Kumbukirani Kubwererako!
1 “Koma ndiye zinali zokambirana zabwino bwanji! Kumenekuja n’dzakumbukire kudzachita ulendo wobwereza.” Kodi munayamba mwanenapo mawu ameneŵa ndipo kenako n’kuiwala kumene munthuyo amakhala? Ngati ndi choncho, mukudziŵa kuti njira yokha yokukumbutsani kubwererako ndiyo kulemba.
2 Lembani Zonse: Pamene mukukumbukira bwinobwino zimene mwakambirana ndi munthu amene wasonyeza chidwi, khalani ndi nthaŵi yoti mulembe mfundo zonse zoyenera zokhudza munthu amene munam’fikirayo. Lembani dzina la munthuyo ndi mmene mudzam’dziŵire. Lembaninso adiresi yake, musangolota. Funsaninso kuti mutsimikize kuti zimene mukulembazo n’zolondola. Lembani nkhani imene munakambirana, malemba alionse amene munaŵerenga, ndi buku limene munam’gaŵira.
3 Ngati mwam’siyira funso loti mudzakambirane ulendo wotsatirawo, lilembeni. Kodi mwadziŵa zinazake ponena za munthuyo, banja lake, kapena chipembedzo chake? Ngati ndi choncho, zilembeni zimenezi. Ndiyeno nthaŵi ina imene mudzam’fikire, kutchula zinthu zimenezi kudzasonyeza kuti muli ndi chidwi ndi munthuyo. Pomaliza, lembani tsiku ndi nthaŵi imene munam’fikira koyamba ndi tsiku limene mwanena kuti mudzapitakonso. Mwakulemba notsi zolondola, mudzakumbukira bwinobwino ndipo simungaiŵale kupitanso kumene mwalonjeza kuti mudzapita.—1 Tim. 1:12.
4 Mukatha kulembako, ikani zimene mwalembazo pamodzi ndi zinthu zanu za muutumiki wakumunda monga chikwama cha mabuku, Baibulo, buku la Kukambitsirana, ndi magazini kuti nthaŵi zonse zizikhala pafupi. Ndibwino kulemba nyumba imene simunapeze anthu pacholembapo cha kunyumba ndi nyumba chosiyana ndi chimene mumalembapo kofunika kubwererako. N’zoona, mosasamala kanthu za khama limene mungapange kuti mulembe zolondola, chofunika kwambiri n’kukumbukira kubwererako!
5 Lingalirani za Munthuyo: Pokonzekera utumiki, pendani notsi zamaulendo anu obwereza. Lingalirani za munthu aliyense payekha ndi zimene zingakhale zoyenera kukamba paulendo wobwereza. Ganizirani mmene mungakulitsire chidwi cha munthuyo kuti likhale phunziro la Baibulo lapanyumba. Kulinganiza zinthu koteroko kungawonjezere zipatso zanu komanso chimwemwe chanu monga mtumiki wa uthenga wabwino.—Miy. 21:5a.
6 Choncho nthaŵi ina mukadzapeza munthu womvetsera, musadzanene kuti mudzakumbukira munthuyo mosavuta. M’malo mwake, lembani, pendani notsi zanu, m’lingalirenibe munthuyo, ndiyeno kumbukirani kubwererako!