Misonkhano Yautumiki ya October
Mlungu Woyambira October 2
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Limbikitsani onse kusunga kope lawo la “Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1996” imene yaikidwa m’kope lino la Utumiki Wathu Waufumu. Ayenera kuliika pamalo osavuta kuti azionamo mu 1996.
Mph. 15: “Tamandani Yehova Nthaŵi Zonse.” Mafunso ndi mayankho. Gogomezerani tanthauzo la Malemba osonyezedwa ndi ogwidwa mawu.
Mph. 20: “Gaŵirani Magazini Nthaŵi Iliyonse.” Kambani mfundo zazikulu, ndiyeno sonyezani nkhani zimene zingagwiritsiridwe ntchito pogaŵira makope atsopano. Khalani ndi zitsanzo zosonyeza maulaliki aŵiri kapena atatu.
Nyimbo Na. 153 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 9
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Zosoŵa za pamalopo. Kapena nkhani yokambidwa ndi mkulu yakuti, “Kuchotsa—Makonzedwe Achikondi?” yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 1995, masamba 25-7.
Mph. 20: “Kodi Tikudikira—Tikumapeŵa Zochenjenetsa?” Mafunso ndi mayankho. Ngati nthaŵi ilola, wonjezanipo mfundo zotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 1992, masamba 20-2.
Nyimbo Na. 128 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 16
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Sonyezani kabuku kakuti Good News for All Nations, kamene kali ndi maulaliki akunyumba ndi nyumba m’zinenero 59 zosiyanasiyana. Alimbikitseni kugwiritsira ntchito kabukuka pamene akumana ndi anthu olankhula chinenero chachilendo m’gawo.
Mph. 15: “Mboni za Yehova ndi Maphunziro.” Mkulu akambitsirana ndi omvetsera mbali za brosha latsopanoli mwa kugwiritsira ntchito manotsi a nkhani ya pamsonkhano wachigawo. Khalani ndi chitsanzo choyesezedwa bwino kusonyeza mmene kholo lingalankhulire ndi mphunzitsi kapena akuluakulu a sukulu ndi kugaŵira broshalo. Limbikitsani aja omwe ana awo amapita kusukulu kugaŵira broshalo malinga ndi malangizo a m’nkhani ya pamsonkhano ngati kuti sanachitebe zimenezo.
Mph. 20: “Maulendo Obwereza Okhala ndi Chifuno.” Kambani za zonulirapo zathu popanga maulendo obwereza. Konzani kuti ofalitsa okhoza bwino achite zitsanzo ziŵiri zosiyana za ulaliki.
Nyimbo 130 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 23
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Mbiri Yateokrase.
Mph. 15: “Mpingo Uli Wofunika kwa Ife.” Mafunso ndi mayankho.
Mph. 20: Tsogolerani Okondwerera ku Gulu. Woyang’anira utumiki akukambitsirana ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu, akumagwiritsira ntchito brosha lakuti Mboni za Yehova Zikuchita Chifuniro cha Mulungu Mogwirizana pa Dziko Lonse Lapansi. Fotokozani chifukwa chake kuli kopindulitsa kudziŵitsa okondwerera mmene gulu limayendera, mmene ntchito zosiyanasiyana zimakonzedwera, ndi mmene iwo angatengeremo mbali. Kambitsiranani mfundo zotengedwa pamasamba 14 ndi 15 pamutu wakuti “Misonkhano Yosonkhezera Chikondano ndi Ntchito Zabwino.” Ofalitsawo achite chitsanzo chachidule kusonyeza mmene mfundozi zingaphatikizidwire pa kukambitsirana kwa paulendo wobwereza kapena paphunziro la Baibulo kuthandiza munthu wokondwererayo kuzindikira kufunika kwake kwa kupezekapo.
Nyimbo Na. 126 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 30
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Popeza kuti kudzakhala holide yakudziko m’December, limbikitsani achinyamata onse obatizidwa kulembetsa upainiya wothandiza.
Mph. 15: Kodi Mwayesa Kulalikira Mabwenzi a Phunziro Lanu? Nkhani. Ofalitsa ena ayambitsa maphunziro atsopano a Baibulo mwa njira iyi: Ataphunzira ndi munthu wokondwerera kwa kanthaŵi, amafunsa munthuyo ngati akudziŵa aliyense pakati pa mabwenzi ake, achibale, kapena achinansi amene angafune kuphunzira Baibulo. Nthaŵi zambiri amapereka maina angapo. Mfunseni ngati mungagwiritsire ntchito dzina lake pofikira anthu amenewo. Mutafika panyumba, munganene kuti: “Auje akukondwera kwambiri kuphunzira Baibulo kwakuti aganiza kuti inunso mungafune kupindula ndi programu ya phunziro laulere la Baibulo.” Zimenezi zingakuchititseni kukhala ndi mpambo wabwino wa maulendo obwereza amene angakhale maphunziro a Baibulo opita patsogolo. Phatikizanipo chokumana nacho chimodzi kapena ziŵiri za ofalitsa amene apeza anthu okondwerera kapena amene ayambitsa maphunziro atsopano a Baibulo mwa njira imeneyi.
Mph. 20: Kugaŵira New World Translation Ndi Buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? mu November. Fotokozani mbali za New World Translation m’buku la Kukambitsirana, masamba 327-330. Ŵerengani “Tanthauzo,” lofotokoza chifukwa chake inalembedwa. Yankhani mafunsoŵa: Kodi matembenuzidwe ameneŵa anazikidwa pa chiyani? Kodi otembenuza ake anali ayani? Kodi alidi matembenuzidwe aukatswiri? Kodi nchifukwa ninji dzinalo Yehova likugwiritsiridwa ntchito m’Malemba Achigiriki Achikristu? Ndiyeno fotokozani chifukwa chake tiyenera kukhala oyamikira pokhala ndi matembenuzidwe ameneŵa. (Onani buku la “All Scripture,” tsamba 331, ndime 22 ndi 23.) Wofalitsa wokhoza bwino achitire chitsanzo ulaliki wachidule mwa kugwiritsira ntchito mawu oyamba m’mutu 14 wa buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? patsamba 184. Kumbutsani onse kuwombola makope okagwiritsira ntchito mu utumiki mlungu uno.
Nyimbo Na. 138 ndi pemphero lomaliza.