Funafunani Amene Ali Ophunzitsika
1 “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa ine koma ngati Atate wondituma ine amkoka iye.” (Yoh. 6:44) Yehova, amene amasanthula mtima, adzafupa aja amene ali ophunzitsika ndi kuchita zimene akuphunzira. (Yer. 17:10; Yoh. 6:45) Tili ndi mwaŵi wa kukhala antchito anzake pofunafuna ofatsa amene akulakalaka dziko latsopano.—Sal. 37:11; 1 Akor. 3:9.
2 Yesu analongosola ophunzira ake kukhala “asodzi a anthu.” (Mat. 4:19) Pamene kuli kwakuti ntchito imeneyo nthaŵi zina imafuna kuyesetsa kwambiri, zotulukapo zake zabwino zimadzetsa chikhutiro chachikulu. M’malo molimbikira kupeza phindu laumwini, ife kwenikweni tikupulumutsa “nsomba” ku chiwonongeko chotsimikizirika. Msodzi waluso amadziŵa zochita kuti nsomba zidyere. Momwemonso, tiyenera kupereka uthenga wa Ufumu mwa njira yokopa imene idzachititsa chidwi omvetsera athu. Makamaka zimenezi nzofunika pamene tikupanga maulendo obwereza. Kodi tinganenenji?
3 Ngati munthu anachita chidwi ndi nkhani za mu “Nsanja ya Olonda” zonena za chipembedzo, mukhoza kunena kuti:
◼ “Tsiku lija tinakambitsirana za chifukwa chimene anthu ambiri samafunira kukambitsirana za chipembedzo. Kodi zimenezo sizimakudabwitsani, popeza kuti anansi athu ochuluka amati ndi Akristu? Mwinamwake mumadabwa kuti nchifukwa ninji chipembedzo chili nkhani yobutsa magaŵano ndi mkangano kwambiri chotero.” Yembekezerani yankho. Tsegulani patsamba 83 m’buku la Kukambitsirana, ndipo kambitsiranani mfundo zingapo pamutu wakuti “Kodi Nchifukwa Ninji Pali Zipembedzo Zambiri Motero?”
4 Mwina mungagwiritsire ntchito njira yotsatirayi yofanana ndi imeneyo kuyambitsa kukambitsirana pankhani ya chipembedzo:
◼ “Kodi ilipo njira imene tingadziŵire kuti tili ndi chipembedzo choona? [Yembekezerani yankho.] Popeza kuti pali zipembedzo zambiri zosiyanasiyana, anthu ambiri ali osokonezeka ndi osadziŵa chochita.” Tsegulani patsamba 89 ndi 90 m’buku la Kukambitsirana, pamene pakuyankha funso lakuti “Kodi munthu angadziŵe motani chimene chili chipembedzo chowona?” Kambani mwachidule pa funso la nambala 5, “Kodi ziŵalo zake zimakondanadi?” Fotokozani mmene angaphunzirire zambiri kupyolera m’phunziro Labaibulo laumwini.
5 Ngati mwininyumba anaoneka kukhala woda nkhaŵa ndi mikhalidwe ya dziko, mwina mungafune kuyesa zotsatirazi:
◼ “Mwachionekere inu muli ndi nkhaŵa ponena za mikhalidwe yoipa imene tiyenera kulimbana nayo m’moyo ndi posamalira mabanja athu. Baibulo limapereka lonjezo labwino kwambiri limene Mulungu adzalikwaniritsa patsogolopa.” Ŵerengani Miyambo 2:21, 22, ndi kufotokoza mmene Yehova walonjezera dziko la mtendere wosatha.
6 Popanga maulendo obwereza mkupiti wapadera wa Uthenga wa Ufumu utayamba, chonde musaiŵale kusiya kope la Uthenga wa Ufumu kwa mwini nyumba amene alibe. Zimene munganene pamaulendo obwereza potsatira Uthenga wa Ufumu umene munagaŵira zidzafotokozedwa mu Utumiki Wathu Waufumu wa May.
7 Popeza kuti Mawu a Mulungu “ali ndi mphamvu,” tiyenera kuwagwiritsira ntchito m’maulaliki athu. (Aheb. 4:12, NW) Musaiŵale kulimbikitsa mwininyumba kuŵerenga Baibulo mwa iye mwini. (Yerekezerani ndi Mac. 17:11.) Ngati tichita mbali yathu mwakhama, Yehova adzadalitsa kuyesayesa kwathu.