Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/05 tsamba 1
  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 8

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 8
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Kutsogoza Ophunzira ku Gulu la Dzina lathu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Gulu Lowoneka la Mulungu
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Thandizani Ena Kupezeka Pamisonkhano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Azipezeka Pamisonkhano
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 5/05 tsamba 1

Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo​—Gawo 8

Kutsogolera Ophunzira ku Gulu

1. N’chifukwa chiyani kuli kothandiza kukambirana mfundo imodzi yokhudza gulu la Yehova mlungu uliwonse paphunziro la Baibulo?

1 Tikamachititsa maphunziro a Baibulo, cholinga chathu sikungophunzitsa nkhani zokhudza ziphunzitso zokha, koma timafunanso kuthandiza ophunzira kulowa mpingo wachikristu. (Zek. 8:23) Bulosha lakuti Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani? lingatithandize kuchita zimenezi. Apatseni buloshali ophunzira Baibulo atsopano ndi kuwalimbikitsa kuti aliwerenge. Kuwonjezera pamenepo, muzipatula mphindi zingapo mlungu uliwonse paphunziro lanu kukambirana nawo mfundo imodzi yokhudza gulu la Yehova.

2. Kodi mungawalimbikitse bwanji ophunzira Baibulo kuti azipezeka pa misonkhano ya mpingo?

2 Misonkhano ya Mpingo: Njira yofunika kwambiri imene ophunzira Baibulo angayamikirire gulu la Mulungu ndiyo mwa kusonkhana nafe pa misonkhano ya mpingo. (1 Akor. 14:24, 25) Choncho, mukhoza kuyamba kuwadziwitsa za misonkhano isanu imene timakhala nayo mlungu uliwonse powafotokozera msonkhano umodzi ndi umodzi. Tchulani mutu wa nkhani ya onse ya mlungu umenewo. Aonetseni nkhani imene mukaphunzire pa Msonkhano wa Nsanja ya Olonda ndiponso pa Phunziro la Buku la Mpingo. Fotokozani za Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi Msonkhano wa Utumiki. Mukakhala ndi nkhani mu sukulu, mwina mukhoza kuyesezera nawo limodzi. Auzeni mfundo zabwinozabwino zimene zinakambidwa pa misonkhano. Aonetseni zithunzi za m’mabuku athu kuti muwathandize kuona m’maganizo mwawo zimene zimachitika pa misonkhano. Paphunziro loyambirira lenileni, apempheni kuti abwere ku misonkhano.

3. Kodi ndi zinthu ziti zokhudza gulu zimene tingafotokoze?

3 Nthawi ya Chikumbutso, misonkhano ikuluikulu, ndiponso ya woyang’anira dera ikamayandikira, muzipatula mphindi zingapo kuti muwafotokozere ndi kuwathandiza kuchita chidwi kwambiri ndi misonkhano imeneyi. Ulendo uliwonse muziyankha limodzi la mafunso ngati awa: N’chifukwa chiyani timatchedwa Mboni za Yehova? N’chifukwa chiyani malo athu osonkhanira timawatcha Nyumba za Ufumu? Kodi ntchito za akulu ndi atumiki otumikira n’zotani? Kodi ntchito yolalikira ndi magawo ake dongosolo lake amalikonza bwanji? Kodi mabuku athu amapangidwa bwanji? Kodi ndalama zoyendetsera gulu lathu zimachokera kuti? Kodi ofesi ya nthambi ndi Bungwe Lolamulira zili ndi magawo anji oyang’anira ntchito yolalikira?

4, 5. Kodi mavidiyo athu angalimbikitse bwanji ena kuyamikira gulu?

4 Mavidiyo Othandiza: Njira ina imene ophunzira Baibulo angaonere kuti gulu la Yehova n’labwino kwambiri ndi mwa kugwiritsa ntchito mavidiyo athu. Vidiyo yakuti To the Ends of the Earth imasonyeza ntchito yolalikira ya padziko lonse; Our Whole Association of Brothers imasonyeza ubale wathu wa padziko lonse; ndi yakuti United by Divine Teaching imasonyeza mmene Mboni za Yehova zilili zogwirizana. Mayi wina amene wakhala akulandira magazini ndi mabuku athu kwa zaka zisanu anafika pogwetsa misozi ataonera vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name. Mayiyu anali kukhulupirira Mboni zimene zimapita kukam’chezera, koma atangoonera vidiyoyi, anaona kuti ayeneranso kukhulupirira gulu. Phunziro linayambika ndi mayiyo, ndipo mlungu wotsatira, anakapezeka pa misonkhano ku Nyumba ya Ufumu.

5 Mwa kupatula mphindi zingapo ndi ophunzira athu mlungu uliwonse ndiponso kugwiritsa ntchito zipangizo zimene tili nazo, tikhoza pang’ono ndi pang’ono kutsogolera ophunzira Baibulo ku gulu limodzi lokha limene Yehova akuligwiritsa ntchito masiku ano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena