“Dikirani”
1 Yesu atatha kufotokoza zochitika zapadera zimene zidzakhala zizindikiro za masiku otsiriza a dongosolo lino la zinthu, analimbikitsa ophunzira ake kukhala ‘odikira.’ (Marko 13:33) N’chifukwa chiyani Akristu ayenera kukhala odikira? Chifukwa chakuti tikukhala m’nthaŵi yoopsa zedi m’mbiri ya anthu. Sitikufuna kukhala ogona mwauzimu. Zimenezo zingatilepheretse kudziŵa ntchito imene Yehova watipatsa kuti tiichite m’nthaŵi ya mapeto ino. Kodi ntchito imeneyi n’njotani?
2 Yehova watuma anthu ake kulengeza m’dziko lonse uthenga wabwino wa Ufumu wake umene ndi chiyembekezo chokha cha mtundu wa anthu. Kugwira kwathu ntchito imeneyi pamodzi ndi gulu la Mulungu kumatidziŵikitsa monga Akristu oona, amene tikudziŵa nthaŵi ndiponso kufunika kothandiza ena kumva “mawu a moyo wosatha.” (Yoh. 6:68) Mwa kuchita nawo ntchito yofunika kwambiri imeneyi, timapereka umboni wakuti tili odikira mwauzimu.
3 Kusonkhezeredwa Kulalikira: Monga Mboni za Yehova, tiyenera kukhala ndi malingaliro oyenera a utumiki wathu. Kukonda Mulungu ndi anansi kuyenera kusonkhezera aliyense wa ife payekhapayekha kuchita nawo ntchito yolalikira. (1 Akor. 9:16, 17) Potero, tidzadzipulumutsa tokha komanso iwo akumva ife. (1 Tim. 4:16) Pakulalikira za Ufumu wa Mulungu womwe uli boma labwino koposa onse amene mtundu wa anthu wakhalapo nawo, tiyeni tikhale ofunitsitsa kulalikira nawo mokhazikika, kwa maola ambiri monga kulili kofunikira!
4 Ntchito yathu n’njoyenera changu chifukwa cha mfundo ina yofunikira, chisautso chachikulu chidzayamba ife tikuchitabe ntchito imeneyi. Kusadziŵa kwathu tsiku ndi nthaŵi kumafuna kuti tikhale odikira ndi okonzeka nthaŵi zonse, ndi kudalira Yehova m’pemphero. (Aef. 6:18) Ntchito yolalikira ikupitiriza kukula. Komabe tsiku lina posachedwapa, ntchito yaikulu yochitira umboni m’mbiri ya athu idzafika pakaindeinde.
5 Mverani mokhulupirika lamulo la Yesu la kukhala ‘odikira.’ Zimenezi zikufunika kwambiri makamaka tsopano lino. Tichitepotu kanthu mwachangu. Tiyeni tikhalebe ogalamuka mwauzimu, atcheru ndi achangu mu utumiki wa Yehova, lero ndi masiku onse. Inde, tiyeni “tidikire, ndipo tisaledzere.”—1 Ates. 5:6.