Bokosi la Mafunso
◼ Kodi komiti ya chiweruzo ya mpingo itatha kumvetsera nkhani ya munthu wolakwa ndi kupenda umboni wonse wa nkhaniyo ndi kugamula kuti munthu wolakwayo achotsedwe mu mpingo, kodi azitani naye?
Ndibwino kuti komiti ya chiweruzo ilankhule naye munthuyo, kumuuza kuti komitiyo yagamula kuti achotsedwe mumpingo. Ndiyeno imufunse ngati akufuna kuchita apilo. Angachite apilo ngati akuona kuti komitiyo sinagamule bwino nkhaniyo. Panthaŵi imene akufuna kuchita apilo, komitiyo isalengeze zimene yagamulazo. Zikatere amuuze kuti achite apiloyo pasanathe mlungu umodzi. Achite zimenezi mwa kulembera kalata komiti ya chiweruzo, ndipo apereke zifukwa zake. Komiti ya chiweruzo ikalandira kalatayo, tcheyamani wa komitiyo alankhule mwachangu ndi woyang’anira dera, amene kenako adzasankhe akulu oti aimire komiti ya apilo.
Pakatha mlungu umodzi asanachite apiloyo, lengezani kumpingo kuti wachotsedwa. Komiti ya chiweruzo izilemba chilengezo chokaŵerenga ku mpingo. Woyang’anira wotsogolera apende chilengezocho kuti aone ngati chikugwirizana ndi malangizo a Bungwe Lolamulira. Zikatero, mkulu, kapena tcheyamani wa komiti ya chiweruzo, aŵerenge chilengezocho ku mpingo pa Msonkhano wa Utumiki wotsatira.
Komanso, akulu a m’komiti ya chiweruzo am’fotokozere munthu wolakwayo kufunika kolapa ndiponso zina zimene angachite kuti panthaŵi yake adzabwezeretsedwe. Izi n’zothandiza ndiponso zabwino, pamene tikuyembekeza kuti adzasinthe njira zake ndi kubwerera m’gulu la Yehova m’kupita kwa nthaŵi.—2 Akor. 2:6, 7.