Tumikirani Yehova popanda Chochenjeneketsa
1 “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” (Sal. 144:15) Kodi mawuŵa a Mfumu Davide adakali owona, ngakhale m’masiku ano oipa? (Aef. 5:16) Inde! Akristu adakapezabe chisangalalo m’kutumikira Yehova. Si nthaŵi zonse pamene zinthu zimakhala zofeŵa kwa ife. Satana amatidzetsera zovuta mkati mwa “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino, komabe sititaya mtima. (2 Tim. 3:1, 2) Mikhalidwe yomaipaipirabe ili umboni wowonjezereka wakuti nthaŵi yayandikira yakuti Ufumu wa Mulungu ufafanize dziko lakale lowolali ndi kuloŵetsa mmalo mwake dziko latsopano loyera. (2 Pet. 3:13) Mdima wa dzikoli sumaphimba kapena kuzimitsa laŵi la chiyembekezo chathu chachisangalalo; mmalo mwake, chiyembekezo chathu cha Ufumu chikuŵaliraŵalira mwamphamvu nthaŵi zonse. Kodi simuli wosangalala kutumikira Yehova monga muuni m’dziko lino lamdima?—Afil. 2:15.
2 Aliyense payekha, tiyenera kudziyang’anira nthaŵi zonse mmene timatumikirira Yehova. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Satana ali Wododometsa wamkulu. Dikishonale ina imatanthauzira “kuchenjeneketsa” kukhala “kudodometsa,” “kukopa kapena kutembenuzira (maganizo a munthu) ku chinthu china kapena ku njira zosiyana panthaŵi imodzimodzi,” ndi “kupotoza kapena kusokoneza mwa kupereka malingaliro kapena zolinga zowombana.” Chiyambire pamene anaponyedwa padziko lapansi lino, Satana wakhala ndi chipambano pa ‘kunyenga’ mtundu wa anthu. Iye amagwiritsira ntchito machenjera ambiri kuchotsa maganizo a anthu pankhani zowona za m’tsiku lathu. (Chiv. 12:9) Ngakhale kuti Mboni za Yehova zadzipereka mwamphamvu m’kulalikira Ufumu kwa zaka zana limodzi zapitazo, kodi ndi anthu angati amene amazindikira nkhani zofunika koposa za kuyeretsa dzina la Mulungu ndi kulemekeza uchifumu wake mwa Ufumu wa Mulungu? Ali oŵerengeka chabe. (1 Yohane 5:19) Ngati Satana akhoza kuchenjeneketsa mamiliyoni zikwi a anthu padziko lapansi, ngozi yokhalapo nthaŵi zonse ndi yakuti akhoza kuchenjeneketsa ifenso kapena kukopa maganizo athu kotero kuti tisiye utumiki wa Yehova. Mwachisoni, abale athu ena asokonezedwa ndi zochenjeneketsa za Satana. Alola maganizo awo kukopedwa m’njira zosiyanasiyana. Pali zododometsa za mitundu yonse lerolino. Talingalirani zoŵerengeka chabe.
3 Mavuto a Chuma ndi Chikondi cha pa Zinthu Zakuthupi: M’maiko ambiri a dziko lapansi, ulova ndi kukwera mtengo kwa zinthu zimachititsa nkhaŵa. Nzowona, tiyenera kupeza chakudya, zovala, ndi nyumba kaamba ka ife eni ndi mabanja athu. Koma ngati tidzilola kukhala odera nkhaŵa mopambanitsa pa zofunika za moyo, nkhaŵa zimenezi zidzalamulira kalingaliridwe kathu. Kukhalapo kwathu ndi moyo kungakhale chinthu chofunika koposa m’moyo mmalo mwa kuchirikiza nkhani ya Ufumu. Mtumwi Paulo anapereka uphungu pankhaniyi pa Ahebri 13:5, 6. Yesu Kristu akutitsimikizira kuti awo amene afunafuna Ufumu choyamba safunikira kukhala odera nkhaŵa; Yehova amapereka zimene timafunikiradi. (Mat. 6:25-34) Apainiya ndi atumiki a nthaŵi yonse kuzungulira dziko lonse akhoza kuvomereza kuti zimenezi zilidi zowona.
4 Dziko la Satana limachirikiza chikondi cha pa zinthu zakuthupi. Kupeza zinthu zowonjezereka kapena kuzitetezera ndiko mphamvu imene imasonkhezera miyoyo ya mamiliyoni a anthu. Zochenjeneketsa zofananazo zinalipo m’tsiku la Yesu. Mnyamata wina wachuma anafunsa Yesu zimene anafunikira kuchita kuti apeze moyo wosatha. Yesu anayankha kuti: “Ngati ufuna kukhala wangwiro [kapena, wa mtima wamphumphu], pita, kagulitse zonse uli nazo, nupatse aumphaŵi, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba, ndipo ukadze kuno, unditsate.” (Mat. 19:16-23) Mwachionekere, chuma chake chambiricho chinachenjeneketsa mnyamatayu pa kutumikira Mulungu ndi moyo wonse. Mtima wake unakopedwera pa chuma chake. Yesu anadziŵa kuti mnyamatayu akapindula ngati akanadzichotsera mtolo wa zochenjeneketsa zimenezi. Izo zinamlepheretsa kukhala wa mtima wamphumphu pa kudzipereka kwake kwa Mulungu. Bwanji ponena za inuyo? Kodi mumakhala mukugwira ntchito yakuthupi kwa maola ochulukirapo kuti chabe musunge njira ya moyo imene mwaizoloŵera? Kodi zimenezi zayambukira utumiki wanu kwa Yehova? Kodi chuma chanu chakuthupi chikutenga nthaŵi yanu yaikulu kwambiri kwakuti simutsala ndi iliyonse kaamba ka zinthu za Ufumu? (Mat. 6:24) Kodi mukhoza kufeŵetsa moyo wanu kuti mupereke nthaŵi yowonjezereka ku zinthu zauzimu?
5 Zochita Wamba za Moyo wa Tsiku ndi Tsiku: Ngati sitisamala, tingatanganitsidwe kwambiri ndi zochita wamba za moyo kwakuti nkuyamba kunyalanyaza zinthu zauzimu. Kumbukirani anthu a m’tsiku la Nowa. Iwo anali otanganitsidwa kwambiri ndi zinthu za umoyo, kudya ndi kumwa, kukwatira ndi kukwatitsa ana awo, kwakuti sanazindikire za uthenga wochenjeza wa Nowa wa Chigumula choyandikiracho. Iwo asanazindikire, Liyambwelo linafika nilisesa onse. Zochenjeneketsa zinachititsa kuwonongedwa kwawo. Yesu anati: “Kotero, kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.” (Mat. 24:37-39) Ndithudi, anthu ochuluka lerolino ali otanganitsidwa kwambiri ndi miyoyo yawo kwakuti samasamala za uthenga wochenjeza umene timawapatsa. Iwo amasonyeza mphwayi yochititsa mantha pa zinthu zauzimu.
6 Kodi moyo wanu ukuchulukiridwa kwambiri ndi zochita za umoyo kwakuti zinthu zauzimu zikupatsidwa chisamaliro chocheperachepera? Nthaŵi ina, Yesu anaitanidwa monga mlendo m’nyumba mwa Marita ndi Mariya. Mariya anali kumvetsera mosamalitsa zimene iye anali kunena. Komabe Marita, “anatekeseka ndi kutumikira kwambiri.” Marita anali ndi nkhaŵa yopambanitsa ya kukhala wochereza mlendo wabwino. Iye analephera kuzindikira kufunika kwa kupatula nthaŵi ndi kumvetsera kwa Yesu. Yesu mokoma mtima anauza Marita kuti zakudya zabwino koposa sizinali zofunikira kwenikweni; chisamaliro chachikulu chiyenera kuikidwa pa zinthu zauzimu. Kodi inuyo mufunikira kulabadira uphungu umenewo? (Luka 10:38-42) Yesu anachenjezanso kuti tiyenera kudziyang’anira tokha kuti tisamadye ndi kumwa mopambanitsa, tikumagodomalitsa maganizo athu. Pa nyengo ino yovuta kwambiri ya mbiri ya munthu, tifunikira kukhala ogalamuka kwenikweni.—Luka 21:34-36.
7 Kufuna Zosangulutsa: Chimodzi cha zochenjeneketsa zazikulu kopambana zimene Mdyerekezi amagwiritsira ntchito kuchotsa maganizo a anthu pa nkhani ya Ufumu ndicho kufuna zosangulutsa. Anthu mamiliyoni m’Dziko Lachikristu aika zosangulutsa pamalo a Mulungu. Iwo amakonda kusangalatsidwa ndi zocheutsa mmalo mwa kuika chikondwerero chachikulu m’Mawu a Mulungu. (2 Tim. 3:4) Ndithudi, zosangulutsa zoyenera ndi maseŵera si zolakwa mwa izo zokha. Koma kuwononga nthaŵi yaikulu kwambiri mlungu ndi mlungu pa zinthu zoterozo monga wailesi yakanema, akanema, mavidiyo, maseŵera, kuŵerenga mabuku adziko, kapena zokonda zina kungatichititse kukhala ndi mtima wonyenga umene ungatipambutse kwa Yehova. (Yer. 17:9; Aheb. 3:12) Kodi zimenezo zingachitike motani? Mkati mwa misonkhano Yachikristu, mungaone kuti maganizo anu akuyendayenda; mungakhumbe kuti msonkhano uthe kotero kuti mupite ku zosangulutsa. Posapita nthaŵi, mungayambe kufunafuna zifukwa zakuti mukhalire panyumba mmalo mopita kumisonkhano kapena muutumiki wakumunda. Tsopano ndiyo nthaŵi yakuti tipende mosamalitsa kuona ngati zosangulutsa zimenezi zakhala zangozi m’moyo wanu. (Luka 8:14) Kodi ena a maola amtengo wake amene amatengedwa ndi zosangulutsa sangagwiritsiridwe ntchito mwanjira yabwinopo kaamba ka kupita patsogolo kwauzimu?
