Mbiri Yateokratiki
Haiti: Chiwonjezeko cha 12 peresenti m’February chinadzetsa chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 9,115. Mpambo wa misonkhano yadera ya 1994 unakhala ndi opezekapo 15,824, ndipo 252 anabatizidwa.
Japan: February unali mwezi wozizira kwambiri wokhala ndi chipale chambiri. Komabe, chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 188,844 chinafikiridwa. Panalinso ziŵerengero zapamwamba zatsopano m’maulendo obwereza, maphunziro a Baibulo, ndi apainiya okhazikika.
Philippines: Lipoti la February linasonyeza chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 117,519. Maphunziro a Baibulo anapitirira pa 100,000 kwa nthaŵi yoyamba, okwanira 100,146 akumachitiridwa lipoti. Magazini ogaŵiridwa anapyola pa 100,000 kuposa November wa 1993 chifukwa cha kusinthira kumaonekedwe achibadwa a magazini.