NKHANI YOPHUNZIRA 36
NYIMBO NA. 103 Abusa Ndi Mphatso
‘Itanani Akulu’
“Aitane akulu a mpingo.”—YAK. 5:14.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi, tiona kufunika kopempha akulu mumpingo kuti atithandize.
1. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amaona kuti nkhosa zake ndi zamtengo wapatali?
YEHOVA amaona kuti nkhosa zake ndi zamtengo wapatali. Iye anazigula ndi magazi a Yesu ndipo anapereka udindo kwa akulu mumpingo kuti azizisamalira. (Mac. 20:28) Mulungu amafuna kuti nkhosa zake zizisamalidwa mwachikondi. Motsogoleredwa ndi Khristu, akulu amalimbikitsa abale ndi alongo omwe ndi nkhosa komanso kuwathandiza kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova.—Yes. 32:1, 2.
2. Kodi Yehova amachita chidwi kwambiri ndi ndani? (Ezekieli 34:15, 16)
2 Yehova amakonda nkhosa zake zonse koma amasamalira mwapadera zomwe zikufunika thandizo. Amagwiritsa ntchito akulu posamalira atumiki ake omwe akudwala mwauzimu. (Werengani Ezekieli 34:15, 16.) Komabe iye amafuna kuti tonsefe tizipempha thandizo pa nthawi imene tikufunikira thandizolo. Kuwonjezera pa kupempha Yehova, tizipemphanso thandizo kwa “abusa ndi aphunzitsi” mumpingo.—Aef. 4:11, 12.
3. Kodi kuganizira udindo wa akulu n’kothandiza bwanji?
3 Munkhaniyi, tiona zimene Mulungu anakonza zoti akulu azithandiza atumiki ake omwe afooka. Tionanso nthawi imene tingapemphe akulu kuti atithandize, chifukwa chake tiyenera kuchita zimenezo, komanso mmene iwo angatithandizire. Ngakhale ubwenzi wathu ndi Yehova utakhala wolimba, mfundozi zingatithandize kuti tiziyamikira zimene Mulungu anakonza zoti azitithandiza ndipo tsiku lina zingadzapulumutse moyo wathu.
KODI NDI PA NTHAWI ITI POMWE ‘TINGAITANE AKULU’?
4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti matenda otchulidwa pa Yakobo 5:14-16, 19, 20 ndi matenda auzimu? (Onaninso zithunzi.)
4 Pofotokoza zimene Mulungu anakonza zoti akulu azitithandiza tikafooka, Yakobo anafunsa kuti: “Kodi pali aliyense amene akudwala pakati panu? Aitane akulu a mpingo.” (Werengani Yakobo 5:14-16, 19, 20.) Apa Yakobo akunena za matenda auzimu. Mwachitsanzo, wodwalayo akuuzidwa kuti aitane akulu a mpingo, osati dokotala. Matendawo akuoneka kuti ndi auzimu. Tikutero chifukwa wodwalayo kuti achire, akufunika kukhululukidwa machimo ake. Zina zomwe zimafunika kuti munthu wodwala mwauzimu achire, zikufanana ndi zimene zimafunika pa matenda enieni. Mwachitsanzo, tikadwala timakafotokozera dokotala mmene tikumvera komanso kutsatira malangizo ake. Tikadwalanso mwauzimu tiyenera kukauza akulu vuto limene tili nalo, n’kutsatira malangizo a m’Malemba omwe angatipatse.
Tikadwala timakaonana ndi dokotala. Tiyeneranso kuonana ndi akulu tikadwala mwauzimu (Onani ndime 4)
