Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/97 tsamba 3-4
  • Kutsogoza Ophunzira ku Gulu la Dzina lathu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutsogoza Ophunzira ku Gulu la Dzina lathu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 8
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Thandizani Ena Kupezeka Pamisonkhano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Mmene Tingapangire ophunzira ndi Buku la Chidziŵitso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 4/97 tsamba 3-4

Kutsogoza Ophunzira ku Gulu la Dzina lathu

1 “Uthengawo ukulankhulidwa m’zinenero zoposa 200. Ndi uthenga umene ukumveka m’maiko oposa 210. Ndiwo uthenga umene ukuperekedwa ndi anthu mwachindunji kulikonse kumene kuli anthu. Uli mbali ya mkupiti wolalikira waukulu koposa umene dziko silinaonepo, uthenga umene ukugwirizanitsa anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi. Kwa zaka zoposa zana limodzi, Mboni za Yehova zalinganizidwa kuchita ntchito imeneyi!”

2 Imayamba motero nkhani ya vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name. Imayankha mafunso awa: Kodi Mboni za Yehova ndani kwenikweni? Kodi ntchito yawo njolinganizika motani? Imatsogozedwa motani? Nanga ndalama zake zimachokera kuti? Imasonyeza openyerera kuti “Mboni za Yehova padziko lonse zaphunzitsidwa monga gulu mmene zingathandizire anansi awo kukhulupirira Baibulo,” ndipo imawalimbikitsa kudzionera okha gulu la dzina lathu. Mkazi wina amene anali kuphunzira ataonerera vidiyo imeneyi, anagwetsa misozi yachimwemwe ndi chiyamiko nati: “Kodi ndani angalephere kuona kuti ili ndilo gulu la Mulungu woona, Yehova?”—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 14:24, 25.

3 Mkazi wina anaphunzira Baibulo apa ndi apo nthaŵi yaitali, koma sanavomereze kuti chiphunzitso cha Utatu nchonyenga. Kenako iyeyo ndi mwamuna wake anasonyezedwa vidiyo yathu. Anachita nayo chidwi kwambiri moti anaionerera kaŵiri usiku womwewo. Paphunziro lawo lotsatira, mkaziyo ananena kuti akufuna kukhala Mboni. Anatero kuti ankasumika kwambiri maganizo pa chikhulupiriro chake cha Utatu nalephera kupenda gulu lathu ndi anthu ake. Ataonerera vidiyo imeneyo, anazindikira kuti wapeza gulu loona la Mulungu. Nthaŵi yomweyo anafuna kuyamba kulalikira kunyumba ndi nyumba. Atamfotokozera zofunika kuti akhale wofalitsa wosabatizidwa, anati: “Ndiyamba tsopano lino.” Anachoka m’tchalitchi chake, nayamba ntchito ya utumiki wakumunda, ndipo anakhala waluso potsutsa Utatu.

4 Nzodziŵikiratu kuti ophunzira Baibulo amapita bwino patsogolo mwauzimu ndi kukula msinkhu mofulumira kwambiri pamene azindikira gulu la Yehova ndi kugwirizana nalo. Kuchirikiza mfundoyo, okwanira 3,000 atabatizidwa pa Pentekoste, “anali chikhalire m’chiphunzitso cha atumwi ndi m’chiyanjano.” (Mac. 2:42) Tifunika kuthandizanso ophunzira lerolino. Tingachite motani zimenezo?

5 Senzani Thayolo: Aliyense wopanga ophunzira ayenera kuzindikira kuti lili thayo lake kumtsogoza wophunzira Baibulo ku gulu la Mulungu. (1 Tim. 4:16) Phunziro lililonse liyenera kuonedwa monga njira yofikira patsiku lachimwemwe pamene watsopanoyo adzasonyeza kudzipatulira kwake kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi. Funso lina limene adzafunsidwa pankhani ya ubatizo nlakuti: “Kodi mukuzindikira kuti kudzipatulira kwanu ndi ubatizo zimakudziŵikitsani monga mmodzi wa Mboni za Yehova wogwirizana ndi gulu la Mulungu lotsogozedwa ndi mzimu?” Chifukwa chake, afunika kuzindikira kuti sangatumikire Mulungu popanda kugwirizana kwambiri ndi mpingo woona wachikristu.—Mat. 24:45-47; Yoh. 6:68; 2 Akor. 5:20.

