Tonse Tilemekeze Yehova ndi Mwana Wake
Mmene Onse Opezeka pa Chikumbutso pa April 8 Angapindulire Kwambiri
1 Kodi ndani amene amapatsidwa ulemu wapadera lerolino? Ndi amene amachita zinthu zimene dzikoli limaona kuti n’zofunika kwambiri. Komabe, nthaŵi zambiri ntchito zawo sizichedwa kuiŵalika. Koma bwanji zinthu zimene zimapindulitsadi anthu onse? Zazikulu kuposa zimenezi tidzaziganizira mwapadera pa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye dzuŵa litaloŵa pa April 8, 2001.
2 Kodi ndani ali woyenera kulandira ulemu waukulu koposa? Baibulo limati: “Muyenera inu, Ambuye [“Yehova,” NW], . . . kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse.” (Chiv. 4:11) Monga Mlengi, Yehova ndiye Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. Kuyenera kwake ulemu sikudzatha! — 1 Tim. 1:17.
3 Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, anachita zinthu zofunika zimene zidzabweretsa madalitso osatha kwa anthu. Anatsanzira ndendende Atate ake. (Yoh. 5:19) Kumvera kwake kwangwiro ndiponso kutumikira kwake mokhulupirika kunam’pangitsa kukhala ‘woyenera kulandira chilimbikitso, ndi chuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi chiyamiko.’ (Chiv. 5:12) Atate wake anam’lemekeza mwa kumuika kukhala Mfumu. (Sal. 2:6-8) Ifeyo tidzakhala ndi mwayi wolemekeza Atate ndi Mwana yemwe pa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye pa April 8, 2001.
4 N’zachisoni kuti anthu ochepa okha m’mbiri ya anthu ndi amene alemekeza Yehova ndi Mwana wake mokwanira. Nthaŵi zina, ngakhale Aisrayeli, anthu a Mulungu akale, ankatumikira Yehova mwachiphamaso. Mwachionekere kumeneku kunali kupanda ulemu. (Mal. 1:6) Kupereka ulemu woyenera kumafuna kumvera mokhulupirika mosonkhezeredwa ndi chikondi ndiponso kuyamikira zonse zimene Yehova ndi Mwana wake atichitira. Ulemu woterowo umasonyeza kuti timawopa ndi kulemekeza Mulungu, ndiponso kuti timakumbukira Yehova ndi Yesu m’zochita zathu zonse. Mpingo wachikristu umayesetsa kuphunzitsa ndi kuthandiza ena kuchita zimenezi.
5 Nthaŵi Yapadera Yosonyeza Ulemu: Chaka chilichonse mwambo wa Chikumbutso ndiwo msonkhano wofunika kwambiri kwa anthu a Yehova. Aliyense wofuna kutumikira ndi kulemekeza Yehova ayenera kudzakhalapo. (Luka 22:19) Tikukhulupirira kuti kuwonjezera pa Mboni zachangu 6 miliyoni, anthu achidwi adzachulukitsa chiŵerengerochi mpaka kuposa 14 miliyoni. Ndi nthaŵi yabwino kwambiri yolemekeza Atate wathu wa Kumwamba! Ngakhale kuti mwambowu kwenikweni umakhudza Yesu, kulemekeza zimene anachita kumatamanda Atate, amene anam’tuma.—Yoh. 5:23.
6 Kodi tingatani kuti tichirikize nyengo yapaderayi? Tingathandize anthu oyamba kumene kusonyeza chidwi kupindula kwambiri. Alimbikitseni kuti adzakhalepo, ndipo ngati n’kofunika, athandizeni mokoma mtima kukafika kumaloko. Afotokozereni cholinga cha nkhani imene ikakambidwe kumeneko. Adziŵikitseni kwa ena. Zimene akaone ndi kumva kumeneko zingawasonkhezere kulemekeza nawo Yehova.
7 Musachepetse mphamvu ya pulogalamuyi. Wophunzira wina wa payunivesite ina anati: “Ndakhala ndikupezeka pa mgonero kambirimbiri ku tchalitchi kwathu, koma izi n’zina. Ndikuona kuti izi n’zimene Baibulo limanena, ndipo ndikukhulupirira kuti ndinu amene mumachita zoona.” Anayamba kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse ndipo mosakhalitsa anabatizidwa.
8 Thandizani Atsopano Kupita Patsogolo: Adziŵeni atsopano amene abwera pa Chikumbutso ndipo ayendereni pambuyo pake kuti mukakambirane zinthu zachilendo zimene anaphunzira ndiponso anaona kumeneku. Auzeni za misonkhano ina, imene ingawathandize kulidziŵa kwambiri Baibulo. Kupenda chaputala 17 cha buku la Chidziŵitso pamutu wakuti, “Pezani Chisungiko Pakati pa Anthu a Mulungu,” kudzawasonyeza zogaŵira zauzimu zosiyanasiyana za pampingo, zimene zikuwadikira.
9 N’kofunika kuti anthu achidwi aphunzire mmene angalemekezere Yehova paokha. Afotokozereni kuti Yehova amasangalala ndi pemphero lochokera pansi pamtima ndipo limatsitsimula mwauzimu nthaŵi zonse. (1 Yoh. 5:14) Mwa kugwiritsa ntchito phunziro 8 mpaka 12 m’bulosha la Mulungu Amafunanji, fotokozani makhalidwe amene amalemekeza Yehova. Mwa kukambirana za m’bulosha la Mboni za Yehova, masamba 30-1, limbikitsani atsopano kulingalira zolemekeza Yehova mwa kuchita nawo ntchito yolalikira.
10 Kuyamikira nsembe ya Yesu limodzi ndi mwayi wathu wotumikira monga ophunzira ake kumalemekeza Atate ndipo kumapindulitsa ena. Yesu analonjeza kuti: “Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzam’chitira ulemu.” —Yoh. 12:26.