Kufesa Mowoloŵa Manja Kumabweretsa Madalitso Ochuluka
1 Tonsefe timayembekeza kukwaniritsidwa kwa malonjezo akuluakulu a m’Mawu a Mulungu. Ngakhale pakalipano, Yehova amatipatsa madalitso ambiri amene amawonjezera chimwemwe m’moyo wathu. Komabe mmene timapindulira zimadalira kwambiri pa khama lathu. Malinga n’kulemba kwa mtumwi Paulo, “iye wakufesa mowoloŵa manja, mowoloŵa manjanso adzatuta.” (2 Akor. 9:6) Onani mbali ziŵiri zimene mfundoyi imagwira ntchito.
2 Utumiki Wathu: Kuuza anthu uthenga wabwino nthaŵi iliyonse imene tingathe kuchitira umboni, kumabweretsa mapindu ambiri. (Miy. 3:27, 28) Ubwino wake, anthu ambiri akufesa mowoloŵa manja mwa kuwonjezera zimene amachita mu utumiki, komanso kuchita upainiya wothandiza kapena wokhazikika. Tonse tingafese mowoloŵa manja mwa kuyesetsa kupita kukakulitsa chidwi cha anthu amene tinapeza ndiponso mwa kuwapempha kuphunzira nawo Baibulo ngati papezeka mwayi wochita zimenezo. (Aroma 12:11) Kuyesetsa kuchita zimenezi kumabweretsa zotsatira zosangalatsa ndiponso chimwemwe chochuluka mu utumiki wathu.
3 Kuchirikiza Ufumu wa Mulungu: Paulo ananena mawu ake onena za ‘kufesa mowoloŵa manja’ pankhani yopereka zinthu zakuthupi. (2 Akor. 9:6, 7, 11, 13) Masiku ano, pali zambiri zimene tingachite pochirikiza Ufumu wa Mulungu. Tingagwire nawo ntchito ndiponso tingapereke zinthu zakuthupi. Tingathandize nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Tikhozanso kudzipereka kuthandiza nawo ntchito yoyeretsa ndi kukonza nyumba za kulambira koona zimenezi. Komanso, tingapereke ndalama zogulira zinthu zofunika pampingo wathu komanso za ntchito ya padziko lonse yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. Tonse tikachita mbali yathu, timasangalala kwambiri kuona Yehova akudalitsa kwambiri ntchitoyi, imene walamula kuti igwiridwe.—Mal. 3:10; Luka 6:38.
4 Mawu a Mulungu amatilimbikitsa ‘kuchita zabwino, kukhala ochuluka mu ntchito zabwino, kukhala owoloŵa manja, okonzeka kugaŵira ena.’ Tikamvera langizo limeneli, timapeza madalitso ochuluka pakalipano. Komanso timakhala ‘tikudzikundikira tokha maziko okoma ku nyengo ikudzayo ndi moyo weniweni’ ukubwerawo.—1 Tim. 6:18, 19, NW.