Nyimbo 124
Chipatso cha Kudziletsa
1. Mkristu tchinjiriza moyo;
Khala wolimbatu.
Yesetsani kudziletsa,
Mudzapambanatu.
2. Monga tisonyezeratu
Chikondi ndi nzeru,
Tisonyeze kudziletsa
Ngatitu Mulungu.
3. Matupi asamagonja;
Kuzikhumbo zathu.
Kutinso tipulumuke,
Timadziletsatu.
4. Tikhalenso odekhatu
Ngati tizunzidwa;
Imanibe nji kwa M’lungu
Ndi kuchilungamo.