KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri mu Utumiki—Muzifunsa Mafunso
Yehova, yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe,” amafuna kuti tizisangalala tikakhala mu utumiki. (1Ti 1:11) Timasangalala kwambiri tikamayesetsa kuwonjezera luso lathu lophunzitsa. Kufunsa mafunso kumachititsa kuti munthu akhale ndi chidwi komanso ndi njira yabwino yoyambira kucheza. Mafunso amathandizanso anthu kuganiza. (Mt 22:41-45) Tikafunsa munthu funso, n’kumamumvetsera pamene akuyankha, timakhala tikumuuza kuti ‘Ndinu ofunika kwa ine.’ (Yak 1:19) Zimene munthuyo wayankha zingatithandize kudziwa zoyenera kulankhula.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIWONJEZERA LUSO LANU KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA—MUZIFUNSA MAFUNSO NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi ndi makhalidwe abwino ati amene Jane anasonyeza?
Kodi Anita anagwiritsa ntchito bwanji mafunso posonyeza kuti akuchita chidwi ndi Jane?
Kodi Anita anagwiritsa ntchito bwanji mafunso pothandiza Jane kuti achite chidwi ndi uthenga wabwino?
Kodi Anita anagwiritsa ntchito bwanji mafunso pothandiza Jane kuganiza?