Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb23 September tsamba 7
  • Abusa Amene Amachitira Zabwino Anthu a Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Abusa Amene Amachitira Zabwino Anthu a Yehova
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Itanani Akulu’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Mmene Tingasonyezere Chikondi ndi Chifundo Wina Akachita Tchimo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukhale Mkulu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwb23 September tsamba 7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Abusa Amene Amachitira Zabwino Anthu a Yehova

Anthu ambiri amaona molakwika anthu amene ali ndi udindo. Chifukwa chiyani? Chifukwa kuyambira kalekale, anthu akhala akugwiritsa ntchito udindo pofuna kudzipindulitsa okha. (Mik 7:3) Koma timayamikira kwambiri kuti akulu amaphunzitsidwa kuti azigwiritsa ntchito udindo wawo pochitira zabwino anthu a Yehova.—Est 10:3; Mt 20:​25, 26.

Mosiyana ndi anthu audindo a m’dzikoli, akulu amagwira bwino ntchito yawo yoyang’anira chifukwa amakonda Yehova ndi anthu ake. (Yoh 21:16; 1Pe 5:​1-3) Motsogoleredwa ndi Yesu, abusawa amathandiza wofalitsa aliyense kuti azikhala womasuka mumpingo wa Chikhristu ndi kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Amakhala okonzeka kupereka thandizo lauzimu kwa nkhosa za Yehova, amathandiza wofalitsa akadwala mwadzidzidzi komanso amathandiza kukachitika ngozi zam’chilengedwe kapena zoyambitsidwa ndi anthu. Ngati mukufunikira thandizo, lankhulani ndi akulu a mumpingo mwanu ndipo adzakuthandizani.—Yak 5:14.

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Abusa Amene Amasamalira Gulu la Nkhosa.” Mkulu wakumbatira Elias mosangalala pamene akulonjerana.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ABUSA AMENE AMASAMALIRA GULU LA NKHOSA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi thandizo lomwe akulu anapereka kwa Mariana linamulimbikitsa bwanji?

  • Kodi thandizo lomwe akulu anapereka kwa Elias linamulimbikitsa bwanji?

  • Kodi zimene mwaona muvidiyoyi, zakhudza bwanji mmene mumaonera ntchito imene akulu amagwira?

Muzidziwitsa akulu . . .

  • mukasintha manambala a foni kapena mukasamuka

  • ngati mukukumana ndi mayesero

  • ngati mukuchoka ndipo mukakhala kwa nthawi yaitali musanabwerere

  • mukadwala matenda aakulu kapena mukagonekedwa m’chipatala

  • ngati mwachita tchimo lalikulu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena