Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb22 March tsamba 15
  • Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Akhale pa Ubwenzi ndi Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Akhale pa Ubwenzi ndi Yehova
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Asiye Makhalidwe Oipa
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Azidzidyetsa Mwauzimu
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri Mu Utumiki​—Muzifunsa Mafunso
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Muziwafika Pamtima
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22 March tsamba 15

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Akhale pa Ubwenzi ndi Yehova

Yehova amafuna kuti tizimutumikira chifukwa choti timamukonda. (Mt 22:37, 38) Kukonda Mulungu n’kumene kungathandize ophunzira Baibulo kuti asinthe komanso akhalebe olimba akamakumana ndi mayesero. (1Yo 5:3) Ndiponso kukonda Mulungu ndi komwe kumawathandiza kuti abatizidwe.

Muziwathandiza ophunzira anu kuti aziona kuti Mulungu amawakonda. Muziwafunsa mafunso monga: “Kodi zimenezi zikukuphunzitsani chiyani zokhudza Yehova?” kapena “Kodi zimenezi zikusonyeza bwanji kuti Yehova amakukondani?” Muziwathandiza kuti aziona mmene Yehova akuwathandizira paokha. (2Mb 16:9) Muziwafotokozera zitsanzo za mmene Yehova wakhala akuyankhira mapemphero anu, ndipo muziwalimbikitsa kuti aziona mmene akuyankhira mapemphero awo. Timasangalala kwambiri tikaona ophunzira Baibulo athu akukondedwa ndi Yehova, iwonso n’kumamukonda ndiponso kumayesetsa kuti akhale naye pa ubwenzi wolimba.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZITHANDIZA AMENE MUKUPHUNZIRA NAWO BAIBULO KUTI AKHALE PA UBWENZI NDI YEHOVA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza Amene Mukuphunzira Nawo Baibulo Kuti Akhale pa Ubwenzi ndi Yehova.” Jane akuoneka wankhawa pamene akulankhula pa foni.

    Kodi Jane anakumana ndi vuto liti?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza Amene Mukuphunzira Nawo Baibulo Kuti Akhale pa Ubwenzi ndi Yehova.” Anita akulankhulana ndi Jane.

    Kodi Anita anathandiza bwanji Jane?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzithandiza Amene Mukuphunzira Nawo Baibulo Kuti Akhale pa Ubwenzi ndi Yehova.” Jane akuganizira mmene Yehova wamuthandizira.

    Kodi Jane anakwanitsa bwanji kuthana ndi vutolo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena