Aitaneni Kuti Afike
1 Chiitano choperekedwa zaka mazana apitawo tsopano chikuperekedwa m’mayiko 233 padziko lonse chakuti: “Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, . . . ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” (Yes. 2:3) Kusonyeza anthu gulu la Yehova ndi imodzi mwa njira zabwino kwambiri zimene tingathandizire anthu kupita patsogolo mwauzimu komwe kumatsogolera kumoyo wosatha.
2 Ofalitsa ena amachedwa kuitanira anthu ku Nyumba ya Ufumu mpaka ataona kuti afika patali paphunziro lawo la Baibulo lapanyumba. Komabe, nthaŵi zina anthu amayamba kumafika pamisonkhano ya mpingo ngakhale asanayambitsidwe phunziro la Baibulo. Tisachedwe kupereka chiitano kwa anthu ndi kuwalimbikitsa kufika pamisonkhano.
3 Zoyenera Kuchita: Onetsetsani kuti mwauza anthu za misonkhano yakwanu. Tchulani kuti misonkhano ndi yaulere ndiponso sayendetsapo mbale ya zopereka. Longosolani mmene misonkhano imachitikira. Auzeni kuti ndi kosi yeniyeni ya Baibulo ndipo pamakhala zophunzirira kuti onse ayendere limodzi ndi wochititsa. Auzeni za kusiyana mitundu kwa opezekapo komanso moyo wawo, ophunzira ndi osaphunzira, olemera ndi osauka. Tchulaninso kuti ofikapo ndi anthu a m’dera lomwelo ndipo ana a zaka zilizonse ndi aufulu kufikapo. Tiyenera kuitana awo amene timachita nawo phunziro, tikumawathandiza mwanjira ina iliyonse kuti afikepo.
4 Chimodzi mwa zinthu zolembedwa kumapeto m’Baibulo ndi chiitano chogwira mtima cholandira zogaŵira za Yehova zopatsa moyo chakuti: “Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. . . . Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chiv. 22:17) Palibe chingafanane ndi kuitana ena kufika pamisonkhano yathu.
5 Mwaulosi Yesaya 60:8 amanena za zikwi mazanamazana za atamandi atsopano amene panopo akufika mumpingo wa anthu a Mulungu monga nkhunda zomwe ‘zikuuluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda ku mazenera awo.’ Tonse tiyenera kuitanira achatsopano kumisonkhano ndi kuwalandira bwino. Mwa njira imeneyi, tidzakhala ogwirizana ndi Yehova pamene akufulumiza ntchito yosonkhanitsa.—Yes. 60:22.