MBIRI YA MOYO WANGA
Tinapeza ‘Ngale Yamtengo Wapatali’
WINSTON ndi Pamela Payne akutumikira kunthambi ya ku Australasia. Pa moyo wawo akumanapo ndi zinthu zosangalatsa komanso mavuto. Mwachitsanzo, ankafunika kuzolowera zikhalidwe zosiyanasiyana ndiponso kupirira vuto la kupita padera. Ngakhale zinali choncho, akupitirizabe kukonda Yehova komanso anthu ndipo akusangalala ndi utumiki wawo. Tsopano tiwafunsa mafunso n’cholinga choti atifotokozere zimene zawachitikira potumikira Yehova.
A Winston, kodi munayamba bwanji kufunafuna Mulungu?
Ndinakulira m’banja losapembedza kufamu inayake ku Queensland m’dziko la Australia. Popeza tinkakhala kwatokha, sindinkacheza ndi anthu ambiri, kupatulapo a m’banja lathu. Ndili ndi zaka pafupifupi 12, ndinayamba kufuna kudziwa za Mulungu. Ndinapemphera kwa iye kuti andithandize kumudziwa bwino. Ndinachoka pafamu ija n’kukapeza ntchito ku Adelaide ku South Australia. Ndili ndi zaka 21, ndinakumana ndi Pamela pamene ndinali ku tchuthi ku Sydney. Iye anandiuza za gulu lina lachipembedzo limene limanena kuti anthu a ku Britain anachokera ku mafuko ena a Isiraeli. Gululi limanena kuti anthuwo anachokera ku mafuko 10 akumpoto a Isiraeli, omwe anapita ku ukapolo cha m’ma 700 B.C.E. Nditabwerera ku Adelaide, ndinakambirana nkhaniyi ndi mnzanga wina wakuntchito amene ankaphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Nditangokambirana naye kwa maola ochepa, makamaka zimene a Mboni amakhulupirira, ndinazindikira kuti pemphero limene ndinapereka ndili mwana lija likuyankhidwa. Ndinayamba kuphunzira choonadi chokhudza Mlengi komanso Ufumu wake. Apa tingati ndinapeza ‘ngale yamtengo wapatali.’—Mat. 13:45, 46.
A Pamela, nanunso munayamba kufufuza ngale yamtengo wapatali ija muli wamng’ono. Kodi munaipeza bwanji?
Ndinakulira m’banja lopembedza kutauni ya Coffs Harbour ku New South Wales. Makolo komanso agogo anga ankakhulupiriranso zimene gulu lachipembedzo lija linkaphunzitsa. Ineyo, mchimwene wanga, mkulu wanga komanso achibale ena ambiri tinkauzidwa kuti Mulungu amakondera anthu amene anachokera ku Britain. Zinkandivuta kukhulupirira zimenezi ndipo ndinkaona kuti sindinkamudziwa bwino Mulungu. Ndili ndi zaka 14, ndinayamba kupita kumatchalitchi osiyanasiyana monga Anglican, Baptist ndi Seventh-day Adventist. Koma konseku sanandithandize kudziwa bwino Mulungu.
Kenako banja lathu linasamukira ku Sydney komwe ndinakumana ndi Winston pa nthawi imene anali pa tchuthi. Monga wanenera, zimene tinakambirana zinachititsa kuti ayambe kuphunzira ndi a Mboni. Kungoyambira pamenepo, ankakonda kuika mavesi ambiri m’makalata amene ankandilembera. Kunena zoona, poyamba zinkandidandaulitsa ndipo pena zinkandinyansa. Koma pang’ono ndi pang’ono ndinazindikira kuti zomwe ankandiphunzitsazo zinali zoona.
Mu 1962, ndinasamukira ku Adelaide kuti ndikakhale pafupi ndi Winston. Iye anakonza zoti ndizikakhala ndi banja lina la Mboni. Banjali linali la a Thomas ndi a Janice Sloman, omwe anakhalapo amishonale ku Papua New Guinea. Banja limeneli linkandikomera mtima kwambiri. Pa nthawiyo ndinali ndi zaka 18 zokha ndipo iwo anandithandiza kudziwa bwino Yehova. Choncho inenso ndinayamba kuphunzira Mawu a Mulungu ndipo ndinazindikira kuti ndapeza choonadi. Ine ndi Winston titakwatirana, nthawi yomweyo tinayamba moyo wosangalatsa kwambiri wotumikira Mulungu. N’zoona kuti takumana ndi mavuto koma kutumikira Yehova kwatithandiza kuti tiziyamikira kwambiri ngale yamtengo wapatali imene tinapeza.