5. Kodi tingadziwe bwanji kuti tayamba kudwala mwauzimu?
5 Pa Yakobo chaputala 5, timalimbikitsidwa kuti tikazindikira kuti ubwenzi wathu ndi Yehova wayamba kusokonekera, tizikauza akulu. Zingakhaletu bwino kulandira thandizo tisanachite zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Tizidzifufuza moona mtima chifukwa Malemba amachenjeza kuti tingadzipusitse n’kumaona ngati ubwenzi wathu ndi Yehova uli bwino. (Yak. 1:22) Izi zinachitikiranso Akhristu ena a ku Sade, ndipo Yesu anawachenjeza kuti Yehova sankasangalala nawo. (Chiv. 3:1, 2) Njira imodzi imene tingadziwire mmene moyo wathu wauzimu ulili ndi kuyerekezera changu chathu ndi mmene tinkachitira m’mbuyomu. (Chiv. 2:4, 5) Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimakondabe kuwerenga Baibulo komanso kuganizira zimene ndawerenga? Kodi ndimakonzekerabe misonkhano komanso kupezekapo nthawi zonse? Kodi ndimagwirabe mwakhama ntchito yolalikira? Kodi ndinasiya kuganizira kwambiri za zinthu zosangalatsa komanso ndalama?’ Ngati yankho lathu pa funso lililonse ndi lakuti ayi, zingasonyeze kuti tafooka mwauzimu. Ngati sitingachitepo kanthu mwamsanga, zinthu zingaipe kwambiri. Choncho ngati sitingathane ndi vutolo patokha kapenanso ngati tachita kale zinthu zosemphana ndi mfundo za Mulungu, tizipempha akulu kuti atithandize.
6. Kodi munthu amene wachita tchimo lalikulu ayenera kuchita chiyani?
6 Munthu akachita tchimo lomwe lingachititse kuti achotsedwe, ayenera kufotokozera akulu. (1 Akor. 5:11-13) Aliyense amene wachita tchimo lalikulu amayenera kuthandizidwa kuti akonzenso ubwenzi wake ndi Yehova. Kuti Yehova atikhululukire pogwiritsa ntchito dipo, tiyenera ‘kuchita zinthu zosonyeza kulapa.’ (Mac. 26:20) Zinthu zimenezo zikuphatikizapo kukafotokozera akulu.
7. Kodi ndi anthu enanso ati amene amafunika kuthandizidwa ndi akulu?
7 Sikuti akulu amangothandiza anthu amene achita machimo aakulu okha, koma amathandizanso anthu amene afooka mwauzimu. (Mac. 20:35) Mwachitsanzo, mwina mukulephera kulimbana ndi zilakolako zanu zoipa. Zingakhale zovuta kwambiri ngati musanaphunzire choonadi munkagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza ubongo, kuonera zolaula kapenanso kuchita chiwerewere. Musamalimbane ndi mavutowa panokha. Mungafotokozere mkulu yemwe angamvetsere nkhawa zanu, kukupatsani malangizo othandiza komanso kukutsimikizirani kuti mungathe kusangalatsa Yehova. (Mlal. 4:12) Mukakhumudwa chifukwa chakuti mukulimbanabe ndi zilakolako zoipa, akulu adzakukumbutsani kuti umenewo ndi umboni wakuti mumaona kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ndi wofunika ndipo mumapewa mtima wodzidalira.—1 Akor. 10:12.
8. Kodi ndi machimo ati omwe sitingafunike kukafotokozera akulu?
8 Si chilichonse chomwe talakwitsa chimene timafunika kukafotokozera akulu. Tiyerekeze kuti munakwiya kapena munalankhula mawu opweteka kwa Mkhristu mnzanu. Apa mungachite bwino kutsatira malangizo a Yesu omwe angathandize kuti mukhalenso pamtendere ndi mnzanuyo. (Mat. 5:23, 24) Mungafufuzenso m’mabuku athu zokhudza makhalidwe monga kufatsa, kuleza mtima ndi kudziletsa kuti mudzawasonyeze pa nthawi ina. Komabe ngati mukulephera kuthetsa vuto lanulo mungapemphe mkulu kuti akuthandizeni. Polembera Akhristu a ku Filipi, mtumwi Paulo anapempha m’bale wina, yemwe sanamutchule dzina, kuti athandize Eodiya ndi Suntuke kuti athetse kusamvana kwawo. Inunso mkulu wamumpingo mwanu akhoza kukuthandizani.—Afil. 4:2, 3.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUITANA AKULU?
9. N’chifukwa chiyani sitiyenera kulola manyazi kutilepheretsa kupempha thandizo kwa akulu? (Miyambo 28:13)
9 Pamafunika chikhulupiriro komanso kulimba mtima kuti tipemphe thandizo tikachita tchimo lalikulu kapena tikamalephera kulimbana ndi zinthu zoipa zimene timalakalaka. Manyazi asamatilepheretse kupempha akulu kuti atithandize. Tikutero chifukwa Yehova anatipatsa akulu kuti azitithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. Choncho tikamawafotokozera mavuto athu timasonyeza kuti timamudalira komanso kumumvera. Timazindikira kuti timafunikira thandizo lake kuti tipitirize kuchita zabwino. (Sal. 94:18) Ndipo tikachimwa, Mulungu angatichitire chifundo ngati talapa n’kusiya zoipazo.—Werengani Miyambo 28:13.
10. Kodi chingachitike n’chiyani tikabisa tchimo lathu?
10 Tikafotokozera akulu za tchimo lathu, Yehova amatikhululukira ndipo tingakhalenso naye pa ubwenzi wabwino. Koma tikabisa, mavuto athu amakula. Davide atabisa machimo ake ubwenzi wake ndi Yehova unasokonekera, anali ndi nkhawa komanso anadwala. (Sal. 32:3-5) Mofanana ndi matenda enieni, matenda auzimu amapitirizabe kukula ngati munthu sanalandire thandizo loyenera. Yehova amamvetsa zimenezi, choncho amatipempha kuti ‘tikambirane naye’ pogwiritsa ntchito njira imene anakhazikitsa yotithandiza kukhalanso naye pa ubwenzi.—Yes. 1:5, 6, 18.
11. Kodi kubisa machimo kungakhudze bwanji ena?
11 Kubisa machimo kungakhudzenso anthu ena. Kungachititse kuti mzimu wa Mulungu usamagwire bwino ntchito mumpingo, ndipo izi zingasokoneze mtendere. (Aef. 4:30) Tikadziwanso kuti munthu wina wachita tchimo lalikulu tizimulimbikitsa kuti akauze akulu.a Tikabisa tchimo la munthu wina timakhala ndi mlandu kwa Yehova. (Lev. 5:1) Kukonda Yehova kuzitilimbikitsa kuti tiziuza akulu. Tikatero timathandiza kuti mpingo ukhale woyera komanso kuti munthu wochimwayo akonze ubwenzi wake ndi Yehova.
MMENE AKULU AMATITHANDIZIRA
12. Kodi akulu amatithandiza bwanji?
12 Akulu amalangizidwa kuti azithandiza anthu amene afooka mwauzimu. (1 Ates. 5:14) Mukalakwitsa zinazake, angakufunseni mafunso owathandiza kudziwa maganizo anu ndi mmene mukumvera. (Miy. 20:5) N’zoona kuti si zophweka kufotokozera akulu momasuka, mwina chifukwa cha manyazi, chikhalidwe chanu kapenanso chibadwa chanu. Koma mungawathandize kwambiri ngati mutafotokoza bwino. Musamadere nkhawa kuti zimene mungalankhule zingaoneke ngati ndinu munthu ‘wosaganiza bwino.’ (Yobu 6:3) M’malo moweruza mwamsanga, akuluwo adzayesetsa kukumvetserani kuti adziwe nkhani yonse asanakupatseni malangizo. (Miy. 18:13) Iwo amazindikira kuti kuweta nkhosa kumafuna nthawi yokwanira, choncho sangayembekezere kuti vuto lanulo litha mutangokambirana ulendo umodzi.
13. Kodi mapemphero a akulu komanso malangizo awo a m’Malemba zingatithandize bwanji? (Onaninso zithunzi.)
13 Pokambirana nanu, akulu sadzakuchititsani kuti muzidziimba mlandu kwambiri. M’malomwake, adzakupemphererani. Mungadabwe ndi mmene pemphero lawo lingakuthandizireni chifukwa “limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.” Thandizo lawo limaphatikizapo ‘kukupakani mafuta m’dzina la Yehova.’ (Yak. 5:14-16) “Mafuta” amenewa ndi choonadi cha m’Baibulo. Akulu angagwiritse ntchito mwaluso Baibulo kuti akulimbikitseni ndi kukuthandizani kuti mukonzenso ubwenzi wanu ndi Yehova. (Yes. 57:18) Malangizo awo angakulimbikitseni kuti mukhale ndi mtima wofuna kuchita zoyenera. Kudzera mwa akuluwo, mungamve Yehova akukuuzani kuti: “Njira ndi iyi. Yendani mʼnjira imeneyi.”—Yes. 30:21.
Akulu amagwiritsa ntchito Baibulo kuti atonthoze komanso kulimbikitsa anthu amene akudwala mwauzimu (Onani ndime 13-14)
14. Mogwirizana ndi Agalatiya 6:1, kodi akulu amathandiza bwanji munthu akayamba kulowera “njira yolakwika”? (Onaninso zithunzi.)
