Khalani a Mtima Wonse!
1 Tili ndi zifukwa zambiri zokhalira oyamikira kwa Yehova. Zimenezi zikuphatikizapo zinthu zimene anachita kale, zimene akuchita tsopano lino, ndi zimene adzatichitirabe mtsogolo. Kodi chiyamikiro chathu chiyenera kutisonkhezera kuchitanji? Salmo la Davide likuyankha kuti: “Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala mkamwa mwanga kosalekeza.”—Sal. 34:1.
2 Baibulo limasonyeza bwino lomwe kuti tikulamulidwa kulalikira. Imeneyi ndi ntchito imene timachita “mochokera mumtima, monga kwa [Yehova, NW].” (Akol. 3:23) Kodi tidzachita zotani mu utumiki ngati tilidi a mtima wonse? Pamene tilingalira za chikondi cha Yehova pa ife, moonadi mitima yathu imatisonkhezera kudzipereka pa kuuza ena za iye ndi zifuno zake zamtengo wapatali! Timasonkhezeredwa kuchita zimene tingathe.
3 Kungakhale kwanzeru kuyembekezera kuti munthu amene ali wamtima wonse amafuna kusumika maganizo ake pa utumiki wopatulika. Wamasalmo, amene mosakayikira analingalira motero, anati: “Ndikulemekezani kasanu ndi kaŵiri, tsiku limodzi.” (Sal. 119:164) Awo amene ali ndi malingaliro onga a wamasalmo amayesetsa kugwiritsira ntchito mipata ina kuti alemekeze Yehova. Monga mmene mikhalidwe yawo ingalolere, amatumikira mwachangu malinga ndi kukhoza kwawo.
4 Tazingidwa ndi Mipata Yolemekezera Yehova: Sititofunikira kuyembekezera mpaka pamene tigaŵanamo m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba kuti tilalikire uthenga wabwino. Anzathu akuntchito, anzathu akusukulu, achibale, ndi odziŵana nawo onse ayenera kumva uthenga wa Ufumu. Pamene tili paulendo, tingayambitse makambitsirano amene angatsogolere ku kuchitira umboni kwa antchito a mu hotela, antchito a mu lesitilanti, antchito a pomwetsera galimoto mafuta, kapena oyendetsa mateksi. Pamene tili panyumba, tingachitire umboni kwa anansi kapena odzagulitsa zinthu. Ngati tagonekedwa m’chipatala, pali manesi, madokotala, ndi odwala ena amene tingalalikire mwamwaŵi.
5 Umboni Wamwamwaŵi Umakhala ndi Zotulukapo: Tsiku lina Mboni ziŵiri zinali kuyenda m’paki ndipo zinayambitsa makambitsirano ndi mwamuna wina amene anali kuwongola miyendo ndi mwana wake. M’kupita kwa nthaŵi iyeyo ndi mkazi wake analandira choonadi. Mwamunayo pambuyo pake anaulula kuti kanthaŵi kochepa chabe asanakumane ndi Mboni ziŵirizo kwa nthaŵi yoyamba, anali atapemphera kwa Mulungu, akumapempha kuti, ‘Ngati muliko, chonde ndiloleni ndikudziŵeni.’ Iye amaona zimene zinachitika m’paki kukhala yankho la Yehova la pemphero lake.
6 Awo amene ali a mtima wonse pa chikhumbo chawo cha kuthandiza ena mwauzimu amakhala ndi chimwemwe chachikulu. Iwo amadziŵa kuti utumiki wotere, “ndi mtima wangwiro,” umakondweretsa Yehova.—1 Mbiri 28:9.