Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/06 tsamba 8
  • Thandizo Lopezekeratu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thandizo Lopezekeratu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Mpingo Wachikristu—Gwero la Chitonthozo
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Pemphani Thandizo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 2/06 tsamba 8

Thandizo Lopezekeratu

1. Kodi n’chiyani chingachititse kuti munthu afooke mwauzimu?

1 Anna ndi mlongo amene anali ndi mwamuna wosakhulupirira komanso ntchito yopanikiza. Nthawi zambiri zinali zomuvuta kupita ku misonkhano yachikristu, kupita ku ulaliki, ndi kuwerenga Mawu a Mulungu. Ngakhale kuti anali kukondabe Yehova, iye anafika posiya kulalikira. Komabe chosangalatsa n’chakuti akulu anali kumudera nkhawa ndipo anamuthandiza mwauzimu.

2. Kodi Akristu onse angasonyeze bwanji kuti alidi thandizo lopezekeratu?

2 Munthu amene amalolera kulandira thandizo lauzimu loperekedwa kudzera mu mpingo wachikristu amasonyeza kuti amadalira Yehova. Potsanzira chikondi chimene Yesu Kristu anali kusonyeza, akulu mu mpingo amafufuza mwayi wolimbikitsira ndi kuthandizira anthu amene akukumana ndi mavuto pochita zinthu zauzimu. (1 Ates. 5:14) Nthawi zambiri, chimene chimafunikira ndi mawu olimbikitsa ochokera m’Malemba. Udindo wothandiza anthu amene afooka kwa kanthawi si wa akulu okha ayi, koma wa Akristu onse. N’zosakayikitsa kuti tonsefe taonapo mmene “mawu oyenera a pa nthawi yake” amalimbikitsira.—Miy. 25:11; Yes. 35:3, 4.

3, 4. Kodi n’chiyani chimene chimafunikira kuti tithandize ena, ndipo tingachite zimenezi motani?

3 Yambani Ndinuyo: Kusonyeza chikondi anthu amene akufunikira thandizo kumafuna kuti tiyambe ndifeyo kuwachitira ntchito zabwino, ndi kuwathandiza ndi mtima wonse. Pamene Jonatani anazindikira kuti Davide anali m’mavuto, iye “ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, nam’limbitsa dzanja lake.” (1 Sam. 23:15, 16) Khalani wokoma mtima pothandiza ena. Ngati mumafuniradi ena zabwino, mawu anu angakhaledi olimbikitsa. Ndiponso, Yesu anapereka chitsanzo chomveka bwino, chosonyeza kuti timafunikira kukhala ndi khama komanso cholinga chabwino kuti tibweze mbale wathu ku zoipa. (Luka 15:4) Ngati tili ofunitsitsa kuthandiza munthu wina, tidzapitirizabe kuthandiza munthuyo ngakhale ngati sakusintha mwamsanga.

4 Kumakhaladi kolimbikitsa ngati tiyamba ndifeyo kupempha ena kuti tiyende nawo mu utumiki. Mwachitsanzo, tingapemphe anthu a m’phunziro lathu la buku. Tikamathandiza mtumiki wa Yehova mnzathu kulalikira, tingagwiritse ntchito mwayi umenewu kulimbikitsa dzanja lake. Nthawi zosangalatsa zotere zoyendera limodzi mu utumiki wa Yehova zimathandiza kwambiri anthu amene akuyambanso kuchita bwino pa zinthu zauzimu.

5. Kodi ndi thandizo lotani limene akulu nthawi zina angapereke?

5 Makonzedwe Achikondi: Anthu amene anasiya kulalikira ndi kusonkhana ndi mpingo kwa kanthawi angafunikire thandizo lowonjezereka kuti alimbitse chikhulupiriro chawo. Mwina angafunikire kuyambanso phunziro pogwiritsa ntchito buku monga lakuti Lambirani Mulungu Woona Yekha, Yandikirani kwa Yehova kapena Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Pachifukwa chakuti munthuyo ndi wobatizidwa kale, sikofunikira kuti phunzirolo lipitirirebe kwa nthawi yaitali. Komiti ya Utumiki ya Mpingo iyenera kufufuza anthu amene angafunikire makonzedwe amenewa.—Onani Mabokosi a Mafunso a mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 1998 ndi November 2000.

6. Kodi mlongo wina analimbikitsidwa motani kuti ayambe kuchitanso bwino mwauzimu?

6 Anna, mlongo amene tamutchula koyambirira, anathokoza kwambiri akulu atam’pempha kuti mlongo wina wokhwima mwauzimu azichita naye phunziro la Baibulo. Atangophunzira kanayi kokha, Anna anayambanso kuyandikira kwa Yehova. Anayambanso kufika ku misonkhano ya mpingo ndipo chikhumbo chake chofuna kulemekeza Yehova Mulungu mwa kulalikira chinayambiranso. Mlongo wokhwima uja anathandizanso Anna mu utumiki wa kumunda mwa kupita naye ku maphunziro ake ena a Baibulo kufikira pamene anatha kulalikira khomo ndi khomo. Anna, anangofunikira thandizo lachikondi kuti ayambenso kuchita bwino mwauzimu.

7. Kodi timakhala ndi madalitso otani ngati tilimbikitsa ena mwauzimu?

7 Kulimbikitsa anthu amene akufunikira thandizo kumadzetsa madalitso kwa onse. Amene akuthandizidwa amasangalala akayambanso kuyandikira kwa Yehova ndi kuchita zinthu pamodzi ndi gulu Lake. Akulu amakondwa kuona munthu amene anali wofooka akuchitanso bwino. (Luka 15:5, 6) Pamene onse akusonyezana chikondi mwa njira imeneyi, mpingo umakhala wogwirizana kwambiri. (Akol. 3:12-14) Tilidi ndi zifukwa zabwino zotsanzira Yehova, thandizo lopezekeratu!—Aef. 5:1.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena