KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI
Muzilola Kuti Yehova Azikuthandizani Kudzera M’pemphero
Yehova ndi amene amachititsa kuti mbewu ya choonadi imere komanso ikule mumtima mwa munthu. (1Ak 3:6-9) Choncho kuti zinthu zizitiyendera bwino mu utumiki, tiyenera kudalira Yehova kuti azitithandiza komanso kuti azithandiza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo.
Muzipempha Yehova kuti azithandiza ophunzira anu kupirira mavuto komanso kulimbana ndi mayesero. (Afi 1:9, 10) Muzitchula zimenezi mwachindunji. Muzipemphera kuti mzimu woyera uzitsogolera maganizo komanso zochita zanu. (Lu 11:13) Muziphunzitsa ophunzira anu kupemphera ndipo muziwalimbikitsa kuti azitero. Muziwapempherera ophunzira anu komanso muzipemphera nawo limodzi ndipo muzitchula dzina lawo.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIGWIRITSA NTCHITO ZOMWE YEHOVA WATIPATSA KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA—PEMPHERO, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi Anita anakumana ndi vuto lotani pamene ankaphunzira ndi Jane?
Kodi lemba la 1 Akorinto 3:6 linamuthandiza bwanji Anita?
Kodi vuto lomwe Anita anakumana nalo linatha bwanji?