6 Pitirizani kuphunzitsa wophunzirayo za mpingo wanu ndi gulu la padziko lonse la Mboni za Yehova. Chitani zimenezi paphunziro la Baibulo lililonse, kuchokera pa loyamba. Kuchokera pachiyambi, itanirani wophunzirayo ku misonkhano, ndipo pitirizani kumamuitanira.—Chiv. 22:17.

7 Gwiritsirani Ntchito Ziŵiya Zoperekedwa: Zofalitsa zathu zabwino koposa zogwiritsira ntchito pochititsa maphunziro a Baibulo a panyumba ndizo brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? ndi buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Zonse ziŵiri zimasonyeza kuti kugwirizana ndi mpingo nkofunika. Ndime yomaliza ya phunziro 5 m’brosha lakuti Mulungu Amafunanji imati: “Mufunikira kupitiriza kuphunzira za Yehova ndi kulabadira zofunika zake. Kupezeka pamisonkhano pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yakwanuko kudzakuthandizani kuchita zimenezo.” Buku la Chidziŵitso limalimbikitsa wophunzira mobwerezabwereza kuti azisonkhana. Mutu 5, ndime 22, umapereka pempho ili: “Mboni za Yehova . . . zikukusonkhezerani mwachikondi kugwirizana nazo pakulambira Mulungu ‘mumzimu ndi m’choonadi.’ (Yohane 4:24)” Mutu 12, ndime 16, umati: “Pamene mupitiriza ndi phunziro limeneli ndi kukhala ndi chizoloŵezi cha kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova, chikhulupiriro chanu chidzalimba kwambiri.” Mutu 16, ndime 20, umati: “Khalani ndi chizoloŵezi cha kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova.” Umawonjeza kuti: “Zimenezi zidzakuthandizani kumvetsa ndi kugwiritsira ntchito chidziŵitso chonena za Mulungu m’moyo wanu ndipo mudzakhala achimwemwe. Kukhala mmodzi wa gulu la abale achikristu la padziko lonse kudzakuthandizani kukhalabe pafupi ndi Yehova.” Mutu 17 umafotokoza bwinobwino mmene munthu angapezere chisungiko chenicheni pakati pa anthu a Mulungu. Pamene tiphunzira ndi ena, ndi thayo lathu kugogomezera zigawo zimenezo za mutuwo.

8 Brosha lakuti Mboni za Yehova—Zikuchita Chifuniro cha Mulungu Mogwirizana pa Dziko Lonse Lapansi ndilo chiŵiya chabwino chimene chatulutsidwa kuti chithandize anthu kulidziŵa bwino gulu lokha la Yehova looneka limene akuligwiritsira ntchito lerolino kuchita chifuniro chake. Chidziŵitso chatsatanetsatane chomwe lili nacho cha utumiki wathu, misonkhano, ndi kakonzedwe chidzalimbikitsa woŵerenga kuyanjana nafe polambira Mulungu. Titangokhazikitsa phunziro la Baibulo, kungakhale bwino kupatsa wophunzira kope la broshali kuti aziŵerenga yekha. Sitifunika kuliphunzira pamodzi naye monga momwe tinali kuchitira kale.