14 Werengani Agalatiya 6:1. Mkhristu akayamba kulowera “njira yolakwika,” amakhala kuti sakutsatira mfundo zolungama za Mulungu. Njira yolakwikayi ingakhale kusankha zinthu molakwika kapena kuchita tchimo lalikulu. Chifukwa cha chikondi, akulu ‘amathandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.’ Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti ‘kuthandiza’ amafotokozanso za kubwezeretsa fupa limene lathyoka kuti munthu asalumale. Dokotala waluso amachita zimenezo m’njira yoti munthu asamve ululu kwambiri. Akulunso amathandiza munthu yemwe wayamba kulowera njira yolakwika mwanjira yoti asamve ululu kwambiri. Iwo amalangizidwanso kuti pochita zimenezi ayenera ‘kusamala, kuopera kuti nawonso angayesedwe.’ Amazindikira kuti nawonso si angwiro ndipo akhoza kulakwitsa zinthu. M’malo mokhala ndi mtima woweruza kapena kudziona kuti ndi olungama, iwo amayesetsa kukhala achifundo.—1 Pet. 3:8.
15. Kodi tizichita chiyani ngati tili ndi vuto linalake?
15 Tizidalira akulu mumpingo. Iwo anaphunzitsidwa kuti azisunga chinsinsi, azipereka malangizo pogwiritsa ntchito Baibulo komanso azitithandiza kupirira mavuto. (Miy. 11:13; Agal. 6:2) Akuluwa amakhala ndi makhalidwe komanso luso losiyanasiyana, koma tizimasuka ndi mkulu aliyense n’kukambirana naye vuto lathu. Koma si bwino kuti tikapempha malangizo kwa mkulu tizipitanso kwa mkulu wina kuti tikamve zotikomera. Tikamatero tidzakhala ngati anthu ongofuna kumva “zowakomera mʼkhutu,” osati ofuna ‘kuphunzitsidwa mfundo zolondola’ za m’Baibulo. (2 Tim. 4:3) Tikafotokozera mkulu za vuto lathu, angatifunse ngati talankhulanso ndi mkulu wina komanso malangizo amene watipatsa. Mkuluyo angasonyezenso kudzichepetsa pofunsa malangizo kwa mkulu wina.—Miy. 13:10.
UDINDO UMENE ALIYENSE ALI NAWO
16. Kodi aliyense ali ndi udindo wotani?
16 Akulu amatipatsa malangizo komanso kutithandiza tikakumana ndi mavuto, koma samatisankhira zochita. Ndi udindo wa aliyense kukhala moyo wodzipereka kwa Mulungu. Aliyense adzayankha yekha mlandu pa zimene amalankhula komanso kuchita. Ndipo Mulunguyo angatithandize kuti tikhalebe okhulupirika kwa iye. (Aroma 14:12) Choncho m’malo motiuza zoyenera kuchita, akulu amagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu potithandiza kudziwa maganizo ake. Potsatira malangizo awo a m’Baibulo, tingathe kuphunzitsa ‘luso lathu la kuganiza’ kuti tizisankha zochita mwanzeru.—Aheb. 5:14.
17. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?
17 Ndi mwayi wamtengo wapatali kukhala nkhosa za Yehova. Yehova anatumiza Yesu, yemwe ndi “m’busa wabwino,” kuti adzapereke dipo kuti tidzapeze moyo wosatha. (Yoh. 10:11) Yehova amagwiritsa ntchito akulu pokwaniritsa lonjezo lake lakuti: “Ndidzakupatsani abusa amene amachita zinthu zogwirizana ndi zofuna zanga ndipo adzakuthandizani kuti mudziwe zinthu zambiri ndiponso kuti mukhale omvetsa zinthu.” (Yer. 3:15) Tikafooka kapena kudwala mwauzimu, tisamazengereze kuitana akulu kuti atithandize. Choncho tiyeni titsimikize mtima kuti nthawi zonse tizilandira thandizo lochokera kwa Yehova kudzera mwa akulu mumpingo.
NYIMBO NA. 31 Muziyenda Ndi Mulungu
a Ngati papita nthawi ndipo munthu yemwe wachita tchimo sakukanena kwa akulu, mungasonyeze kuti ndinu wokhulupirika kwa Yehova popita kwa akuluwo kukawauza zomwe mukudziwa.