Zida Zimene Zimaphunzitsa, Kusonkhezera, ndi Kulimbikitsa
1 Ndi amphamvu pophunzitsa anthu za Baibulo ndi za Mboni za Yehova. Asonkhezera anthu ambiri kukhala olimba m’choonadi. Alimbitsa chikhulupiriro cha anthu odzipatulira a Mulungu ndi kuwathandiza kuyamikira kwambiri makonzedwe ake. Kodi ameneŵa ndani? Mavidiyo opangidwa ndi gulu la Yehova. Kodi munaonerapo mavidiyo 10 onse? Chiwaonereni papita nthaŵi yaitali motani? Kodi m’mawagwiritsa ntchito mu utumiki wanu? Pa msonkhano wachigawo analengeza kutulutsidwa kwa vidiyo ya nambala 11 yamutu wakuti, Our Whole Association of Brothers. Kodi mwaitanitsa vidiyoyi? Ndi motani mmene mungapindulire kwambiri ndi zida zabwino kwambirizi?
2 Nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1999 yakuti “Phunzirani Mawu A Mulungu Mokhazikika Monga Banja” inalimbikitsa ‘kupatula nthaŵi ina ya phunziro lanu kuti muonere mbali ina ya imodzi mwa mavidiyo ophunzitsa a Sosaite . . . ndiyeno n’kuzikambirana.’ Mogwirizana ndi langizo labwino limenelo, mwezi uliwonse pa Msonkhano wa Utumiki, tizikambirana vidiyo imodzi. Tikulimbikitsa aliyense mumpingo kuonera vidiyo kunyumba nthaŵi yodzakambirana za vidiyoyi pa Msonkhano wa Utumiki isanafike.
3 Mwezi uno tiyamba ndi vidiyo yoyambirira kutulutsidwa, ya Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name. Onerani vidiyoyi mwatcheru ndipo pezani mayankho a mafunso aŵa:
◼ Kodi Mboni za Yehova zimadziŵika kwambiri ndi chiyani?
◼ Kodi zinthu zonse zimene zimachitika pa Beteli n’zogwirizana ndi lemba liti?
◼ Kodi ndi chochitika chiti cha m’Baibulo chimene munaona anthu akuchiyerekezera, akuchijambula, ndiponso akuchipenta kuti achigwiritse ntchito m’zofalitsa?
◼ Kodi n’chiyani chimakuchititsani chidwi pa kapangidwe ka mabuku athu?
◼ Kuyambira mu chaka cha 1920 kudzafika mu 1990, kodi Sosaite inasindikiza mabuku angati?
◼ Mwa anthu a Mulungu kodi ndani kwenikweni ali oyenera kukalamira utumiki wa pa Beteli?—Miy. 20:29.
◼ Kodi banja la Beteli limasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri kwa Mboni za Yehova zonse m’njira ziti?
◼ Kodi n’chiyani chakusangalatsani pa ntchito za pa Beteli zothandiza kufikira anthu ambiri ndi uthenga wabwino mmene tingathere?
◼ Kodi ndalama zochirikiza ntchito ya padziko lonse zimachokera kuti?
◼ Ndi ntchito iti imene tingachirikize mwachangu, ndipo ndi mzimu wotani?—Yoh. 4:35; Mac. 1:8.
◼ Kodi mumaganiza chiyani ponena za gulu lodziŵika ndi dzina lathu?
◼ Kodi mungagwiritse ntchito bwanji vidiyo imeneyi mu utumiki?
Mu December tidzakambirana vidiyo yakuti The Bible—Accurate History, Reliable Prophecy.