Kodi Muli ndi “Munga m’Thupi”?
1 Timafunitsitsadi kugwira ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino. Komabe, ambiri mwa abale ndi alongo athu okondedwa zimawavuta kuchita mbali yawo mokwanira chifukwa cha matenda aakulu kapena kufooka, ndiye zimawalepheretsa kuchita zambiri monga mmene akanafunira. Kwa iwowo, zingakhale zowafooketsa kwambiri, makamaka akamaona anzawo ali okangalika mu utumiki.—1 Akor. 9:16.
2 Yemwe Tingatsanzire: Mtumwi Paulo anafunikira kupirira “munga m’thupi.” Katatu konse anapempha Yehova kumchotsera chopinga chosautsa chimenechi, chomwe anachitcha “mngelo wa Satana” yemwe ankangomzunza. Komabe, Paulo analimbikirabe mu utumiki wake mosasamala zimenezo. Iye sankangodzimvera chisoni kapena kumangodandaula nthaŵi zonse. Ankachita zimene anali kukhoza. Chomwe chinamthandiza kupirira linali lonjezo la Mulungu lakuti: “Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa [“ionekera,” NW], m’ufoko.” Kufooka kwa Paulo kunasanduka nyonga pamene analizoloŵera vuto lake mwa kudalira Yehova ndi mzimu woyera kuti apirire.—2 Akor. 12:7-10.
3 Mmene Mungapiririre: Kodi Kufooka kwa thupi kumakulepheretsani kuchita zambiri potumikira Mulungu? Ngati zili choncho, tengerani maganizo a Paulo. Ngakhale kuti matenda kapena kufooka kwanu kulibe mankhwala ochiritsiratu m’dongosolo lino la zinthu, mungadalire Yehova kwambiri, yemwe amadziŵa zosoŵa zanu, yemwenso amapatsa “mphamvu yoposa yaumunthu.” (2 Akor. 4:7, NW) Landirani chithandizo chimene a mumpingo mwanu angakupatseni, osamadzipatula. (Miy. 18:1) Ngati zimakuvutani kuchita nawo ntchito ya kukhomo ndi khomo, funafunani njira zabwino zochitira umboni wamwamwayi kapena wa patelefoni.
4 Ngakhale kuti munga m’thupi umakulepheretsani kuchita zimene mungathe kuchita mu utumiki, musamamve ngati simukuchita chilichonse. Mofanana ndi Paulo, inunso ‘mungachitire umboni uthenga wabwino wa chisomo cha Mulungu,’ mukumatero mogwirizana ndi nyonga yanu ndi mmenenso mikhalidwe yanu ingakulolereni. (Mac. 20:24) Mmene mukuyesetsa kutsiriza utumiki wanu, dziŵani kuti Yehova akukondwera nazo.—Aheb. 6:10.