9 Ena a mavidiyo amene Sosaite yatulutsa alinso ziŵiya zabwino koposa zotsogozera ophunzira ku gulu la dzina lathu. Zingakhale bwino ngati angapenyerere (1) The New World Society in Action, yosonyeza filimu ya mu 1954 imene inaonetsa mzimu wachikondi, woyendetsa zinthu bwino, ndi mwataŵataŵa umene gulu la Yehova limagwira nawo ntchito; (2) United by Divine Teaching, imene imasonyeza umodzi wamtendere umene wasonyezedwa pamisonkhano yathu ya mitundu yonse ku Eastern Europe, South America, Afirika, ndi Asia; (3) To the Ends of the Earth, imene inasonyeza chaka cha 50 cha Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ndipo imasonyeza zimene amishonale achita pantchito ya dziko lonse yolalikira; (4) Jehovah’s Witnesses Stand Firm Against Nazi Assault, imene imasimba nkhani yochititsa chidwi ya kulimba mtima ndi kulakika kwa Mboni angakhale Hitler anawazunza mwankhanza; ndiponso osaiŵala (5) Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name.

10 Ikani Zonulirapo Zopita Patsogolo za Misonkhano: Ophunzira afunika kuwauza kuti tifunikira zonse ziŵiri phunziro lapambali limene timakhala nalo paphunziro la Baibulo la panyumba ndi makambitsirano a m’kalasi amene amakhalako kumisonkhano ya mpingo. (Yoh. 6:45) Watsopano ayeneranso kupita patsogolo pakudziŵa kwake zonse ziŵiri Malemba ndi gulu. Kuti zimenezo zitheke, sangachitire mwina kusiyapo kupezeka pamisonkhano. (Aheb. 10:23-25) Yambani kuitanira munthuyo ku misonkhano ya mpingo nthaŵi yomweyo. Ena atsopano amayamba kupezeka pamisonkhano ngakhale asanayambe phunziro lawo la Baibulo la panyumba lanthaŵi zonse. Inde, tiyenera kupereka chitsanzo chabwino ife eni mwa kupezekapo nthaŵi zonse.—Luka 6:40; Afil. 3:17.

11 Muuzeni zokwanira ponena za misonkhano ndi mmene imachitikira kuti wophunzirayo akhale womasuka atapezeka pamsonkhano nthaŵi yoyamba. Popeza anthu ena samamasuka thupi akapita kumalo atsopano nthaŵi yoyamba, kungakhale bwino kupitira limodzi naye wophunzirayo ku Nyumba ya Ufumu ngati ndiyo nthaŵi yoyamba kupezekapo. Adzamasuka kwambiri ngati muli naye pamene aonana ndi ena a mumpingomo. Chonde, mcherezeni bwino mlendo wanuyo, kummasula ndi kummvetsa bwino.—Mat. 7:12; Afil. 2:1-4.

12 Mlimbikitseni wophunzirayo kupezekapo patsiku la msonkhano wapadera, msonkhano wadera, kapena wachigawo mpata utangopezeka. Mwina mungamphatikizepo pamakonzedwe anu akayendedwe.

13 Kulitsani Mtima Woyamikira: Buku lakuti Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, patsamba 92, limati: “Ngati kuyamikira kwanu kwakukulu gulu la Yehova kusonyezedwa m’makambitsirano anu ndi anthu okondwerera, kudzakhala kwapafupi kwambiri kwa iwo kukula m’kuyamikira ndipo kudzawasonkhezera kupanga kupita patsogolo kokulirapo m’kufika pakudziŵa Yehova.” Nthaŵi zonse lankhulani zabwino ponena za mpingo wanu, osati zoipa ayi. (Sal. 84:10; 133:1, 3b) M’mapemphero amene mumapereka paphunziro la Baibulo, tchulanimo mpingo ndi kufunika kwakuti wophunzirayo azigwirizana nawo nthaŵi zonse.—Aef. 1:15-17.

14 Inde, tikufunitsitsa kuti atsopano akhale ndi mtima woyamikira unansi wosangalatsa ndi chisungiko chauzimu chopezeka mwa anthu a Mulungu. (1 Tim. 3:15; 1 Pet. 2:17; 5:9) Monga Mboni za Yehova, tiyeni tichite zonse zotheka kuti titsogoze ophunzira Mawu a Mulungu ku gulu la dzina lathu.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Ophunzira amapita patsogolo mofulumira kwambiri mwauzimu pamene adzionera okha gulu

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Musachedwe kuitanira wophunzira ku misonkhano

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena