Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1996
MALANGIZO
Mu 1996, otsatiraŵa ndiwo adzakhala makonzedwe pochititsa Sukulu Yautumiki Wateokratiki.
MABUKU OPHUNZIRA: Baibulo Lopatulika [bi53], Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona [uw-CN], Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu [om-CN], Kukambitsirana za m’Malemba [rs-CN], Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha [kl-CN], ndi Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako [gt-CN] adzakhala magwero a nkhani zimene zidzagaŵiridwa.
Sukulu iyenera kuyamba PANTHAŴI YAKE ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje, ndiyeno kupitiriza motere:
NKHANI NA. 1: Mphindi 15. Imeneyi iyenera kukambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira, ndipo idzatengedwa m’buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona kapena Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu. Pamene itengedwa m’buku la Uminisitala Wathu, nkhaniyi iyenera kukambidwa monga nkhani yachilangizo ya mphindi 15 popanda mafunso openda; pamene itengedwa m’buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa, iyenera kukambidwa monga nkhani yachilangizo ya mphindi 10 mpaka 12 yotsatiridwa ndi mafunso openda a mphindi 3 mpaka 5, mwa kugwiritsira ntchito mafunso osindikizidwa m’bukulo. Cholinga chake sichiyenera kukhala cha kungokamba nkhaniyo koma kusamalira kwambiri za phindu lenileni la chidziŵitso chimene chikufotokozedwa, mukumagogomezera mfundo zomwe zidzakhala zothandiza kwambiri mpingowo. Gwiritsirani ntchito mutu wosonyezedwa. Onse akulimbikitsidwa kukonzekera bwino lomwe pasadakhale kotero kuti akapindule mokwanira ndi nkhani imeneyi.
Abale opatsidwa nkhani imeneyi ayenera kukhala osamala kusunga nthaŵi. Uphungu wamseri ungaperekedwe ngati uli wofunikira kapena ngati wapemphedwa ndi mlankhuliyo.
MFUNDO ZAZIKULU ZA KUŴERENGA BAIBULO: Mphindi 6. Nkhaniyi iyenera kukambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira amene adzagwiritsira ntchito nsongazo pa zofunika za kumaloko. Siyenera kukhala chidule wamba cha kuŵerenga kwa mlunguwo. Choyamba perekani chithunzi chachidule cha machaputala onse a mlunguwo pa masekondi 30 mpaka 60. Komabe, cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvetsera kuzindikira chifukwa chake ndi mmene chidziŵitsocho chilili chaphindu kwa ife. Ndiyeno woyang’anira sukulu adzauza ophunzirawo kupita kumakalasi awo osiyanasiyana.
NKHANI NA. 2: Mphindi 5. Iyi ndi nkhani ya kuŵerenga Baibulo kwa mbali yogaŵiridwa kochitidwa ndi mbale. Nkhaniyi idzakambidwa m’sukulu yaikulu limodzinso ndi m’timagulu tinato. Kaŵirikaŵiri mbali zoŵerenga zimakhala zazifupi kulola wophunzira kukamba mawu oyamba ndi omaliza opereka chidziŵitso pankhaniyo. Zingaphatikizepo mbiri yakale, tanthauzo la ulosi kapena la chiphunzitso, ndi mmene zitsogozo zingagwirire ntchito. Mavesi onse ogaŵiridwa ayenera kuŵerengedwa mosalekeza. Ndithudi, pamene mavesi owaŵerenga saali ondondozana, wophunzira angatchule vesi lopitirizira kuŵerengako.
NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Nkhaniyi idzapatsidwa kwa mlongo. Idzatengedwa m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Wophunzira wopatsidwa nkhaniyi ayenera kukhala wodziŵa kuŵerenga. Pokamba nkhaniyi, wophunzira angakhale pansi kapena kuimirira. Pamene itengedwa m’buku la Kukambitsirana, mlongo wokamba nkhaniyi ayenera kugwirizanitsa mutu wa nkhaniwo ndiponso nsonga zake ndi chochitika chenicheni, makamaka cha utumiki wakumunda kapena umboni wa mwamwaŵi. Pamene itengedwa m’buku la Chidziŵitso, chochitikacho chingakhale ulendo wobwereza kapena Phunziro la Baibulo lapanyumba. Woyang’anira sukulu adzafuna kwambiri kuona mmene wophunzirayo adzathandizira mwininyumba kulingalira ndi kumvetsetsa nkhaniyo ndi tanthauzo la malemba. Woyang’anira sukulu adzasankha wothandiza mmodzi, koma mukhoza kugwiritsira ntchito wothandiza winanso. Chimene chiyenera kusamaliridwa kwambiri, si mkhalidwe wa chochitikacho, koma kugwiritsira ntchito nsonga kogwira mtima.
NKHANI NA. 4: Mphindi 5. Nkhaniyi idzapatsidwa kwa mbale kapena mlongo. Idzachokera m’buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Pamene ipatsidwa kwa mbale, iyenera kukhala nkhani yokambidwa kwa omvetsera onse. Kaŵirikaŵiri kudzakhala bwino kuti mbaleyo akonzekere nkhani yake akumalingalira za omvetsera ake m’Nyumba Yaufumu kotero kuti idzakhaledi yopatsa chidziŵitso ndi yopindulitsa omvetsera. Pamene ipatsidwa kwa mlongo, iyenera kuperekedwa mofanana ndi Nkhani Na. 3.
UPHUNGU NDI NDEMANGA: Pambuyo pa nkhani ya wophunzira aliyense, woyang’anira sukulu adzapereka uphungu wachindunji, osati kwenikweni motsatira mfundo za uphungu mmene zalondolerana pasilipi la Uphungu wa Kulankhula. M’malo mwake, ayenera kusamalira mbali zimene wophunzirayo afunikira kuwongolera. Ngati wophunzira amapeza “B” ndipo palibe pena pamene patsala “W” kapena “L,” pamenepo wopereka uphunguyo ayenera kulemba mzera wokweteza m’bokosi la mfundo ya kulankhula imene wophunzirayo ayenera kugwirirapo ntchito nthaŵi yotsatira, pamene adzalemba “B,” “W,” kapena “L.” Iye adzadziŵitsa wophunzirayo ponena za mfundo ya kulankhula imeneyi tsiku lomwelo ndipo adzaisonyeza pasilipi la Gawo la Wophunzira m’Sukulu Yautumiki (S-89) pokamba nkhani yotsatira. Okamba nkhani ayenera kukhala kutsogolo. Zimenezi zidzasungitsa nthaŵi ndi kukhozetsa woyang’anira sukulu kupereka uphungu wake mwachindunji kwa wophunzira aliyense. Ngati nthaŵi ilola pambuyo pa kupereka uphungu, phunguyo adzapereka ndemanga pa nsonga zopindulitsa zomwe sizinatchulidwe ndi ophunzirawo. Woyang’anira sukulu adzafunikira kusamala kuti asapitirire pa mphindi ziŵiri popereka uphungu ndi ndemanga zina zachidule pambuyo pankhani ya wophunzira aliyense. Ngati nsonga yofunika kwambiri yasiyidwa pa mfundo zazikulu za Baibulo, uphungu wamseri ungaperekedwe.
KUKONZEKERA NKHANI: Asanakonzekere nkhani yake, wophunzira ayenera kuŵerenga mosamalitsa mbali ya mu Bukhu Lolangiza la Sukulu yokhudza mfundo ya kulankhula imene adzagwirirapo ntchito. Ophunzira opatsidwa nkhani Na. 2 angasankhe mutu wogwirizana ndi chigawo cha Baibulo chimene adzaŵerenga. Nkhani zinazo zidzakambidwa mogwirizana ndi mutu wosonyezedwa pandandanda yosindikizidwa.
KUSUNGA NTHAŴI: Palibe nkhani imene iyenera kudya nthaŵi, ngakhalenso uphungu ndi ndemanga za phungu. Nkhani Na. 2 mpaka 4 ziyenera kuimitsidwa mwaluso pamene nthaŵi ikwana. Wopatsidwa thayo la kupereka chizindikiro cha kuima ayenera kutero nthaŵi itangokwana. Ngati abale opereka Nkhani Na. 1 ndi mfundo zazikulu za Baibulo adya nthaŵi, ayenera kupatsidwa uphungu wamseri. Onse ayenera kusamala kwambiri nthaŵi yawo. Programu yonse: Mphindi 45 kusiyapo nyimbo ndi pemphero.
KUPENDA KOLEMBA: Panthaŵi ndi nthaŵi padzakhala kupenda kolemba. Pokonzekera, pendani mfundo zogaŵiridwa ndi kutsiriza ndandanda ya kuŵerenga Baibulo. Baibulo lokha ndilo liyenera kugwiritsiridwa ntchito pa kupenda kumeneku kwa mphindi 25. Nthaŵi yotsalayo idzagwiritsiridwa ntchito kukambitsirana mafunso ndi mayankho. Wophunzira aliyense adzachonga pepala lake. Woyang’anira sukulu adzakambitsirana mayankho ndi omvetsera ndi kupereka chisamaliro pamafunso ovuta kwambiri, akumathandiza onse kumvetsetsa bwino mayankhowo. Ngati kusintha kukhala koyenera chifukwa cha mkhalidwe winawake wa pamalopo, kupenda kolemba kungachitidwe mlungu wotsatira m’malo mwa umene wasonyezedwa pandandanda.
MIPINGO YAIKULU: Mipingo yokhala ndi ophunzira olembetsa m’sukulu 50 kapena kuposapo ingalinganize magulu ena a ophunzira kukamba nkhani zondandalitsidwazo pamaso pa alangizi ena. Ndithudi, anthu osabatizidwa amene akukhala ndi moyo mogwirizana ndi makhalidwe Achikristu angalembetsenso m’sukulu ndi kupatsidwa nkhani.
OSAPEZEKAPO: Onse mumpingo angasonyeze chiyamikiro kaamba ka sukulu imeneyi mwa kuyesayesa kupezekapo paprogramu iliyonse ya mlungu ndi mlungu, mwa kukonzekera nkhani zawo bwino lomwe, ndiponso mwa kutengamo mbali m’mbali ya mafunso. Tikhulupirira kuti ophunzira onse adzasamalira nkhani zawo mwakhama. Ngati wophunzira sanapezekepo panthaŵi yomwe waikidwa, wavolontiya angaikambe, akumayesa mulimonse mmene angakhozere kupereka mfundo zoyenera panthaŵi yaifupiyo imene wauzidwa. Kapena woyang’anira sukulu angakambe nkhaniyo limodzi ndi kutengamo mbali koyenera kwa omvetsera.
NDANDANDA
Jan. 1 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 13 Mpaka 15
Na. 1: Mmene Chigwirizano Choona Chachikristu Chimapezedwera (uw-CN mas. 5-7 ndime 1-7)
Na. 2: Yeremiya 14:10-22
Na. 3: Kodi Ndani Yekha Amene Anayamba Wakhalako Asanakhale Munthu? (rs-CN tsa. 203, kamutu koyamba)
Na. 4: Kuchita Zinthu Zokhala ndi Chiyanjo cha Mulungu (gt-CN mutu. 83)
Jan. 8 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 16 Mpaka 19
Na. 1: Zinthu Zofunika Zobweretsa Chigwirizano Chachikristu (uw-CN tsa. 8 ndime 8 mpaka 8[3])
Na. 2: Yeremiya 18:1-17
Na. 3: Si Anthu Onse Abwino Amene Amapita Kumwamba (rs-CN tsa. 203, kamutu komaliza)
Na. 4: Thayo la Kukhala Wophunzira (gt-CN mutu 84)
Jan. 15 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 20 Mpaka 22
Na. 1: Zinthu Zinanso Zimene Zimagwirizanitsa Akristu (uw-CN tsa. 9 ndime 8[4] mpaka 9)
Na. 2: Yeremiya 20:1-13
Na. 3: Adamu Sanalonjezedwe Moyo wa Kumwamba (rs-CN tsa. 204, kamutu koyamba)
Na. 4: Peŵani Kudziyesa Nokha Wolungama, Ndipo Kondani Kudzichepetsa (gt-CN mutu 85)
Jan. 22 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 23 Mpaka 25
Na. 1: Peŵani Zisonkhezero Zogaŵanitsa (uw-CN mas. 10-11 ndime 10-12)
Na. 2: Yeremiya 23:16-32
Na. 3: Kukhala ndi Mtsogolo mwa Chimwemwe Sikumalira Kupita Kumwamba (rs-CN tsa. 204, kamutu kachiŵiri)
Na. 4: Mwana Woloŵerera ndi Atate Wake Wachikondi (gt-CN mutu 86 ndime 1-9)
Jan. 29 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 26 Mpaka 28
Na. 1: Mtundu wa Mulungu Amene Yehova Ali (uw-CN mas. 12-13 ndime 1-4)
Na. 2: Yeremiya 26:1-16
Na. 3: Yesu Sanatsegulire Njira Yakumwamba Aja Amene Anafa Imfa Yake Isanachitike (rs-CN tsa. 205, kamutu koyamba)
Na. 4: Linganizani Mtsogolo ndi Nzeru Yogwira Ntchito (gt-CN mutu 87)
Feb. 5 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 29 Mpaka 31
Na. 1: Tsanzirani Chitsanzo cha Chikondi cha Yehova (uw-CN mas. 14-15 ndime 5-7)
Na. 2: Yeremiya 31:27-40
Na. 3: Moyo wa Kumwamba Suli Chiyembekezo cha Akristu Onse (rs-CN tsa. 206)
Na. 4: Munthu Wachuma ndi Lazaro (gt-CN mutu 88 ndime 1-10)
Feb. 12 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 32 ndi 33
Na. 1: Phunzitsani Anthu Choonadi Chonena za Mulungu (uw-CN mas. 15-17 ndime. 8-11[2])
Na. 2: Yeremiya 33:1-3, 14-26
Na. 3: Malemba Achikristu Amasonyeza Chiyembekezo cha Madalitso a Dziko Lapansi (rs-CN tsa. 207, kamutu)
Na. 4: Zimene Fanizo la Munthu Wachuma ndi Lazaro Limatanthauza (gt-CN mutu 88 ndime 11-21)
Feb. 19 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 34 Mpaka 37
Na. 1: Pali Yehova Mmodzi Yekha (uw-CN mas. 17-18 ndime 11[3] mpaka 12)
Na. 2: Yeremiya 35:1-11, 17-19
Na. 3: Chiŵerengero cha Amene Adzalandira Mphotho Yakumwamba ndi Chifukwa Chake Chiŵerengerocho Sichili Chophiphiritsira (rs-CN tsa. 208, kamutu koyamba, ndi tsa. 209, kamutu koyamba)
Na. 4: Ulendo Wokasonyeza Chifundo ku Yudeya (gt-CN mutu 89)
Feb. 26 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 38 Mpaka 41
Na. 1: Chimene Kuyenda m’Dzina la Mulungu Kumatanthauza (uw-CN mas. 18-19 ndime 13-15)
Na. 2: Yeremiya 38:1-13
Na. 3: A 144,000 Sali Ayuda Akuthupi Okha (rs-CN tsa. 208, kamutu kachiŵiri)
Na. 4: Yesu Alankhula za Chiyembekezo cha Chiukiriro (gt-CN mutu 90)
Mar. 4 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 42 Mpaka 45
Na. 1: Thandizani Ena Kulandira Baibulo Monga Mawu a Mulungu (uw-CN mas. 20-2 ndime 1-6)
Na. 2: Yeremiya 43:1-13
Na. 3: Khamu Lalikulu Pamaso pa Mpando Wachifumu wa Mulungu, Koma Osati Kumwamba (rs-CN tsa. 209, kamutu kachiŵiri)
Na. 4: Yesu Aukitsa Lazaro (gt-CN mutu 91)
Mar. 11 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 46 Mpaka 48
Na. 1: Ŵerengani Baibulo Masiku Onse (uw-CN mas. 23-5 ndime 7-11)
Na. 2: Yeremiya 48:1-15
Na. 3: Mathayo Akumwamba a a 144,000 (rs-CN tsa. 210, kamutu koyamba)
Na. 4: Sonyezani Chiyamikiro Kaamba ka Ubwino wa Mulungu (gt-CN mutu 92)
Mar. 18 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 49 ndi 50
Na. 1: Phunzirani Kuti Mudziŵe za Yehova (uw-CN mas. 25-6 ndime 12 mpaka 12[1])
Na. 2: Yeremiya 49:1-11, 15-18
Na. 3: Baibulo Limasonyeza Kuti Akufa Samamva Ululu (rs-CN tsa. 144, kamutu koyamba ndi kachiŵiri)
Na. 4: Pamene Mwana wa Munthu Avumbulidwa (gt-CN mutu 93)
Mar. 25 Kuŵerenga Baibulo: Yeremiya 51 ndi 52
Na. 1: Atumiki Otumikira Amachita Ntchito Yofunika (om-CN mutu 6)
Na. 2: Yeremiya 51:41-57
Na. 3: Baibulo Limasonyeza Kuti Abwino ndi Oipa Omwe Amapita ku Helo pa Imfa (rs-CN tsa. 145, kamutu koyamba mpaka kachitatu)
Na. 4: Kufunika kwa Pemphero ndi Kudzichepetsa (gt-CN mutu 94)
Apr. 1 Kuŵerenga Baibulo: Maliro 1 ndi 2
Na. 1: Chifuno cha Nyumba Yaufumu ndi Ntchito Yake (om-CN tsa. 60 ndime 1-tsa. 64 ndime 1)
Na. 2: Maliro 2:13-22
Na. 3: Otembenuza Baibulo Amachititsa Chisokonezo Ponena za Helo (rs-CN tsa. 146, kamutu koyamba)
Na. 4: Maphunziro pa Chisudzulo ndi Chikondi cha pa Ana (gt-CN mutu 95)
Apr. 8 Kuŵerenga Baibulo: Maliro 3 Mpaka 5
Na. 1: Kupindula ndi Misonkhano Yachikristu (om-CN tsa. 64 ndime 2-tsa. 69 ndime 1)
Na. 2: Maliro 5:1-22
Na. 3: Oipa Amalangidwa Kwamuyaya Koma Osati Kuzunzidwa Kwamuyaya (rs-CN tsa. 146, kamutu kachiŵiri)
Na. 4: Yesu ndi Woweruza Wachichepere Wachuma (gt-CN mutu 96)
Apr. 15 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 1 Mpaka 4
Na. 1: Chifuno cha Msonkhano Wautumiki ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki (om-CN tsa. 69 ndime 2-tsa. 74 ndime 2)
Na. 2: Ezekieli 3:16-27
Na. 3: Tanthauzo la Chizunzo Chamuyaya Chotchulidwa m’Chivumbulutso (rs-CN tsa. 147, kamutu)
Na. 4: Fanizo la Yesu la Munda Wampesa (gt-CN mutu 97)
Apr. 22 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 5 Mpaka 8
Na. 1: Sinkhasinkhani Mutu wa Baibulo ndi Mawu Apatsogolo ndi Apambuyo a Malemba (uw-CN tsa. 26 ndime 12[2] ndi 12[3])
Na. 2: Ezekieli 5:1-15
Na. 3: Kodi Gehena wa Moto Wotchulidwa ndi Yesu Nchiyani? (rs-CN tsa. 148, kamutu)
Na. 4: Yesu Akonzekeretsa Ophunzira Ake Kaamba ka Zimene Zidzachitika (gt-CN mutu 98)
Apr. 29 Kupenda Kolemba. Malizani Yeremiya 13 Mpaka Ezekieli 8
May 6 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 9 Mpaka 11
Na. 1: Gwiritsirani Ntchito Zimene Mumaphunzira ndi Kuzilankhula kwa Ena (uw-CN mas. 26-8 ndime 12[4] mpaka 13)
Na. 2: Ezekieli 9:1-11
Na. 3: Mulungu Amafuna Kuti Mukhale ndi Mtsogolo Mwachimwemwe (kl-CN mas. 6-7 ndime 1-5)
Na. 4: Yesu Abwezeretsa Mwana Wotayika wa Abrahamu (gt-CN mutu 99)
May 13 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 12 Mpaka 14
Na. 1: Zimene Aneneri Amanena za Yesu (uw-CN mas. 29-31 ndime 1-6)
Na. 2: Ezekieli 14:1-14
Na. 3: Moyo Wosatha m’Paradaiso—Si Loto Chabe (kl-CN mas. 7-9 ndime 6-10)
Na. 4: Fanizo la Ndalama (gt-CN mutu 100)
May 20 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 15 ndi 16
Na. 1: Samalirani Zitsanzo Zaulosi (uw-CN mas. 32-3 ndime 7 mpaka 8[2])
Na. 2: Ezekieli 16:46-63
Na. 3: Mmene Moyo Udzakhalira m’Paradaiso (kl-CN mas. 9-10 ndime 11-16)
Na. 4: Yesu Atetezera Mariya pa Chabwino Chimene Anachita (gt-CN mutu 101)
May 27 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 17 Mpaka 19
Na. 1: Mkulu wa Ansembe Wathu Anaphiphiritsiridwa (uw-CN tsa. 33 ndime 8[3] ndi 8[4])
Na. 2: Ezekieli 18:21-32
Na. 3: Chifukwa Chake Chidziŵitso Chonena za Mulungu Chili Chofunika Kwambiri (kl-CN mas. 10-11 ndime 17-19)
Na. 4: Kuloŵa m’Yerusalemu Kwachipambano kwa Kristu (gt-CN mutu 102)
June 3 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 20 Mpaka 21
Na. 1: Mmene Tingasonyezere Chikhulupiriro Chathu mwa Kristu (uw-CN mas. 33-7 ndime 9-14)
Na. 2: Ezekieli 21:18-32
Na. 3: Buku Limene Limavumbula Chidziŵitso Chonena za Mulungu (kl-CN mas. 12-13 ndime 1-6)
Na. 4: Yesu Adzudzula Amene Aipitsa Kachisi wa Mulungu (gt-CN mutu 103)
June 10 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 22 ndi 23
Na. 1: Kumvera Mulungu Kumapatsa Ufulu Weniweni (uw-CN mas. 38-9 ndime 1-5)
Na. 2: Ezekieli 22:17-31
Na. 3: Zimene Baibulo Limavumbula Ponena za Mulungu (kl-CN mas. 13-15 ndime 7-9)
Na. 4: Liwu la Mulungu Limveka Kachitatu (gt-CN mutu 104)
June 17 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 24 Mpaka 26
Na. 1: Kumene Kungapezeke Ufulu Weniweni Lerolino (uw-CN mas. 40-2 ndime 6-9)
Na. 2: Ezekieli 26:1-14
Na. 3: Chifukwa Chake Mungalikhulupirire Baibulo (kl-CN mas. 15-16 ndime 10-13)
Na. 4: Chimene Mtengo wa Mkuyu Wotembereredwa Umatanthauza (gt-CN mutu 105)
June 24 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 27 Mpaka 29
Na. 1: Ufulu Wakudziko Kwenikweni Uli Ukapolo (uw-CN mas. 42-3 ndime 10-12)
Na. 2: Ezekieli 29:1-16
Na. 3: Baibulo Lili Lolondola ndi Lodalirika (kl-CN tsa. 17 ndime. 14, 15)
Na. 4: Mmene Atsogoleri Achipembedzo Avumbulidwira (gt-CN mutu 106)
July 1 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 30 Mpaka 32
Na. 1: Mmene Tingadziŵire Mayanjano Oipa (uw-CN mas. 44-5 ndime 13, 14)
Na. 2: Ezekieli 31:1-14
Na. 3: Baibulo Lili Buku la Ulosi (kl-CN mas. 17-18 ndime 16-18)
Na. 4: Chimene Fanizo la Phwando la Ukwati Limatanthauza (gt-CN mutu 107)
July 8 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 33 ndi 34
Na. 1: Nkhani Yaikulu Imene Aliyense Ayenera Kuyang’anizana Nayo (uw-CN mas. 46-7 ndime 1-3)
Na. 2: Ezekieli 34:17-30
Na. 3: Maulosi a Baibulo Onena za Yesu (kl-CN mas. 18-21 ndime 19, 20)
Na. 4: Alephera Kumkola Yesu (gt-CN mutu 108)
July 15 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 35 Mpaka 37
Na. 1: Tsanzirani Chikhulupiriro cha Okhulupirika (uw-CN mas. 47-52 ndime 4-11)
Na. 2: Ezekieli 35:1-15
Na. 3: Khalani ndi Chilakolako cha Chidziŵitso Chonena za Mulungu (kl-CN mas. 21-2 ndime 21-3)
Na. 4: Yesu Adzudzula Adani Ake (gt-CN mutu 109)
July 22 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 38 ndi 39
Na. 1: Kulemekeza Yehova mwa Mayendedwe Athu (uw-CN mas. 52-4 ndime 12-15)
Na. 2: Ezekieli 38:1-4, 10-12, 18-23
Na. 3: Mulungu Woona ndi Dzina Lake (kl-CN mas. 23-4 ndime 1-5)
Na. 4: Yesu Amaliza Uminisitala Wake wa pa Kachisi (gt-CN mutu 110)
July 29 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 40 Mpaka 44
Na. 1: Zimene Kulola Kuipa kwa Mulungu Kumatiphunzitsa (uw-CN mas. 55-7 ndime 1-7)
Na. 2: Ezekieli 40:1-15
Na. 3: Chifukwa Chake Muyenera Kutchula Dzina la Mulungu (kl-CN mas. 24-5 ndime 6-8)
Na. 4: Yesu Apereka Chizindikiro cha Masiku Otsiriza (gt-CN mutu 111 ndime 1-11)
Aug. 5 Kuŵerenga Baibulo: Ezekieli 45 Mpaka 48
Na. 1: Kulani Mwauzimu ndi Makonzedwe a Phunziro Labuku Lampingo (om-CN tsa. 74 ndime 3-tsa. 77 ndime 1)
Na. 2: Ezekieli 47:1-12
Na. 3: Mmene Yehova Anakuzira Dzina Lake (kl-CN mas. 25-7 ndime 9-13)
Na. 4: Yesu Alongosola Zowonjezereka Ponena za Masiku Otsiriza (gt-CN mutu 111 ndime 12-19)
Aug. 12 Kuŵerenga Baibulo: Danieli 1 ndi 2
Na. 1: Zochitika Zomangirira Mwauzimu (om-CN tsa. 78 ndime 2-tsa. 81 ndime 2)
Na. 2: Danieli 2:31-45
Na. 3: Mikhalidwe ya Mulungu Woona (kl-CN mas. 27-8 ndime 14-16)
Na. 4: Anamwali Ochenjera ndi Opusa (gt-CN mutu 111 ndime 20-8)
Aug. 19 Kuŵerenga Baibulo: Danieli 3 ndi 4
Na. 1: Mulungu Alibe Chisalungamo (uw-CN mas. 58-61 ndime 8-16)
Na. 2: Danieli 3:16-30
Na. 3: Yehova Mulungu Ali Wachifundo ndi Wachisomo (kl-CN mas. 28-9 ndime 17-19)
Na. 4: Fanizo la Matalente (gt-CN mutu 111 ndime 29-37)
Aug. 26 Kupenda Kolemba. Malizani Ezekieli 9 Mpaka Danieli 4
Sept. 2 Kuŵerenga Baibulo: Danieli 5 ndi 6
Na. 1: Kanizani Mizimu Yoipa (uw-CN mas. 62-4 ndime 1-5)
Na. 2: Danieli 6:4-11, 16, 19-23
Na. 3: Yehova Sakwiya Msanga, Ali Wopanda Tsankhu, Ndipo Ali Wolungama (kl-CN tsa. 30 ndime 20, 21)
Na. 4: Pamene Kristu Afika m’Mphamvu ya Ufumu (gt-CN mutu 111 ndime 38-46)
Sept. 9 Kuŵerenga Baibulo: Danieli 7 ndi 8
Na. 1: Khalani Maso ndi Machenjera a Mdyerekezi (uw-CN mas. 64-7 ndime 6-12)
Na. 2: Danieli 7:2-14
Na. 3: Yehova Mulungu ndi Mmodzi (kl-CN mas. 30-1 ndime 22, 23)
Na. 4: Paskha Womaliza wa Yesu Wayandikira (gt-CN mutu 112)
Sept. 16 Kuŵerenga Baibulo: Danieli 9 ndi 10
Na. 1: Valani Zida Zonse za Mulungu (uw-CN mas. 67-9 ndime 13-15)
Na. 2: Danieli 9:20-27
Na. 3: Yesu Kristu Ndiye Kiyi ya Chidziŵitso Chonena za Mulungu (kl-CN mas. 32-3 ndime 1-3)
Na. 4: Yesu Apereka Phunziro la Kudzichepetsa (gt-CN mutu 113)
Sept. 23 Kuŵerenga Baibulo: Danieli 11 ndi 12
Na. 1: Aminisitala a Mbiri Yabwino Alondola Mapazi a Mbuye (om-CN tsa. 81 ndime 3-tsa. 84 ndime 1)
Na. 2: Danieli 12:1-13
Na. 3: Mesiya Wolonjezedwayo (kl-CN tsa. 33 ndime 4, 5)
Na. 4: Yesu Ayambitsa Chikumbutso (gt-CN mutu 114)
Sept. 30 Kuŵerenga Baibulo: Hoseya 1 Mpaka 5
Na. 1: Kulalikira ndi Ntchito Yotumidwa ndi Mulungu (om-CN tsa. 84 ndime 2-tsa. 88 ndime 2)
Na. 2: Hoseya 5:1-15
Na. 3: Mzera Wobadwira wa Yesu Umamsonyeza Kukhala Mesiya (kl-CN tsa. 34 ndime 6)
Na. 4: Yesu Aphunzitsa Moleza Mtima Ophunzira Ake za Chikondi ndi Kudzichepetsa (gt-CN mutu 115)
Oct. 7 Kuŵerenga Baibulo: Hoseya 6 Mpaka 10
Na. 1: Chidziŵitso, Chikhulupiriro, ndi Chiukiriro (uw-CN mas. 70-3 ndime 1-7)
Na. 2: Hoseya 8:1-14
Na. 3: Maulosi Okwaniritsidwa Amasonyeza Yesu Kukhala Mesiya (kl-CN mas. 34-6 ndime 7, 8)
Na. 4: Yesu Akonzekeretsa Atumwi za Kuchoka Kwake (gt-CN mutu 116 ndime 1-14)
Oct. 14 Kuŵerenga Baibulo: Hoseya 11 Mpaka 14
Na. 1: Chifuno cha Maulendo Obwereza (om-CN tsa. 88 ndime 3-tsa. 92 ndime 1)
Na. 2: Hoseya 11:1-12
Na. 3: Umboni Wina Wakuti Yesu Anali Mesiya (kl-CN tsa. 36 ndime 9)
Na. 4: Amene Ali Mabwenzi Enieni a Yesu (gt-CN mutu 116 ndime 15-25)
Oct. 21 Kuŵerenga Baibulo: Yoweli 1 Mpaka 3
Na. 1: Folani Gawo Lanu Mokwanira (om-CN tsa. 92 ndime 2-tsa. 97 ndime 1)
Na. 2: Yoweli 2:1-11, 28-32
Na. 3: Yehova Amachitira Umboni Mwana Wake (kl-CN tsa. 38 ndime 10, 11)
Na. 4: Yesu Akonzekeretsa Ophunzira Ake ndi Kuwalimbikitsa (gt-CN mutu 116 ndime 26-37)
Oct. 28 Kuŵerenga Baibulo: Amosi 1 Mpaka 5
Na. 1: Mmene Mpingo Umakulira (om-CN tsa. 97 ndime 2-tsa. 100 ndime 1)
Na. 2: Amosi 3:1-15
Na. 3: Kukhalako kwa Yesu Asanakhale Munthu (kl-CN tsa. 39 ndime 12-14)
Na. 4: Pemphero la Yesu Lotsiriza m’Chipinda Chapamwamba (gt-CN mutu 116 ndime 38-51)
Nov. 4 Kuŵerenga Baibulo: Amosi 6 Mpaka 9
Na. 1: Zimene Ziyenera Kulembedwa pa Lipoti Laumwini la Utumiki Wakumunda (om-CN tsa. 100 ndime 2-tsa. 104 ndime 1)
Na. 2: Amosi 8:1-14
Na. 3: Moyo wa Yesu pa Dziko Lapansi (kl-CN tsa. 40-1 ndime 15-17)
Na. 4: Ululu m’Munda (gt-CN mutu 117)
Nov. 11 Kuŵerenga Baibulo: Obadiya Mpaka Yona 4
Na. 1: Chifukwa Chake Timachitira Lipoti Utumiki Wathu Wakumunda (om-CN tsa. 104 ndime 2-tsa. 109 ndime 2)
Na. 2: Yona 3:10; 4:1-11
Na. 3: Yesu Ali Wamoyo Ndipo Akulamulira Monga Mfumu (kl-CN mas. 41-2 ndime 18-20)
Na. 4: Kuperekedwa ndi Kugwidwa kwa Yesu (gt-CN mutu 118)
Nov. 18 Kuŵerenga Baibulo: Mika 1 Mpaka 4
Na. 1: Kodi Mungafutukule Uminisitala Wanu? (om-CN tsa. 110 ndime 1-tsa. 114 ndime 2)
Na. 2: Mika 4:1-12
Na. 3: Kulambira Kumene Mulungu Amakuvomereza (kl-CN mas. 43-5 ndime 1-5)
Na. 4: Yesu Akuchitidwa Mwankhanza ndi Kuzengedwa Mlandu mwa Njira Yakuswa Lamulo (gt-CN mutu 119)
Nov. 25 Kuŵerenga Baibulo: Mika 5 Mpaka 7
Na. 1: Mathayo a Utumiki—Kodi Ndani Ali Woyeneretsedwa? (om-CN tsa. 115 ndime 1-tsa. 118)
Na. 2: Mika 6:1-16
Na. 3: Kuchita Chifuniro cha Mulungu (kl-CN tsa. 46-7 ndime 6-10)
Na. 4: Kuwopa Munthu Kuchititsa Petro Kukana Kristu (gt-CN mutu 120)
Dec. 2 Kuŵerenga Baibulo: Nahumu 1 Mpaka 3
Na. 1: Mmene Uminisitalawo Umachirikizidwira (om-CN tsa. 119 ndime 1-tsa. 120 ndime 2)
Na. 2: Nahumu 1:2-14
Na. 3: Lambirani Mulungu mwa Njira Yake (kl-CN tsa. 48 ndime 11-13)
Na. 4: Yesu Alankhula Choonadi Molimba Mtima Pamaso pa Sanhedrin ndi Pilato (gt-CN mutu 121)
Dec. 9 Kuŵerenga Baibulo: Habakuku 1 Mpaka 3
Na. 1: Kusamalira Zosoŵa za Mpingo (om-CN tsa. 121 ndime 1-tsa. 123 ndime 2)
Na. 2: Habakuku 1:12–2:8
Na. 3: Peŵani Kuchimwira Mulungu (kl-CN mas. 49-50 ndime 14-17)
Na. 4: Onse Aŵiri Pilato ndi Herode Alephera Kupeza Chifukwa mwa Yesu (gt-CN mutu 122)
Dec. 16 Kuŵerenga Baibulo: Zefaniya 1 Mpaka 3
Na. 1: Kusamalira Bwino Ndalama (om-CN tsa. 124 ndime 1-tsa. 126)
Na. 2: Zefaniya 1:7-18
Na. 3: Sungani Miyezo Yapamwamba ya Mulungu (kl-CN mas. 50-1 ndime 18, 19)
Na. 4: Chifukwa Chake Yesu Anatchedwa “Munthuyu” (gt-CN mutu 123)
Dec. 23 Kuŵerenga Baibulo: Hagai 1 ndi 2
Na. 1: Kumamatira ku Miyezo Yolungama ya Yehova (om-CN tsa. 127 ndime 1-tsa. 129 ndime 1)
Na. 2: Hagai 2:6-19
Na. 3: Lambirani Yehova ndi Moyo Wonse (kl-CN mas. 51-2 ndime 20-2)
No. 4: Chimene Pilato Anawopera Yesu (gt-CN mutu 124)
Dec. 30 Kupenda Kolemba. Malizani Danieli 5 Mpaka Hagai 2