake amene wawalalikira, akulemba kuti: “Tsopano tili ndi chikhulupiriro mwa Mulungu ndipo tikuyesa kuchita mogwirizana ndi chikhulupiriro chathu.” Akumaliza kalata yake motere: “Zikomo potithandiza kuchidziŵa chikondi ndi kupeza chikhulupiriro. Ndikakhalabe ndi moyo, ndidzakuthandizani inunso. Yamikani Mulungu pokhala muli amoyo ndi kuti mukuthandiza ena kukonda Mulungu ndi kumkhulupirira.” Mwamuna ameneyu wachita apilo chilango chake cha imfa. Koma kapena adzanyongedwa kapena adzakhala zaka zambiri m’ndende, ali nachodi chifukwa chotamandira Mulungu.
‘Ngakhale Ndine Wakhungu, Ndikupenya’
Tsopano, talingalirani za mtsikana wathanzi amene mwadzidzidzi waleka kupenya. Zimenezo zinamchitikira Gloria, amene amakhala ku Argentina. Gloria anakhala wakhungu mwadzidzidzi pamene anali ndi zaka 19, ndipo sanathenso kupenya. Pausinkhu wa zaka 29 anayamba kukhala ndi mwamuna yemwe sanali mwamuna wake ndipo posapita nthaŵi anakhala ndi pathupi. Tsopano anaganiza kuti moyo wake unali ndi tanthauzo. Koma pamene anafedwa mwanayo, anakhala ndi mafunso. Anaphanaphana ndi mtima kuti, ‘Nchifukwa ninji zimenezi zikundichitikira? Kodi ndinalakwanji? Mwati Mulungu aliko?’
Panthaŵiyi, Mboni ziŵiri za Yehova zinafika pakhomo pake. Anayamba kuphunzira Baibulo nadziŵa lonjezo lake lakuti m’dziko latsopano, akhungu adzapenyanso. (Yesaya 35:5) Kwa Gloria chiyembekezo chimenecho chinali chabwino kwambiri! Anakondwera kwambiri, makamaka pamene mwamuna wake anavomereza kuti alembetse ukwati wawo. Ndiyeno mwamuna wake anapezeka m’ngozi nakhala wolemala, wongokhala mu mpando wamagudumu. Lero mkazi wakhungu ameneyu amagwiritsa ntchito kuti apeze zofunika. Ndiponso, amachita ntchito yonse panyumba, ndi kusamaliranso mwamuna wake pa zofuna zake. Komabe Gloria amatamanda Yehova! Mothandizidwa ndi abale ake ndi alongo achikristu, iye amaphunzira Baibulo la akhungu, ndipo misonkhano yachikristu ku Nyumba ya Ufumu imamlimbikitsa kwambiri. Iye akuti: “Nzovuta kufotokoza, koma ngakhale ndine wakhungu, zili monga kuti ndikupenya.”
Nthaŵi zina anthu amazunzidwa pamene atamanda Mulungu. Mkazi wina ku Croatia anakondwera pamene anaphunzira za Mulungu, koma mwamuna wake anatsutsa chikhulupiriro chake chatsopano namkana, natenga mwana wawo wamkazi wachaka chimodzi. Pokhala m’khwalala, mwamuna wake ndi banja atamsiya, ali wopanda nyumba, ntchito, ndi mwana wake yemwe, poyamba anataya mtima. Koma kukonda kwake Mulungu kunamlimbikitsa, ngakhale kuti kambiri sanali kuonana ndi mwana wake wamkaziyo kufikira atakula. Mkaziyu anapeza ‘ngale ya mtengo wapatali’ ndipo sanafune kuitaya. (Mateyu 13:45, 46) Kodi anachisunga motani chimwemwe chake panthaŵi yovuta imeneyi? Iye akuti: “Chimwemwe ndi chipatso cha mzimu wa Mulungu. Chingakulitsidwe popanda mikhalidwe yakunja, monga momwe maluŵa amamerera mu greenhouse kaya machedwe akhale otani kunjaku.”
Ku Finland, Markus wazaka zisanu ndi chimodzi anampeza ndi matenda osachira a m’minofu. Posapita nthaŵi anayamba kumakhala pa mpando wamagudumu. Patapita zaka zingapo, amayi ake anampereka kwa wa tchalitchi cha Pentecostal amene anali kutchuka chifukwa chonena kuti akhoza kuchiritsa anthu odwala. Koma sanamchiritse ndi chozizwitsa. Chotero Markus sanafunenso kumva za Mulungu ndipo analondola maphunziro a sayansi ndi ntchito zina zakudziko. Ndiyeno zaka ngati zisanu zapitazo, mkazi wina wokhala mu mpando wamagudumu pamodzi ndi mnyamata wina anafika panyumba yomwe Markus anali kukhala. Iwo anali Mboni za Yehova. Markus tsopano anali wokana Mulungu, koma sanakane kuti akambitsirane za chipembedzo ndipo anawauza kuti aloŵe.
Pambuyo pake, banja lina linamchezera, ndipo phunziro la Baibulo linayambika. M’kupita kwa nthaŵi, mphamvu ya choonadi cha Baibulo inasintha mmene Markus amaonera zinthu, ndipo anazindikira kuti ngakhale anali wopunduka, anali nazodi zifukwa zotamandira Mulungu. Anati: “Ndine wokondwera kwambiri popeza choonadi ndi gulu limene Yehova akuligwiritsira ntchito. Moyo wanga tsopano walongosoka ndipo uli ndi tanthauzo. Nkhosa inanso yosokera yapezeka ndipo siikufuna kuchoka pagulu la nkhosa za Yehova!”—Yerekezerani ndi Mateyu 10:6.
Onse ‘Atamande Ya’
Izizi zangokhala chabe zina za zokumana nazo zosaŵerengeka zimene zingasimbidwe kusonyeza kuti anthu lerolino, kaya mikhalidwe yawo ikhale yotani, angakhale nacho chifukwa chotamandira Mulungu. Mtumwi Paulo anachifotokoza motere: “Chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.” (1 Timoteo 4:8) Tikachita chifuniro cha Mulungu, iye adzakwaniritsa “lonjezano la ku moyo uno.” Ayi, iye m’dongosolo ili la zinthu sadzalemeza osauka kapena kuchiritsa odwala. Koma amapereka mzimu wake kwa awo omwe akumtumikira kuti apeze chimwemwe ndi chikhutiro kaya mikhalidwe yawo yakunja ikhale yotani. Inde, ngakhale mu “moyo uno,” odwala, otsenderezeka, ndi osauka angakhale nacho chifukwa chotamandira Mulungu.
Koma bwanji za “moyo ulinkudza”? Eya, kulingalira za uwo chabe kuyenera kutipangitsa kutamanda Mulungu ndi changu chachikulu koposa! Timasangalala tikaganiza za nthaŵi pamene umphaŵi sudzadziŵika; pamene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala”; ndi pamene Yehova Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” (Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:3, 4; Salmo 72:16) Kodi mukuwaona motani malonjezo ameneŵa a Mulungu?
Mnyamata wina ku El Salvador analandira trakiti la Baibulo lomwe linafotokoza zina za zinthu zimenezi. Iyeyo anati kwa Mboni yomwe inampatsa trakitilo, “Inu Mayi, zimene trakitili likunena zanyanya kukoma, sizingakhale zoona ayi.” Ambiri amatero. Komabe, ameneŵa ndiwo malonjezo ake a Iye amene analenga thambo, amene anayambitsa kayendedwe ka zinthu zachibadwa padziko lathu lapansi pano, amenenso amathandiza osauka ndi odwala kuti apeze chimwemwe. Tiyenera kukhulupirira zimene amanena. Mnyamata wotchulidwayu anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova napeza kuti zimenezi nzoona. Ngati simunayambebe kuchita zimenezi, tikukulimbikitsani kuchita chimodzimodzi. Motero kuti mudzakhaleko pamene dongosolo lilipoli la zinthu lidzapita, ndi pamene chilengedwe chonse chidzagwirizana pofuula kuti: “Haleluya”! [“Tamandani Ya, anthu inu!” NW].—Salmo 112:1; 135:1.
[Mawu a M’munsi]
a M’Baibulo, liwulo lakuti “Yehova” nthaŵi zina limafupikitsidwa kuti “Ya.”
[Chithunzi patsamba 5]
Mudzakhaleko pamene chilengedwe chonse chidzagwirizana pofuula kuti: “Haleluya”!