Mmene Tingakulitsire Luso la Kukambirana
1 Tanthauzo lina la liwu lakuti “kukambirana” ndi “kulankhula ndi munthu wina n’cholinga chosonkhezera zochita zake kapena malingaliro ake.” Kuti mukulitse kugwira mtima kwanu mu utumiki, mufunika kukulitsa luso la kukambirana ndi anthu amene mumakumana nawo. (Mac. 17:2-4) Koma kodi mungalikulitse motani luso limeneli?
2 Limayamba ndi Kusinkhasinkha: Pophunzira choonadi cha Baibulo, n’kothandiza kusinkhasinkha za nkhaniyo. Ngati mbali zina za nkhaniyo zili zovutirapo kuzimva, khalani ndi nthaŵi yofufuza ndi kusinkhasinkha pa zimene mwapeza. Khalani ndi cholinga choti mumvetsetse bwino osati kokha zimene zafotokozedwazo komanso zifukwa za m’Malemba zimene zapangitsa kuti afotokoze motero.
3 Limafunanso Kukonzekera Utumiki: Lingalirani za mmene mungafotokozere anthu osiyanasiyana choonadi. Konzani funso lopangitsa munthu kuganiza kuti mudzutse chidwi. Pezani mmene mungaloŵetserepo mfundo ya m’Malemba ndi kukambirana zimenezo. Lingalirani za zitsutso zimene anthu anganene, ndipo ganizirani mmene mungakawayankhire. Gwirani mfundo m’buku limene mukugaŵira imene ingathandize kwambiri pa kukambiranako.
4 Tsatirani Chitsanzo cha Yesu: Yesu anaika chitsanzo chabwino kwambiri cha kukambirana za m’Malemba mogwira mtima. Kuti muone mmene anaphunzitsira, onani nkhani ya pa Luka 10:25-37. Onani njira izi: (1) Ayankheni anthu mafunso awo mogwiritsa ntchito Malemba. (2) Apempheni kuti anene malingaliro awo, ndipo ayamikireni pamene anena ndemanga zanzeru. (3) Onetsetsani kuti Malemba akugwirizana ndi mafunso. (4) Gwiritsani ntchito fanizo losangalatsa kuti mumveketse kwambiri mfundo yeniyeni ya yankholo.—Onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1986, tsamba 27-8 ndime 8-10.
5 Gwiritsani Ntchito Chida Chimene Tinapatsidwa: Buku la Kukambitsirana za m’Malemba linasindikizidwa monga buku la malangizo a mu utumiki wakumunda. Mawu ake oyamba, mayankho kwa oimitsa kukambirana, ndi mfundo zokambirana zimatithandiza kukulitsa luso la kukambirana. Buku la Kukambitsirana ndi chida chofunika kwambiri chimene tiyenera kuyenda nacho mu utumiki nthaŵi zonse ndipo tiyenera kuligwiritsa ntchito pamene tikukambirana za m’Baibulo. Pendani masamba 7-8 a bukuli kuti muone mmene mungaligwiritsire ntchito bwino.
6 Kukulitsa luso lanu la kukambirana kudzawonjezera luso lanu mu ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa. Izi zidzadzetsa madalitso ochuluka kwa inu ndi kwa anthu amene mumakumana nawo mu utumiki.