Chititsani Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekera
1 Kumbukirani nthaŵi pamene munamva uthenga Waufumu kwa nthaŵi yoyamba. Mfundo zofeŵa za choonadi zinasonkhezera chikhumbo chanu cha kupeza chidziŵitso ndi kuzindikira. Posapita nthaŵi munaona kufunika kwa kusintha njira yanu ya moyo chifukwa njira za Yehova nzapamwamba kwambiri ndi zanu. (Yes. 55:8, 9) Munapita patsogolo, munapatulira moyo wanu, ndi kubatizidwa.
2 Ngakhale pambuyo pa kupita patsogolo mwauzimu, zifooko zofuna kugonjetsedwa zinalipobe. (Aroma 12:2) Mwinamwake munali kuwopa anthu, amene anakuchititsani kuzengereza kugaŵanamo mu utumiki wa m’munda. Mwinamwake munalikulephera kusonyeza chipatso cha mzimu wa Mulungu. M’malo mwa kubwevuka, munali wotsimikiza kupita patsogolo mwa kudziikira zonulirapo zateokrase.
3 Zaka zambiri zingakhale zitapitapo tsopano kuyambira pamene munadzipatulira. Pamene muyang’ana kumbuyo, kodi ndi kupita patsogolo kotani kumene mumakuona mwa inu mwini? Kodi mwafikira zonulirapo zanu zina? Kodi mukali ndi changu chimodzimodzi chimene ‘munali nacho pachiyambi’? (Aheb.3:14, NW) Timoteo anali kale Mkristu wokula msinkhu wokhala ndi chidziŵitso cha zaka zambiri pamene Paulo anamlimbikitsa kuti: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti [kupita kwako patsogolo, NW] kuonekere kwa onse.”—1 Tim. 4:15.
4 Kudzipenda Nkofunika: Pamene tilingalira za moyo wathu wakale, kodi timaona kuti tikali ndi zifooko zina zimene tinali nazo titangoyamba? Kodi talephera kufikira zonulirapo zina zimene tinaika? Ngati zili choncho, nchifukwa ninji? Ngakhale kuti tinali ndi zolinga zabwino, tingakhale titazengereza. Mwinamwake talola nkhaŵa za moyo kapena mavuto a dongosolo lino la zinthu kutibwevutsa.—Luka 17:28-30.
5 Pamene kuli kwakuti palibe zimene tingachite ponena za moyo wathu wakale, tingachitepodi kanthu ponena za mtsogolo. Tikhoza kudzifufuza moona mtima, kupeza pamene tikupereŵera, ndiyeno kuyesayesa mwamphamvu kuti tiwongolere. Tingafunikire kuwongolera pa kusonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu, zonga chiletso, chifatso, kapena kuleza mtima. (Agal.5:22, 23) Ngati tili ndi vuto la kusamvana ndi ena kapena kusagwirizana ndi akulu, nkofunika kuti tikulitse kudzichepetsa mtima.—Afil. 2:2, 3.
6 Kodi tingachititse kupita kwathu patsogolo kuonekera mwa kukalimira mwaŵi wa mautumiki? Mwa kuyesayesa kwambiri abale angathe kuyeneretsedwa monga atumiki otumikira kapena akulu. Ena a ife tingathe kulembetsa monga apainiya anthaŵi zonse. Kwa ena ambiri, upainiya wothandizira ungakhale chonulirapo chofikirika. Ena angamenyere kuwongolera mmene amachitira phunziro laumwini, kukhala otengamo mbali achangu kwambiri m’misonkhano ya mpingo, kapena kukhala ofalitsa a mumpingo obala zipatso kwambiri.
7 Komabe, zili kwa aliyense wa ife kudziŵa pamene tiyenera kupita patsogolo. Tingatsimikize kuti kuyesayesa kwathu koona mtima kuti “tipitirire kutsata ukulu msinkhu” kudzawonjezera kwambiri chimwemwe chathu ndi kutipanga kukhala ziŵalo za mpingo zobala zipatso kwambiri.—Aheb. 6:1.