A Winston, kodi zinthu zinkayenda bwanji mutayamba kutumikira Yehova?
A. Mapu osonyeza madera amene tinayenda tikuyang’anira dera
B. Masitampa amene tinkatumizira makalata m’zilumba zina. Poyamba zilumba za Kiribati ndi Tuvalu zinkatchedwa zilumba za Gilbert ndi Ellice
C. Chilumba chokongola cha Funafuti chomwe chili ku Tuvalu. Ichi ndi chimodzi mwa zilumba zimene tinayendera kusanafike amishonale
Titangokwatirana, Yehova anatitsegulira “khomo lalikulu” loyamba la utumiki. (1 Akor. 16:9) M’bale Jack Porter ndi amene anatithandiza kuzindikira khomoli. M’baleyu anali woyang’anira dera ndipo anabwera kudzatichezera mumpingo wathu waung’ono. (Panopa ndikutumikira limodzi ndi m’baleyu m’Komiti ya Nthambi ya ku Australasia.) Jack ndi mkazi wake Roslyn anatilimbikitsa kuti tiyambe upainiya wokhazikika ndipo tinachita utumikiwu kwa zaka 5. Ndili ndi zaka 29, ine ndi Pamela tinapemphedwa kuti tizikayendera dera lakuzilumba za ku South Pacific. Nthambi ya ku Fiji ndi imene inkayang’anira ntchito yakuzilumba zimenezi. Zilumba zake zinali American Samoa, Samoa, Kiribati, Nauru, Niue, Tokelau, Tonga, Tuvalu ndi Vanuatu.
Pa nthawiyo, anthu ena pazilumbazi ankakayikira a Mboni za Yehova choncho tinkafunika kuchita zinthu mosamala kwambiri. (Mat. 10:16) Mipingo yake inali ing’onoing’ono ndipo ina sinkakwanitsa kutipezera malo ogona. Choncho tinkangopeza malo kwa anthu ena a m’midziyo ndipo ankatilandira bwino.
A Winston, kodi zinatani kuti muyambe kuchita chidwi ndi ntchito yomasulira?
Tili ku Samoa ndipo Winston akuchititsa sukulu ya akulu
Pa nthawiyo, abale akuchilumba cha Tonga anali ndi timapepala ndi timabuku tochepa m’chilankhulo chawo. Choncho, akafuna kuphunzira ndi anthu mu utumiki ankagwiritsa ntchito buku lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya lachingelezi. Titakhala ndi sukulu ya akulu ya milungu 4, akulu atatu amene ankadziwa Chingelezi pang’ono analola kuti amasulire buku la Coonadi m’chilankhulo cha Chitongani. Pamela ndi amene ankatayipa zimene amasulira kenako tinazitumiza ku United States kuti zikapulintidwe. Ntchito yonse inatenga pafupifupi miyezi iwiri. N’zoona kuti bukuli silinamasuliridwe bwino kwenikweni koma linathandiza anthu ambiri achilankhulochi kuti aphunzire choonadi. Ine ndi Pamela si ife omasulira mabuku koma zimenezi zinachititsa kuti tiyambe kuchita chidwi ndi ntchitoyi.
A Pamela, kodi moyo wakuzilumba unkasiyana bwanji ndi wa ku Australia?
Nthawi ina tinkagona m’basimu tikuyendera dera
Moyo wa kumeneku unali wosiyana kwambiri ndi wa ku Australia. M’madera ena tinkavutika ndi udzudzu, kutentha, makoswe, matenda komanso nthawi zina sitinkapeza chakudya chokwanira. Koma madzulo alionse tinkasangalala kwambiri kukhala m’nyumba yathu n’kumaona nyanja. Nyumba zake zinkangokhala ndi denga laudzu popanda khoma. Nthawi zina kukakhala mwezi nyanja inkawala ndipo mitengo ya kokonati inkaoneka. Zinthu ngati zimenezi zinkatithandiza kuti tizisinkhasinkha komanso kupemphera moti tinkasiya kuganizira mavuto athu n’kumaganizira zabwino zokhazokha.
