Kodi Tikudikira—Tikumapeŵa Zochenjenetsa?
1 Yesu anachenjeza kuti: “Dikirani . . . , kuti mukalimbike kupulumuka” masoka analinkudza. (Luka 21:36) Tikukhala m’nthaŵi yowopsa koposa m’mbiri ya munthu. Tsoka likuyembekezera aja amene amawodzera mwauzimu. Zimenezi zikutiika pangozi tonsefe. Yesu anatchula za madyaidya, kuledzera, ndi zosamalira za moyo wa tsiku ndi tsiku. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ngakhale zinthu zimenezi zingatitanganitse, zikumakhala zochenjenetsa, ndi kutichititsa kuwodzera kowopsa kwauzimu.
2 Zochenjenetsa Zofala: Ena atanganitsidwa ndi zosangulutsa zopambanitsa zosaoneka bwino. Ndithudi, kufunafuna Ufumu choyamba sikumatanthauza kuti tiyenera kupeŵa kusanguluka kwa mtundu uliwonse. Pamene tichita mosamala ndi modekha, kusanguluka kungakhale kopindulitsa. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 4:8.) Koma kumakhala chochenjenetsa pamene kukhala chinthu chachikulu kwambiri m’moyo, kukumatidyera nthaŵi yathu yochuluka, chuma chathu, kapena kusokoneza ntchito yathu yolalikira Ufumu.
3 Chochenjenetsa china chofala chimene chimachititsa kuwodzera kwauzimu ndicho kukhumba zinthu zakuthupi zosafunikira. Zimenezi zimafuna kuti munthu awonongere nthaŵi yochuluka kuntchito ndipo zimachititsa zinthu zauzimu kutsamwitsidwa. Ena aiŵala zonulirapo zauzimu mwa kutengeka ndi kukundika chuma kuti akhale ndi moyo wabwino kwambiri. Pamene kuli kwakuti tifunika “zakudya ndi zofunda,” tiyenera kusamala kuti tisakhale ndi chikondi cha pa ndalama, chimene chingatisokeretse kutaya chikhulupiriro. (1 Tim. 6:8-10) Mwa kulephera kusumika maso athu pa zinthu za Ufumu, tingakhale aulesi posamalira zofunika zauzimu za banja lathu ndi kulephera kukwaniritsa utumiki wathu.—1 Tim. 5:8; 2 Tim. 4:5.
4 Ndiponso ena amalola ‘mitima yawo kulemetsedwa ndi zosamalira za moyo’ kwakuti amagona tulo tauzimu. (Luka 21:34) Nthaŵi zina, nkhaŵa imakhalapo chifukwa cha matenda kapena mavuto m’banja. Koma sitiyenera kulola nkhaŵa zotero kutiiŵalitsa za mapeto a dongosolo ili la zinthu amene akudza mofulumira.—Marko 13:33.
5 Chimene Mdyerekezi angakondwere nacho kwambiri ndicho kutinyengeza, akumatichititsa kulondola maloto adziko basi. Tiyenera kulimbikira kuti tikhale odikira mwauzimu. Tikudziŵa kuti ‘tsiku la Yehova lidzadza monga mbala,’ ndipo tifunika ‘kudikira, ndipo tisaledzere.’ (1 Ates. 5:2, 6) Tikamva kuti tikuyamba kuwodzera, tiyenera kufulumira ‘kuvula ntchito za mdima.’—Aroma 13:11-13.
6 Zotithandiza Kukhala Odikira: Kodi zothandizazo nzotani? Pemphero nlofunika. Tiyenera kupemphera kosaleka. (1 Ates. 5:17) Kukhala pafupi ndi mpingo Wachikristu ‘kudzatifulumiza ku chikondano ndi ntchito zabwino.’ (Aheb. 10:24) Kudzipenda ife eni moona mtima nthaŵi zonse kungatithandize kukhala atcheru kuti tigonjetse zofooka zathu. (2 Akor. 13:5) Zizoloŵezi zabwino za phunziro laumwini zidzatichititsa ‘kuleredwa m’mawuwo a chikhulupiriro.’ (1 Tim. 4:6) Ngati tichita khama, tingakhale ndi chidaliro chakuti tidzakhoza kupeŵa zochenjenetsa, ‘kudikira, ndi kuchirimika m’chikhulupiriro.’—1 Akor. 16:13.