Kodi Zikumbutso za Yehova Zikutitsitsimutsa Mwauzimu?
1 Wamasalmo anatamanda Yehova, kuti: “Ndilingalira mboni [“zikumbutso,” NW ] zanu.” (Sal. 119:99) Liwu Lachihebri lotanthauza “zikumbutso” limasonyeza lingaliro lakuti Yehova amatikumbutsa zonenedwa m’malamulo ake, malangizo ake, maweruzo ake, miyezo yake, ndi zitsogozo zake. Ngati tizilabadira, zidzatitsitsimutsa mwauzimu ndi kutipatsa chimwemwe.—Sal. 119:2.
2 Monga anthu a Yehova, timalandira chilangizo ndi uphungu nthaŵi zonse. Zambiri tinazimvapo kale. Ngakhale kuti timayamikira chilimbikitso chimenechi, timakonda kuiŵala. (Yak. 1:25) Moleza mtima, Yehova amapereka zikumbutso zachikondi. Mtumwi Petro analemba zina za zikumbutso zimenezi kuti ‘atsitsimutse mtima wathu kuti tikumbukire malamulo a Ambuye.’—2 Pet. 3:1, 2.
3 Timakumbutsidwa mobwerezabwereza za kufunika kwa phunziro laumwini ndi kufika pamisonkhano. Zimenezi zimachitika chifukwa chakuti mbali zimenezi nzofunika kwambiri pa umoyo wathu wauzimu.—1 Tim. 4:15; Aheb. 10:24, 25.
4 Vuto lalikulu kwambiri kwa ena ndilo kukwaniritsa ntchito Yachikristu yolalikira. Ntchito imeneyi imafuna kuyesayesa, kulimba mtima, ndi khama. Ngakhale kuti imafuna zambiri kwa ife, imatithandiza ‘kuchirimika’ mwa ‘kuveka mapazi athu ndi makonzedwe a uthenga wabwino.’—Aef. 6:14, 15.
5 Utumiki wathu suyenera kusonkhezeredwa ndi chidziŵitso chabe cha zofuna za Yehova. Mtumwi Paulo akutikumbutsa kuti mtima ndiwo umapereka chisonkhezero chimene tifunikira cha ‘kulengeza poyera chipulumutso.’ (Aroma 10:10, NW ) Ngati tili ndi chikhulupiriro cholimba ndipo ngati mtima wathu ukonda zikumbutso za Yehova, tidzakakamizika kulankhula za kutamanda dzina lake.—Sal. 119:36, Mat. 12:34.
6 Pamene tilimbikira kuchita ntchito zabwino, moyenera timayembekezera kuti zimenezo zidzatipatsa chimwemwe. (Mlal. 2:10) Paulo akusonyeza kuti chimwemwe ndi chipatso cha mzimu wa Yehova, ndipo tiyenera kuyesayesa kuchisonyeza kwambiri. (Agal. 5:22) Petro anawonjezera kuti “changu chonse” chidzafupidwa ndi utumiki wobala zipatso, umene umatulutsa chimwemwe.—2 Pet. 1:5-8.
7 Pamene tayang’anizana ndi vuto, tiyenera kukumbukira kaimidwe kolimba ka atumwi pamene anati, “Sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:20) Timalimbikitsidwa kuchirimika pamene tikumbukira kuti ‘pochita ichi, tidzadzipulumutsa ife eni ndi iwo akumva ife.’—1 Tim. 4:16.
8 Sitimadandaula kapena kuipidwa chifukwa cholandira zikumbutso nthaŵi zonse. M’malo mwake, timayamikira kwambiri mapindu ake aakulu kopambana. (Sal. 119:129) M’nthaŵi zino zovuta, tikuthokoza Yehova kuti akutitumizirabe zikumbutso zotitsitsimutsa mwauzimu ndi zotisonkhezera kukhala achangu pa ntchito zabwino!—2 Pet. 1:12, 13.