Kodi Mukufesa Mooloŵa Manja?
1 Pali mawu onena kuti: “Ukalimbikira pachinthu, umapindulapo zochuluka.” Zimenezi nzoona makamaka m’kulambira kwathu. Ngati titayirapo nthaŵi yochuluka ndi zoyesayesa pa kukonzekera misonkhano, kulalikira uthenga wa Ufumu, ndi kusonyeza chikondi kwa abale athu, tidzapindula zochuluka pa kukula kwauzimu. Tikalephera kutero sitidzapindulanso kanthu. Ngati tili ouma dzanja kapena a mitima iŵiri m’zimene tichita, kodi tingayembekezeredi zotulukapo zokhutiritsa?
2 Mtumwi Paulo analongosola bwino lomwe lamulo la mkhalidwe pa 2 Akorinto 9:6 kuti: “Iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa mooloŵa manja, mooloŵa manjanso adzatuta.” Kodi mukufesa mooloŵa manja?
3 Phunziro la Baibulo Laumwini: Kuti tikhale atumiki obala zipatso, choyamba tifunikira kufesa mooloŵa manja m’phunziro lathu laumwini. Tiyenera kukhala ndi njala yaikulu yauzimu. (Sal. 119:97, 105; Mat. 5:3) Pokhala otsenderezedwa ndi zosamalira za moyo za tsiku ndi tsiku, pamafunikira kuyesayesa kosamalitsa kuti tikulitse kuzindikira kwenikweni kwa zosoŵa zathu zauzimu. Kwa ochuluka a ife, pamafunikira “kuwombola nthaŵi yoyenera.” (Aef. 5:16, NW) Ena amalinganiza kudzuka mmamaŵa masiku ena kuti achite phunziro laumwini. Ena apatula madzulo ena kaamba ka chifuno chimenecho. Kodi ndimotani mmene timatutira mooloŵa manja? Timakhala ndi chikhulupiriro champhamvu koposerapo, chiyembekezo choŵalirapo, ndi mkhalidwe wa maganizo wachisangalalo ndi wabwinopo.—Aroma 10:17; 15:4; 1 Pet. 1:13.
4 Misonkhano ya Mpingo: Pa Salmo 122:1, Davide anati: “Ndinakondwera mmene ananena nane, Tiyeni ku nyumba ya Yehova.” Kodi nanunso mumamva motero? Kufesa mooloŵa manja kumatanthauza kufika mokhazikika pamisonkhano yathu isanu ya mlungu ndi mlungu. Tsimikizirani m’maganizo kuti simudzalola kusacha bwino kwa kunja kukudodometsani. Kaŵirikaŵiri, pamene tilaka zododometsa zochuluka, timapezanso madalitso ochuluka.
5 Fikani mwamsanga ndipo musafulumire kupita pambuyo pake kuti mugaŵane m’makambitsirano olimbikitsana ndi abale anu. Futukulani mayanjano anu kuphatikizamo ambiri osiyanasiyana malinga ndi mmene mungakhozere. Konzekerani bwino lomwe Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi misonkhano ina kotero kuti mufese mooloŵa manja mwa kupereka ndemanga pamene mukhala ndi mwaŵi. Mwa ‘kuthirira’ ena kwaulere pamisonkhano, nanunso ‘mudzathiriridwa’ kwaulere.—Miy. 11:25.
6 Utumiki Wakumunda: Mwinamwake palibe kulikonse kumene lamulo la mkhalidwe limeneli la kufesa mooloŵa manja limagwira ntchito kwambiri kuposa mu utumiki wakumunda. Pamene titayirapo nthaŵi yochuluka, ndi pamenenso timakhala okhoza kututa zokumana nazo zokondweretsa, maulendo obwereza opindulitsa, ndi maphunziro a Baibulo obala zipatso.
7 Kufesa mooloŵa manja mu utumiki wakumunda kumaloŵetsamo mkhalidwe wake ndi kuchuluka kwake. Chithandizo chabwino koposa pa kuwongolera mkhalidwe wa utumiki wathu ndicho buku la Kukambitsirana. Masamba 9-15 amandandalika mawu oyamba oposa 40 a nkhani 18 zothandiza kudzutsa chikondwerero pamakomo. Ngati mupeza chikondwerero, tsimikizirani kulemba zimenezo kotero kuti mukabwerere ndi kututa chipatso cha kufesa kwanu. Mwachionekere kuyesayesa kwanu kudzatsogolera ku phunziro la Baibulo, ndipo mungaphunzitse munthu wina kufesa mooloŵa manja.
8 Ngati tifesa mooloŵa manja, tingayembekezere madalitso aakulu kwa Yehova.—Mal. 3:10.