Kodi Mukugwiritsa Ntchito Buku la Kukambitsirana?
1. Kodi mtumwi Paulo ndi Yesu anaphunzitsa motani anthu ena?
1 Mtumwi Paulo ankayesetsa ‘kukambirana ndi anthu kuchokera m’Malemba.’ (Mac. 17:2, 3; 18:19) Mwa kuchita zimenezi iye anatsanzira Yesu amene nthawi zonse anagwiritsa ntchito Malemba komanso mafanizo amene anathandiza anthu kumvetsa cholinga cha Mulungu. (Mat. 12:1-12) Buku la Kukambitsirana za m’Malemba linakonzedwa kuti litithandize kuchita zimenezi.
2. Kodi tingagwiritsire ntchito bwanji buku la Kukambitsirana pokonzekera ulaliki wogwira mtima?
2 Kukonzekera Mawu Oyamba Ogwira Mtima: M’buku la Kukambitsirana za m’Malemba patsamba 9 mpaka 15 pali mawu oyamba ogwira mtima amene tinganene kwa anthu. Kuphunzira komanso kugwiritsa ntchito mawu amenewa m’dera limene limalalikidwa pafupipafupi kudzakuthandizani kuti muzisinthasintha ulaliki wanu. Ndipo kudzakuthandizaninso kuyamba ulaliki wanu ndi mawu ogwira mtima. Mungawerenge mawu oyamba kuchokera m’bukulo pamene mukuchita ulaliki wa pa foni kapena pamene mukulankhula pa makina olankhulirana amene amakhala panja pa nyumba zovuta kulowamo.
3. Kodi patsamba 16 mpaka 24 m’buku la Kukambitsirana pali mfundo zotani zimene zingatithandize muutumiki?
3 Zimene Tinganene kwa Anthu Amene Akukana Kuwalalikira: Tiyenera kukonzekera kulalikira anthu otsutsa amene angapezeke m’gawo lathu. Musanayambe kulalikira pezani nthawi yoonanso masamba 16 mpaka 21 a bukuli kuti mudziwe zimene munganene kwa anthuwo. Ganizirani ngati eninyumba ena angakhale Abuda, Ahindu, Ayuda kapena Asilamu. Ngati zili choncho mfundo zimene zili patsamba 21 mpaka 24 zikhoza kukuthandizani.
4. Kodi tingagwiritsire ntchito bwanji buku la Kukambitsirana pofotokoza nkhani kapena kuyankha mafunso ovuta?
4 Kuyankha Mafunso: Buku la Kukambitsirana lingatithandizenso pofotokoza nkhani kapena kuyankha mafunso ovuta. Mukhoza kumuuza munthuyo kuti mukufuna kumuuza mfundo ina yochititsa chidwi pa nkhaniyo ndipo tulutsani buku la Kukambitsirana. Popeza mitu yake anaisanja motsatira zilembo za afabeti, pezani mutu umene mukuganiza kuti ungakhale ndi yankho limene mukufuna. Yang’anani mwamsanga mafunso amene alembedwa ndi inki yakuda kwambiri. Ngati simukupeza zimene mukufuna, yang’anani zosonyezera zimene zili kumapeto kwa bukuli. Mukapeza mfundo zothandiza muwerengereni kuchokera m’bukulo. Ndipo ngati mukukambirana lemba, mungapeze mfundo zofunika patsamba 445 pa kamutu kakuti “Malemba Amene Kawirikawiri Agwiritsiridwa Ntchito Molakwa.”
5. Fotokozani ubwino wina wa buku la Kukambitsirana.
5 Ubwino Wina wa Bukuli: Anthu ena amayenda ndi buku la Kukambitsirana kuntchito kapena kusukulu pofuna kuti azitha kuyankha mafunso monga akuti, ‘N’chifukwa chiyani simukondwerera maholide?’ Achinyamata apeza mfundo zothandiza pokonzekera kulemba ntchito ya kusukulu pa mitu yakuti, “Chilengedwe” ndi “Chisinthiko.” Kodi mwina mukufuna kukaona wodwala kapena munthu amene waferedwa? Mfundo zomwe zili pamutu wakuti “Chilimbikitso” zingakuthandizeni kupeza Malemba olimbikitsa. Buku la Kukambitsirana lilinso ndi mfundo zothandiza pokonzekera nkhani komanso misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda.
6. Kodi cholinga chathu polalikira ndi chiyani?
6 Tikamalalikira cholinga chathu si kuwina mikangano kapena kungouza ena mfundo zinazake. M’malo mwake timafuna kukambirana nawo Malemba mwaluso. Tikamagwiritsa ntchito bwino buku la Kukambitsirana tidzasonyeza kuti tikudziyang’anira tokha mosalekeza, ndi kusamalanso zimene timaphunzitsa.—1 Tim. 4:16.