Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb22 January tsamba 9
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Azipezeka Pamisonkhano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Azipezeka Pamisonkhano
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakuthandizeni Bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Akhale pa Ubwenzi ndi Yehova
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Asamacheze ndi Anthu Olakwika
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Asiye Makhalidwe Oipa
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22 January tsamba 9

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Azipezeka Pamisonkhano

Misonkhano yampingo ndi mbali yofunika kwambiri pakulambira koona. (Sl 22:22) Anthu onse amene amasonkhana kuti alambire Yehova, amasangalala komanso amadalitsidwa. (Sl 65:4) Nthawi zambiri ophunzira Baibulo amapita patsogolo mwamsanga ngati akufika pamisonkhano mokhazikika.

Kodi mungathandize bwanji anthu amene mukuphunzira nawo Baibulo kuti azipezeka pamisonkhano? Muziwaitanira kumisonkhano nthawi zonse. Muziwaonetsa vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? Muziwafotokozera kufunika kwa misonkhano. (lff phunziro 10) Mukhoza kuwafotokozera mfundo inayake imene mwaphunzira pamisonkhano kapena zimene mudzaphunzire pamisonkhano yotsatira. Muziwapatsa zinthu zimene zikagwiritsidwe ntchito kumisonkhano. Komanso muziwathandiza, mwina pa nkhani ya mayendedwe. Mukamayesetsa kuitanira ophunzira anu kumisonkhano, mudzasangalala kwambiri akadzayamba kupezekapo.​—1Ak 14:24, 25.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZITHANDIZA AMENE MUKUPHUNZIRA NAWO BAIBULO KUTI AZIPEZEKA PAMISONKHANO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza Amene Mukuphunzira Nawo Baibulo Kuti Azipezeka Pamisonkhano.” Anita akuitanira Jane ku misonkhano ya mpingo.

    Kodi Anita anagwiritsa ntchito mwayi uti kuti aitanire Jane kumisonkhano ya mpingo?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza Amene Mukuphunzira Nawo Baibulo Kuti Azipezeka Pamisonkhano.” Anita akumwetulira ndipo Jane wakhala pambali pake pamsonkhano wa mpingo.

    N’chifukwa chiyani timasangalala kwambiri wophunzira Baibulo akafika pamisonkhano?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza Amene Mukuphunzira Nawo Baibulo Kuti Azipezeka Pamisonkhano.” Alongo akupereka moni mwansangala kwa Jane pambuyo pa misonkhano.

    “Mulungu ali pakati panu”

    Kodi Jane anamva bwanji atafika kumisonkhano koyamba?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena