Nyimbo 131
Kumamatira kwa Yehova Mulungu Wathu
1. Ife a “nyumba” ya M’lungu timtumikira;
Timasunga kudzipereka kwapadera.
Tatopa ndi milungu ya mitunduyi.
Timamatira Ya; timutumikire.
Asonkhezere cho’nadi mumtimamo.
2. Zinthu za lonjezo, zimene ananena,
Zikhala zowona—chitsenderezo chitha!
Ufumu womadza udzathetsa nkhondo.
Timamatirabe; tiwonjeze mbiri.
Ndi Mulungu wathu; adzetsa mtendere.
3. Bukhu la chowonadi tiliŵerengedi.
Timamamatira Ya ndi kumvera Mawu.
Tifuna kumkonda ndi kumtumikira.
Chifuno chake tichikhulupilire
Kulambira kwake kuli kofunika.