Uthenga Wabwino pa Internet
M’nyengo yathu ino ya sayansi, anthu ena amapeza chidziŵitso pakompyuta, kuphatikizapo Internet. Choncho Sosaite yaika pa Internet chidziŵitso china cholongosoka chonena za zikhulupiriro ndi ntchito za Mboni za Yehova.
Keyala yathu ya pa Internet ndi: http://www.watchtower.org ndipo ili ndi mndandanda wa matrakiti, mabrosha, ndi nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! m’Chijeremani, m’Chingelezi, m’Chirasha, m’Chispanya, m’Chitchaina (Chofeŵa), ndi m’zinenero zinanso. Zofalitsa zimene zili pa Internet zimenezi zilimo kale m’mipingo ndipo zikugwiritsiridwa ntchito mu utumiki. Cholinga cha Web yathu pa Internet si chotulutsa mabuku atsopano, koma kugaŵira chidziŵitso kwa anthu ngakhale pakompyuta. Sikofunika kuti munthu aliyense payekha alembe chidziŵitso nkuchiika pa Internet, chonena za Mboni za Yehova, ntchito yathu, kapena zikhulupiriro zathu. Zimene taikamo kale zikupereka chidziŵitso cholongosoka kwa aliyense amene akuchifuna.
Ngakhale kuti Web yathu siitha kutumiza mauthenga a E-mail pakompyuta, taikamo makeyala a papositi a nthambi zapadziko lonse. Choncho anthu angalembe makalata kuti adziŵe zambiri kapena kuti athandizidwe paokha ndi Mboni za kwawoko. Masukani kuuzako ena alionse za keyala ya Internet imene taperekayo, amene angakonde kuyamba kuphunzira choonadi cha Baibulo mwa njira ya Internet.