Bokosi la Mafunso
◼ Kodi tingachitenji kuti tithandizire misonkhano yathu kukhala yopindulitsa kwambiri?
Ena akhoza kumaganiza kuti akulu ndi atumiki otumikira ndiwo ayenera kuchititsa kuti misonkhano ya mpingo iziyenda bwino chifukwa chakuti ndiwo amatsogolera ndi kusamalira mbali zambiri. Komatu, tonsefe pali zimene tingachite patokha kuthandizira misonkhano kukhala yosangalatsa ndi yopindulitsa. Tingathandizire kuti misonkhano ikhale yopindulitsa kwambiri mwa kutsatira njira khumi zotsatira:
Konzekerani pasadakhale. Pamene takonzekera bwino, misonkhano imakopa chidwi chathu. Tonsefe tikachita zomwezo, misonkhano imakhala yosangalatsa kwambiri ndi yolimbikitsa kwambiri. Pezekanipo nthaŵi zonse. Ngati papezeka anthu ochuluka zimalimbikitsa aliyense wopezekapo, kulimbitsa chiyamikiro chathu ponena za kufunika kwa kupezeka pamisonkhano. Fikani panthaŵi yake. Ngati misonkhano imayamba ife titakhala kale pansi, tingaimbe nawo nyimbo yotsegulira ndi kukhala nawo pa pemphero lotsegulira, motero kulandira mapindu okwanira pamsonkhano. Bwerani muli okonzeka bwino. Mwa kubweretsa Baibulo lathu ndi zofalitsa zogwiritsira ntchito pamsonkhano, tingamatsatire ndi kumvetsa bwino zomwe zikufotokozedwa. Peŵani zochenjenetsa. Tingamamvetsere bwino titakhala kutsogolo. Kunong’onezana ndi kupitapita kuchimbudzi kumatichenjenetsa ifeyo ndiponso ena. Tenganimo mbali. Pamene ambiri tikweza manja ndi kuyankhapo, ambiri amalimbikitsidwa ndi kumangiriridwa ndi mawu a chikhulupiriro. Yankhani mwachidule. Zimenezi zimapatsa ambiri mpata woyankhapo. Tiyenera kungoyankha zimene zili m’nkhani yomwe tikuphunzira. Kwaniritsani magawo anu. Ngati muli wophunzira m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki kapena muli ndi mbali mu Msonkhano Wautumiki, konzekerani bwino, yesezani pasadakhale, ndipo musayese kuphonya. Yamikirani omwe ali ndi mbali. Uzani ena kuti mukuwayamikira kwambiri pakhama lawo. Zimenezo zimawalimbikitsa ndi kuwasonkhezera kuchita bwino koposa mtsogolo. Limbikitsanani. Kupatsana moni mwaubwenzi ndi kukambitsirana zinthu zomangirira msonkhano usanayambe ndi pambuyo pake kumawonjezera chisangalalo ndi mapindu omwe timapeza mwa kupezeka pamisonkhano.