Thandizani Ena Kupezeka Pamisonkhano
1 “Anansi onse apafupi . . . amene akufuna kubwera pamisonkhano tikuwalandira ndi manja aŵiri.” Kuyambira pamene magazini ya Zion’s Watch Tower ya November 1880 inalengeza zimenezi, Mboni za Yehova zakhala zikulimbikitsa anthu mwachangu kusonkhana pamodzi kuti alandire malangizo a Baibulo. (Chiv. 22:17) Iyi ndi mbali yofunika pa kulambira koona.
2 N’kofunika Kupezekapo: Pamene tisonkhana ndi mpingo timapindula. Timam’dziŵa bwino Yehova, Mulungu wathu wodabwitsayo. Mu mpingo, timasonkhana kuti ‘tiphunzitsidwe ndi Yehova.’ (Yes. 54:13) Gulu lake lili ndi pulogalamu yanthaŵi zonse ya malangizo a Baibulo imene imatithandiza kum’yandikira ndiponso kugwiritsa ntchito “uphungu wonse wa Mulungu.” (Mac. 20:27; Luka 12:42) Misonkhano imaphunzitsa aliyense luso lakuphunzitsa Mawu a Mulungu. Zikumbutso za m’Malemba zimatithandiza kukhala ndi unansi wabwino ndi ena komanso ndi Yehova weniweniyo. Kusonkhana ndi anthu okonda Mulungu kumalimbitsa chikhulupiriro chathu.—Aroma 1:11, 12.
3 Aitaneni Mwachindunji: Pa kuphunzira kwanu koyamba, pemphani wophunzira Baibulo aliyense kufika pamisonkhano. Kulitsani chidwi chake mwa kumuuza mfundo imene inakusangalatsani pamsonkhano wapitawo ndiponso mwa kupenda zina zimene zikakambidwa pamsonkhano ukudzawo. Fotokozani mmene Nyumba ya Ufumu imaonekera, ndipo onetsetsani kuti wamvetsa mmene angaidziŵire.
4 Ngati wophunzira sakuyambabe kufika pa misonkhano, pitirizanibe kum’pempha. Mlungu uliwonse khalani ndi nthaŵi yom’fotokozera mmene gulu lathu limayendera. Gwiritsani ntchito bulosha lakuti Zikuchita Chifuniro cha Mulungu ndiponso ngati n’kotheka muonetseni vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name kuti atidziŵe ndiponso adziŵe za misonkhano yathu. Pitani ndi ofalitsa ena kuti wophunzirayo adziŵane nawo. M’pemphero, thokozani Yehova chifukwa cha gululi ndipo tchulaninso kufunika kwakuti wophunzirayo azisonkhana nalo.
5 Musachite mphwayi kuthandiza anthu ongoyamba kumene kusonyeza chidwi kusonkhana nafe. Pamene akum’dziŵa bwino Yehova, adzasonkhezereka kugwiritsa ntchito zimene akuphunzira ndi kukhala m’gulu la Mulungu la anthu ogwirizana.—1 Akor. 14:25.