Ukhondo Umalemekeza Mulungu
1 Chilamulo cha Mose chinali ndi zofunika zamphamvu kutsimikizira ukhondo. Zinachititsa mtundu wa Israyeli kukhala anthu opatulidwa amene anafunikira kudzisunga ali oyera mwakuthupi ndi mwauzimu. (Lev. 11:35, 36; 15:1-11; Yes. 52:11) Mkhalidwe woyera umenewu unadzetsa ulemu kwa Mulungu ndi kuchirikiza thanzi la mtunduwo.
2 Lerolinonso, ukhondo ndiwo chizindikiro chodziŵikitsa anthu a Yehova. Koma pamene kuli kwakuti chimenechi chimazindikiritsa anthu a Yehova monga gulu, kodi zimenezi zili choncho kwa ife aliyense payekha? Mlingo umene timadera nkhaŵa ponena za udongo ndi ukhondo wa munthu mwini umasonyeza za mmene timayamikirira zofunika za Yehova.
3 Bwanji ponena za kaonekedwe ka nyumba yathu? Kodi imanyazitsa uthenga wa Ufumu umene tili nawo? Kodi nkotheka kuti ena angakayikire za kuona mtima kwathu ngati tilankhula za kusandulizidwa kwa dziko lapansi kukhala paradaiso pamene nyumba ya ife eni ili yauve ndipo bwalo lake lili lowirira ndi udzu? Ngati nyumba yathu ili ndi kaonekedwe kosalongosoka kapena ngati pali fungo loipa chifukwa cha zizoloŵezi za kusasamalira chimbudzi, kodi kunganenedwe kuti takulitsa “zitsanzo za chiyero zimene zidzayenerana ndi dziko latsopano mu Ufumu wa Mulungu”?—om-CN tsa. 130.
4 Bwanji za galimoto limene timagwiritsira ntchito muutumiki wakumunda? Kodi nloyera bwino, mkati ndi kunja, kotero kuti kaonekedwe kake sikakunyazitsa ntchito yathu? Bwanji za zovala zathu, chola chathu cha mabuku, ndi kapesedwe kathu? Kodi izo nzaudongo ndi zolemekezeka, zosapereka chifukwa chokhumudwitsa? Kuli bwino kuti ife enife tidzisunge tili oyera ndi zovala zathu mwa kusamba nthaŵi zonse ndi kuchapa zovala.—w89-CN 6/1 mas. 16-19.
5 Bwanji nanga ngati mbale wafikira kukhala wosasamala kwakuti kusoŵa ukhondo kwake kapena pokhala pake pafikira kukhala chotonzetsa mpingo? Mwinamwake iyeyo angofunikira chithandizo chachikondi chifukwa cha ukalamba kapena kudwala. Ngati zili choncho, kukakhala kukoma mtima kumthandiza. Munthu wina angakhale ndi vutolo ndipo mwina sangalidziŵe; chilangizo chokoma mtima chingamsonkhezere kuwongolera mkhalidwewo. Anthu amene amapitirizabe kupereka chitsanzo choipa pankhaniyi sangayenerere kulandira mathayo apadera mumpingo. Zowonadi, akulu ayenera kusamala kuti sakuika miyezo ya iwo eni kapena zimene amakonda.
6 Anthu okondwerera chatsopano amaitanidwa kudzasangalala ndi phwando lauzimu pa Nyumba Yaufumu. Kaŵirikaŵiri, timakhala ofunitsitsa kuitana ena chifukwa chakuti nyumbayo njokongola ndi yaudongo. Komabe, pamafunikira ntchito kuti ikhale choncho. Unguzani panyumba yanuyo. Kodi mipando yake, pansi pake, ndi zipupa nzoyera? Kodi zimbudzi zake zimasamalidwa nthaŵi zonse? Pamene tizoloŵera kuona pansi pokumbika ndi ming’alu kapena zipupa zautoto wokanganuka, ife mofulumira tingaone zimenezi kukhala zozolowereka. Komabe, alendo ofikapo kwanthaŵi yoyamba angasiyidwe ali ndi lingaliro losakondweretsa. Tiyenera kuyesayesa kuchita zomwe tingathe kusungitsa mkhalidwe wokopa ndi wokongola wa nyumbayo, tikumachita mbali yathu pamene nthaŵi ya kuyeretsa ndi kukonza m’nyumbayo ifika.
7 Tikhoza kulemekeza Mulungu ndi kaonekedwe kathu ndi udongo wa nyumba zathu, galimoto, ndi Nyumba zathu Zaufumu popanda kunena mawu. Chitsanzo chathu chabwino sichidzapereka chifukwa china chilichonse chokhumudwitsa koma chidzasonyeza umboni wakuti kulambira kwathu kuli koyera ndi kowona.—1 Akor. 10:31, 32; Yak. 1:27.