8 Nkhani za Umoyo Zotayitsa Nthaŵi: Ena akoledwa m’zoyesayesa za kuthetsa mavuto ofala m’chitaganya cha makono. Akristu ayenera kupeŵa kudziloŵetsa m’mikangano yosatha ya dzikoli ya nkhani za umoyo kapena kuyesayesa kwake kosaphula kanthu kofuna kuwongolera zisalungamo. (Yohane 17:16) Zonsezi zili mbali ya machenjera a Satana a kupambutsa maganizo a anthu pa uphungu wa Baibulo ndi chenicheni chakuti pali njira yeniyeni imodzi yokha yothetsera mavuto—Ufumu wa Mulungu. Ngati tinachitiridwa moipa kapena mosalungama, tiyenera kupeŵa kukhala ndi maganizo akubwezera kapena kuvutitsidwa mtima kwambiri kwakuti tiiŵala amene tili—Mboni za Yehova. Kwenikweni, ali Yehova amene amalakwiridwa, ndipo ndi dzina lake limene tiyenera kuyeretsa.—Yes. 43:10-12; Mat. 6:9.
9 Pamene kuli kwakuti aliyense akufuna kukhala ndi thanzi labwino, kupereka chisamaliro chopambanitsa pamalingaliro ndi njira zothandiza zoonekera kukhala zosatha kungachititse munthu kukhala wodera nkhaŵa kwambiri ndi nkhani za thanzi. Nthaŵi zonse pakhala anthu ambiri amene amachirikiza mitundu yosiyanasiyana ya zakudya, mankhwala, ndi zithandizo pamavuto akuthupi ndi amalingaliro, ndipo zambiri zimawombana. Zimene munthu amachita m’nkhani ya thanzi zili chosankha chaumwini, malinga ngati sipakhala kuwombana ndi malamulo a mkhalidwe a Baibulo. Lolani kuti nthaŵi zonse tisunge chidaliro chathu chokwanira pa Ufumu wa Mulungu monga mankhwala okha a matenda a mtundu wa anthu.—Yes. 33:24; Chiv. 21:3, 4.
10 Khalani Wokhazikika, Wosasunthika: Pamene mapeto akuyandikira, Satana adzawonjezera zoyesayesa zake za kukuchenjeneketsani pa utumiki wanu kwa Yehova. “Mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro.” (1 Pet. 5:9) Motani? Muyenera kudzilemeretsa ndi malingaliro a Mulungu. (Mat. 4:4) Musalole zochenjeneketsa za dziko lino kulanda inuyo ndi banja lanu nthaŵi imene mufunikira kuti musinkhesinkhe ndi kupenda mwabata Mawu a Mulungu. Pa chakudya cha banja, kambitsiranani pamodzi zochitika zomangirira ndi nkhani zina zauzimu. Mamatirani pa ndandanda yokhazikika ya phunziro laumwini ndi kukonzekera misonkhano.
11 Pamene nkhaŵa zioneka kuti zikulepheretsa maganizo anu kukhazikika, perekani nkhaŵa zanuzo kwa Yehova m’pemphero. Khalani wotsimikiza kuti iye amakusamalani. (1 Pet. 5:7) Lolani kuti mtendere wa Mulungu utetezere mtima wanu ndi mphamvu za maganizo anu. (Afil. 4:6, 7) Musalole zochenjeneketsa kuphimba maso anu auzimu. Ikani Yehova patsogolo panu nthaŵi zonse, monga momwe anachitira Yesu. (Mac. 2:25) Sumikani maso anu molunjika pa chonulirapo chanu mtsogolo, monga momwe lemba la Miyambo 4:25-27 limatilimbikitsira kuti: “Maso ako ayang’ane mtsogolo, zikope zako zipenye mowongoka. Sinkhasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako; njira zako zonse zikonzeke. Usapatuke kudzanja lamanja kapena kulamanzere.”
12 Fikani mokhulupirika pamisonkhano yonse, ndipo dzilangeni nokha kuti musamalire chilangizo cha m’Mawu a Mulungu. (Aheb. 2:1; 10:24, 25) Ndipo mmalo mofunafuna zosangulutsa zoperekedwa ndi dziko lino la makhalidwe oluluzika, dziikireni chonulirapo cha kukhala ndi utumiki wobala zipatso. Ichi nchimene chimadzetsa chisangalalo chosatha ndi chikhutiro. (1 Ates. 2:19, 20) Pomalizira, musalole chilichonse kapena aliyense kukuchenjeneketsani pa utumiki wanu. “Khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.”—1 Akor. 15:58.