Kodi N’chiyani Chimene Chingatithandize Kukhala Ochilimika M’chikhulupiriro?
1 Chiyambireni kugwirizana ndi gulu la Yehova, kupita kwathu patsogolo kwauzimu kwatipatsa chimwemwe! Komabe, kuti tikhalebe ‘ozika mizu, omangirika, ndi okhazikika m’chikhulupiriro’ n’kofunika kupitiriza kukula mwauzimu. (Akol. 2:6, 7) Pamene kuli kwakuti anthu ambiri apita patsogolo mwauzimu, ena asiyana nacho choonadi chifukwa cholephera kukhala ‘ochilimika m’chikhulupiriro.’ (1 Akor. 16:13) Koma titha kupeŵa zimenezi kutichitikira. Tingapeŵe bwanji?
2 Kuchita Zauzimu Nthaŵi Zonse: Khalani ndi chizoloŵezi chabwino chauzimu mu gulu la Yehova. Kuno n’kumene zosoŵa zathu zauzimu amazisamalira bwino zedi. Misonkhano ya mpingo, yadera, ndi yachigawo imatilimbikitsa kukula ndi kukhazikika kwambiri mwauzimu, malinga ngati tisonkhana nawo nthaŵi zonse n’cholinga choti tipindule. (Aheb. 10:24, 25) Chizoloŵezi choŵerenga Baibulo, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, komanso mabuku amene amafotokoza chakudya chotafuna cha Mawu a Mulungu chidzapangitsa mizu yathu yauzimu kuzika pansi komanso kukhazikika. (Aheb. 5:14) Kukhala ndi zolinga zaumwini zauzimu ndi kugwira ntchito mwakhama kuti muzikwaniritse kudzakubweretseraninso mapindu anthaŵi zonse.—Afil. 3:16.
3 Kuthandizidwa ndi Anthu Achikulire Mwauzimu: Futukulani mayanjano mwa kucheza ndi anthu achikulire mwauzimu mumpingo. Dziŵani akulu, popeza ndiwo kwenikweni angatilimbikitse. (1 Ates. 2:11, 12) Landirani uphungu uliwonse kapena malingaliro amene angapereke. (Aef. 4:11-16) Atumiki otumikira amafunanso kuthandiza ena kuti akhale ochilimika m’chikhulupiriro, choncho funani chilimbikitso kwa abale ameneŵa.
4 Kodi mukufuna kukuthandizani mu utumiki? Lankhulani ndi akulu, kuwapempha kuti akuthandizeni. Mwinamwake angakuikeni papologalamu ya Apainiya Athandiza Ena. Kodi mwangobatizidwa kumene? Kuphunzira buku la Olinganizidwa ndi kugwiritsa ntchito za m’menemo kudzakusonkhezerani kupita patsogolo kufikira uchikulire wauzimu. Kodi ndinu kholo? Pitirizani kulimbitsa uzimu wa ana anu.—Aef. 6:4.
5 Mwa kukhala ozika mizu ndi okhazikika m’chikhulupiriro, timakhala pa ubwenzi weniweni ndi Yehova komanso mayanjano abwino ndi abale athu. Izi zimatithandiza kupherera ziukiro za Satana, ndipo zimalimbitsa chiyembekezo chathu cha m’tsogolo mosatha.—1 Pet. 5:9, 10.