Ana ankatisangalatsa kwambiri chifukwa ankachita nafe chidwi. Tsiku lina tili ku Niue, kamnyamata kena kanayamba kuseweretsa cheya chapamkono wa Winston n’kunena kuti: “Koma nthenga zanuzi zimandisangalatsa bwanji!” N’kutheka kuti anali asanaonepo munthu wacheya ndipo sankadziwa kuti angafotokoze bwanji.
Zinkatiwawa kwambiri kuona mmene anthu akuvutikira. Ankakhala kudera lokongola kwambiri koma analibe madzi abwino ndipo ankasowa chithandizo chakuchipatala. Koma abale athu sankadandaula. Ankaona kuti zinthu zili bwinobwino. Ankangosangalala kukhala limodzi ndi banja lawo, kukhala ndi malo olambirira komanso mwayi wotamanda Yehova. Zimenezi zinatithandiza kuti tizikhala moyo wosalira zambiri n’kumangoganizira zinthu zofunika zokhazokha.
A Pamela, munkatani kuti mupeze madzi ndi chakudya kudera lachilendo?
Tili ku Tonga ndipo Pamela akuchapa
Pa nkhani imeneyi ndimathokoza kwambiri bambo anga. Anandiphunzitsa zinthu zambiri monga kusonkha moto n’kumaphika komanso kukhala moyo wosalira zambiri. Ku Kiribati, tinafikira m’kanyumba kansungwi, kadenga laudzu ndipo pansi pake anaikapo timiyala. Kuti ndiphike, ndinkakonza malo ophikira pokumba kadzenje pa timiyalato ndipo nkhuni zake zinkakhala zamakoko a kokonati. Kuti ndipeze madzi ndinkapita kukatunga pachitsime limodzi ndi azimayi am’mudzi. Kuti atunge madzi, azimayiwo ankagwiritsa ntchito chitini, chingwe ndi ndodo yaitali pafupifupi mamita awiri. Ankatenga chingwecho n’kumangirira kundodoyo ndipo mbali ina ankamangirirako chitinicho. Akaponya chitinicho, ankapanga zinazake kuti chilowe m’madzimo n’kutunga. Ndinkaona ngati zosavuta koma itafika nthawi yoti nditunge ndinavutika kwambiri. Ndikaponya, chitinicho chinkangomenya madzi n’kumayandama osatunga madzi ngakhale pang’ono. Azimayiwo anandiseka kwambiri koma atasiya kusekako, wina anandisonyeza mmene ndingatungire. Nthawi zonse anthu akumeneku ankatithandiza mokoma mtima.
Paja nonse munkakonda utumiki wanu kuzilumba. Tatiuzeni zinthu zosangalatsa zimene zinachitika kumeneko.
Winston: Zinatitengera nthawi kuti timvetse chikhalidwe cha kumeneko. Mwachitsanzo, potipatsa chakudya abale ankatipatsa chakudya chonse chimene anali nacho. Poyamba tinkamaliza chonse osadziwa kuti tiyenera kuwasiyira china. Koma titazindikira tinayamba kuwasiyira. Abale ankatimvetsa tikalakwitsa zinthu. Iwo ankasangalala kwambiri akaona kuti tabwera kudzayenderanso mpingo wawo pambuyo pa miyezi 6. Kupatula ifeyo, abale akumeneku sankadziwana ndi abale a mipingo ina.
Tili kuchilumba cha Niue ndipo Winston akutsogolera utumiki
Kupita kwathu kumeneku kunathandizanso kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino. Tikutero chifukwa chakuti anthu ambiri ankaganiza kuti abalewo anayambitsa okha chipembedzo chawo. Choncho akaona munthu wochokera kudziko lina atabwera ndi mkazi wake kudzayendera abalewo, maganizo a anthuwo ankasintha ndipo ankachita chidwi kwambiri.
Pamela: Ine sindiiwala zimene zinachitika ku Kiribati mumpingo wina umene unali ndi abale ndi alongo ochepa kwambiri. Mumpingowu munali mkulu mmodzi yekha dzina lake Itinikai Matera ndipo anachita zonse zimene akanatha potisamalira. Tsiku lina anabwera ndi basiketi muli dzira limodzi lokha n’kunena kuti: “Limeneli ndi lanu.” Pa nthawi imeneyo, dzira la nkhuku linali mphatso yamtengo wapatali. Zimene anachitazi zinatilimbikitsa kwambiri.
A Pamela, tikudziwa kuti pa nthawi ina munapita padera. N’chiyani chinakuthandizani kupirira?
Ndinakhala woyembekezera mu 1973 ndipo pa nthawiyo, ine ndi Winston tinali ku South Pacific. Choncho tinabwerera ku Australia koma patangopita miyezi 4 ndinapita padera. Kunena zoona, Winston zinamupwetekanso kwambiri. Zinandipweteka kwa nthawi yaitali kwambiri koma mtima unakhala m’malo titalandira Nsanja ya Olonda ya April 15, 2009. M’magaziniyi munali nkhani ya “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” ya funso lakuti, “Ngati mwana wabadwa wakufa, kodi pali chiyembekezo chakuti mwanayo adzauka?” Nkhaniyo inatikumbutsa kuti Yehova amachita zoyenera nthawi zonse ndipo iye ndi amene angadziwe zochita pa nkhaniyi. Iye ndi wachikondi ndipo adzachotsa mavuto onse amene tikukumana nawo m’dziko loipali pogwiritsa ntchito Mwana wake kuti awononge ‘ntchito za Satana.’ (1 Yoh. 3:8) Nkhaniyi inatithandizanso kuti tiziyamikira kwambiri “ngale” yamtengo wapatali imene anthu a Yehovafe tili nayo. Pakanapanda chiyembekezo cha Ufumu, anthufe tikanakhala omvetsa chisoni kwambiri.
Pamela atapita padera, tinayambiranso utumiki wa nthawi zonse. Tinatumikira kunthambi ya ku Australia kwa miyezi ingapo kenako tinapita kukayang’anira dera. Mu 1981, titatumikira mumzinda wa Sydney ndi madera ena a ku New South Wales kwa zaka 4, tinaitanidwa kuti tikayambe kutumikira kunthambi. Pa nthawiyo, inkatchedwa nthambi ya ku Australia ndipo takhala tikutumikira kumeneko mpaka pano.
A Winston, kodi zimene zinakuchitikirani kuzilumba za ku South Pacific zakuthandizani bwanji pa ntchito yanu m’Komiti ya Nthambi ya ku Australasia?
Zandithandiza m’njira zingapo. Nthambi ya ku Australia inapemphedwa kuti iziyang’anira ntchito ya ku American Samoa ndi Samoa. Kenako nthambi ya ku New Zealand anaiphatikiza ndi ya ku Australia. Panopa, nthambi ya ku Australasia imayang’anira ntchito ya ku Australia, American Samoa, Samoa, Cook Islands, New Zealand, Niue, Timor-Leste, Tokelau ndi ku Tonga. Ineyo ndakhala ndi mwayi woyendera ambiri mwa mayiko amenewa ngati woimira nthambi. Kugwira ntchito limodzi ndi abale ndi alongo amuzilumbazi kwandithandiza kwambiri kuti ndiziwatumikira bwino pamene ndili kunthambi kuno.
Winston ndi Pamela ali kunthambi ya ku Australasia
Pomaliza, ndingakonde kunena kuti kwa zaka zambiri, ine ndi Pamela tazindikira kuti si akuluakulu okha amene amayesetsa kuti adziwe bwino Mulungu. Nawonso achinyamata amafufuza ‘ngale yamtengo wapatali.’ Amachita zimenezi ngakhale kuti achibale awo sasangalala nazo, ngati mmene zinalili ndi ifeyo. (2 Maf. 5:2, 3; 2 Mbiri 34:1-3) Yehova ndi Mulungu wachikondi ndipo amafuna kuti anthu onse, kaya achikulire kapena aang’ono, adzapeze moyo wosatha.
Pamene ine ndi Pamela tinayamba kufufuza Mulungu zaka 50 zapitazo, sitinkadziwa kuti zotsatira zake zidzakhala zotani. Koma tazindikira kuti choonadi chonena za Ufumu ndi ngale yamtengo wapatali kwambiri. Panopa tikufunitsitsa kugwirabe ngale imeneyi ndi mphamvu zathu zonse.