Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/95 tsamba 8
  • Maulendo Obwereza Okhala ndi Chifuno

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maulendo Obwereza Okhala ndi Chifuno
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Maulendo Obwereza Amathandiza Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Limbikani Mtima Kuti Mupange Maulendo Obwereza
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Kukulitsa Chikondwerero pa Maulendo Obwereza
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 10/95 tsamba 8

Maulendo Obwereza Okhala ndi Chifuno

1 Paulendo wobwereza, muyenera kuyesa kugwiritsira ntchito lemba limene lidzawonjezera chidziŵitso cha munthuyo pa nkhani ya Baibulo imene munakambitsirana poyamba.

2 Cholinga china popanga maulendo obwereza kwa amene tinagaŵira magazini ndicho kukhazikitsa njira ya magazini. Ulaliki wosavuta wonga wotsatirawu ungakhale wogwira mtima:

◼ “Ndikhulupirira munakondwera nayo nkhani ya mu Nsanja ya Olonda imene ndinakusiyirani yofotokoza chifukwa chake tiyenera kuwopa Mulungu. Lero ndakubweretserani magazini a Galamukani! amene ali ndi funso lakuti: ‘Nchifukwa Ninji Moyo Uli Waufupi Motere?’ Kodi si funso labwino limeneli?” Mungapitirize mwa kunena kuti: “Mawu a Yesu odziŵika kwambiri pa Yohane 3:16 amalonjeza moyo wosatha. Chonde tengani magaziniwa ndipo lolani kuti chiyembekezo cholimba choperekedwa m’Mawu a Mulungu chikulimbikitseni.” Ndiyeno fotokozani kuti mudzabweretsanso makope ena ndipo mwinamwake kukambitsirana zowonjezera zimene Mulungu walonjeza anthu omvera. Kumbukirani kuti nthaŵi iliyonse imene mubweretsa magazini, muyenera kulemba ulendo wobwereza.

3 Ngati munagaŵira nkhani yakuti “Dziko Lopanda Nkhondo—Lidzafika Liti?” munganene kuti:

◼ “Kodi moyo ukanakhala wotani pa dziko lapansi ngati kunalibe nkhondo? [Yembekezani yankho.] Lekani ndikusonyezeni zimene Mulungu walonjeza kuchita.” Ŵerengani Salmo 37:10, 11, ndi kufotokoza mmene zinthu zidzakhalira pamene chifuniro cha Mulungu chidzachitidwa pano pa dziko lapansi. Kumbutsani munthuyo zimene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupempherera zolembedwa pa Mateyu 6:9, 10. Muthandizeni kulingalira za tanthauzo la mawu a Yesu. Gaŵirani sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! ndi kupanga makonzedwe a kudzakambitsirana zowonjezera.

4 Ngati mwapanga ulendo wobwereza kukakambitsirana zowonjezera pa nkhani ya pachikuto yakuti “Nchifukwa Ninji Moyo Uli Waufupi Motere?” mungayambe mwa kunena kuti:

◼ “Paja pamene ndinali kuno, tinakambitsirana za utali wa moyo wa munthu. Monga momwe munaonera m’nkhani za mu Galamukani!, asayansi sakupereka chiyembekezo chenicheni cha kutithandiza kukhala ndi moyo zaka zoposa 70 kapena 80. Koma kodi muganiza bwanji za zimene Baibulo limalonjeza? [Yembekezani yankho.] Baibulo limasonyeza kuti Mulungu ali ndi kanthu kena kabwino kamene afuna kuchitira munthu.” Ndiyeno ŵerengani Yohane 17:3, ndi kufotokoza mmene kupeza chidziŵitso kungatsogolere ku moyo wosatha. Tsopano mukhoza kugaŵira phunziro la Baibulo lapanyumba kapena kulinganiza za makambitsirano a Baibulo ena.

5 Kuyambitsa phunziro la Baibulo kuli chonulirapo chofunika cha utumiki wathu. Mwinamwake mwapanga maulendo angapo kwa munthu amene analandira magazini. Bwanji osayesa njira yotsatirayi pamene mupitakonso?:

◼ “Anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana ponena za chipembedzo ndi phindu lake pa moyo wamakono. Pali zikhulupiriro zosemphana ponena za chifukwa chimene Mulungu walolera kuipa kapena chifukwa chake timakalamba ndi kufa. Anthu ena amafuna kudziŵa mmene angapempherere kwa Mulungu ndi kumvedwa.” Tsegulani chofalitsa chathu chilichonse chophunzirira Baibulo pankhani imene muganiza kuti idzachititsa chidwi mwininyumba, ndipo sonyezani mwachidule mmene timachitira phunziro.

6 Yehova ndi Mulungu wachifuno. Tiyeni timtsanzire mu October mwa kupanga maulendo obwereza okhala ndi chifuno.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena